Kugwira Ntchito—Zolimba Kodi Zotulukapo Zake Nzotani?
Yolembedwa ndi mtolankhani wa Galamukani! ku Japan
“‘ZAKUMWA zopereka mphamvu’ zakhala zotchuka kwambiri, zokhala m’mitundumitundu yoposa 200 ndipo malonda ake amapeza 900 miliyoni yen pachaka,” ikusimba motero Mainichi Daily News, nyuzipepala ya ku Japan yotchuka. Kutchuka kwa zinthu zimenezi, zimene amati zimapatsa nyonga mwamsanga kwa antchito otopa, “kukuchitira umboni chisonkhezero cha anthu a ku Japan chakugwira ntchito mosasamala kanthu za kupsinjika maganizo, kusoŵa tulo ndi mphepo yotentha m’chilimwe,” linapitiriza motero lipotilo.
Kumbali ina ya Pacific, “pafupifupi mmodzi mwa asanu ndi atatu a nzika za Amereka anasimbidwa kukhala akugwira ntchito maola 60 kapena owonjezereka pamlungu,” malinga nkunena kwa United States Bureau of Labor Statistics. Mamanijala aang’ono amawona kukhala kofunika kuthera nthaŵi yawo yambiri ndi nyonga pantchito kwakuti nthaŵi zina ntchito yawoyo imakhala yolamulira miyoyo yawo.
Pafupifupi mumtundu uliwonse, anthu amene ali akhama pantchito, ozindikira, ndi ogwira ntchito zolimba amatamandidwa kuti ndi anthu abwino. Ngakhale wolemba Baibulo wakale anati: “Kodi sichabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.” (Mlaliki 2:24) Kwakukulukulu, anthu kulikonse amakhulupirirabe mapindu otero. Kaya amalingalira ntchito kukhala yabwino kapena ayi, anthu ochuluka amagwira ntchito kuyambira mmamaŵa mpaka usiku, kuyambira pamasiku asanu, asanu ndi limodzi, kapena asanu ndi aŵiri pamlungu.
Komabe, kodi kugwira ntchito zolimba konseku kwaphulanji? M’maiko onga Japan ndi Germany, “mikhalidwe yozizwitsa” m’zachuma imene yatheka chiyambire kutha kwa Nkhondo Yadziko II ikukhumbiridwa kwambiri ndi maiko osatukuka. Maiko onse aŵiriwo anatukuka pambuyo pa kugonjetsedwa nakhala amphamvu m’zachuma kwakuti dziko lonse lazindikira zimenezo. Komabe, kodi kudzipereka pantchito kwachitanji kwa anthu ambiri?
Ngakhale kuti mkhalidwe wa moyo ku Japan watukuka kwambiri, Mainichi Daily News ikusimba kuti, anthu a ku Japan ochuluka “samakhala ndi lingaliro lenileni la kukhuphuka m’miyoyo yawo yatsiku ndi tsiku.” Choipa kwambiri nchakuti, m’kulondola kwawo wotchedwa kuti moyo wabwino kodziphako, ambiri afikira pakudwala kapena ngakhale pakufa chifukwa cha kugwira ntchito mopambanitsa ndi kupsinjika maganizo. Mofananamo, m’kupenda kwina kochitidwa ku United States, chigawo chimodzi mwa zitatu za mamanijala zikwi zitatu cha amene anafunsidwa ananena kuti amagwira ntchito zolimba, anathedwa mphamvu, ndipo sanakondweretsedwe ndi ntchito yawo.
Nawonso akazi ogwira ntchito akusonyeza zizindikiro za kuvutika. Kupenda kochitidwa ku Italy kunasonyeza kuti akazi ogwira ntchito m’dziko limenelo amagwira ntchito kwa maola 30 pa avareji kuposa anzawo a muukwati mlungu uliwonse. Kuwonjezera pakuthera maola ambiri mu ofesi kapena m’fakitale, ayenera kugwira ntchito za panyumba pamene abwerera kunyumba. Mkazi wina m’magazini otchedwa kuti Europeo anati: “Kucheza kwanga ndi ena kwatheratu. Ndilibe nthaŵi. Sindingathe kupitirizabe ndi mkhalidwe umenewu.”
Bwanji za moyo wa banja? “M’kufunafuna loto la kukhala ndi chuma la ku Amereka, tikudzigulitsa ndi banja lathu kuti tipeze ndalama ndi mphamvu,” akutero Herbert Freudenberger, katswiri wa ku New York wodziŵa za anthu antchito othedwa mphamvu. Monga chotukukapo cha kudziloŵetsa kwambiri muntchito kwa amuna awo, akazi ena a anthu a mabizinesi a ku Britain amene amagwira ntchito kumaiko ena anasimbidwa kukhala osukidwa ndi osakondwa. Komatu sali okha pankhaniyi.
Talingalirani za zotulukapo za moyo wa banja ku Japan, kumene ogwira ntchito za mu ofesi a zaka zapakatikati osafika patheka amafika kunyumba 8 koloko yausiku isanakwane. Akazi ena samalingaliranso amuna awo kukhala anzawo a muukwati enieni; samafuna kukhala nawo pafupi mowonjezereka kuposa momwe amachitira. Uthenga wa malonda pawailesi ya kanema umanena mwachidule ponena za kugwiritsidwa mwala kwa akaziwo, kuti: “Amuna amamva bwino ndipo samakhala panyumba.”
Monga momwe taoneramo, kuli kwachiwonekere kuti kugwira ntchito zolimba kuli ndi mbali yake yabwino ndi yoipa. Ngati kuchitidwa monkitsa, kungadzetse mavuto. Chotero kodi ndimotani mmene kugwira ntchito zolimba kungakhalire osati mtolo, koma chinthu china chabwinodi ndi magwero a chimwemwe?
Kumbali ina, kodi kuika patsogolo ntchito ya munthu kuposa kanthu kena kalikonse kapena kupitirizabe kumangogwira ntchito nkowopsa motani? Tiyeni tionetsetse mbali zimenezi za kugwira ntchito zolimba kwa munthu.