Anapulumuka Zauchigawenga ku Mumbai
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU INDIA
MZINDA wa Mumbai, womwe kale unkatchedwa Bombay, uli ndi anthu oposa 18 miliyoni ndipo chiwerengerochi chikukulirakulira. Mwina anthu 6 miliyoni kapena 7 miliyoni a mumzindawu amakwera sitima zothamanga zedi popita ndi pobwera ku ntchito, kusukulu, pokagula zinthu, kapenanso popita ndi pobwera ku malo kochitikira zosangalatsa. Anthu ofuna kukwera sitimazi akachuluka kwambiri, makamaka panthawi yopita ndi kuweruka ku ntchito, sitima ya mabogi 9 yomwe imayenera kunyamula anthu 1,710, imatha kunyamula anthu pafupifupi 5,000. Inali nthawi ngati imeneyi pamene zigawenga zinaphulitsa sitima zingapo za mumzindawu pa July 11, 2006. Munthawi yosakwana mphindi 15, mabomba seveni anaphulitsa sitima zingapo za kampani ya Western Railway, ndipo anthu oposa 200 anafa komanso ena oposa 800 anavulala.
Anthu ochuluka ndithu a m’mipingo 22 ya Mboni za Yehova ya mumzinda wa Mumbai, amakwera sitima zimenezi nthawi zonse, ndipo ena mwa iwo anali m’sitimazi panthawi imene zauchigawengazi zinachitika. Ndi mwayitu kuti palibe wa Mboni amene anafa, koma angapo anavulala. Tsiku limenelo, Anita ankapita ku nyumba ataweruka ku ntchito. Iye anakwera m’bogi labwino kwambiri la sitima inayake, imene inali itadzaza kwambiri. Motero anangoima pafupi ndi pakhomo n’cholinga choti asavutike potsika. Ulendo uli mkati, mwadzidzidzi panamveka chiphokoso chachikulu cha chinthu chophulika, ndipo m’bogi lonselo munadzaza utsi wakuda bii. Pamene Anita anasuzumira pakhomo kuti aone kunja, anangoona bogi loyandikana ndi limene iyeyo anakwera litang’ambikiratu ndipo linapendekeka kwambiri. Iye anangoti kakasi ataona mitembo ndiponso zidutswa za mitembo zikugwera m’njanji. Patangodutsa timphindi tingapo, timene Anitayo anationa ngati zaka zambiri, sitimayo inaima. Iye pamodzi ndi anthu ena amene anali m’sitimayo anatuluka n’kuthawira chapatali. Kenaka, Anita anaimbira foni mwamuna wake John, ndipo mwamwayi anakwanitsa kulankhulana ngakhale kuti mafoni ankavuta chifukwa cha anthu ambirimbiri okhudzidwa ndi ngoziyi amene ankayesa kuimba foni. Komatu Anita anayesetsa kuugwira mtima mpaka pamene analankhula ndi mwamuna wake. Kenaka, analephera kupirira moti anayamba kulira. Atam’fotokozera mwamuna wakeyo zimene zinachitika, anamuuza kuti adzamutenge. Ndiye akudikira mwamuna wakeyo, chimvula chinayamba kugwa ndipo chinakokolola zinthu pamalo a ngoziwo zomwe zikanathandiza anthu ofufuza zangoziyo.
Claudius, yemwenso ndi wa Mboni anaweruka ku ntchito mofulumirirapo pa tsikuli. Ndiyeno anakwera sitima, m’bogi labwino kwambiri pasiteshoni yaikulu yotchedwa Churchgate. Sitimayi imanyamuka eyitini pasiti faifi madzulo tsiku lililonse, ndipo ulendo wa Claudius unali wokatsikira pa siteshoni ya Bhayandar, ndipo ndi ulendo wa ola limodzi. Iye akuyang’anayang’ana poti akhale m’sitimamo, anaona Joseph, yemwenso ndi wa Mboni za Yehova ndipo amasonkhana mu mpingo woyandikana ndi umene Claudius alimo. Nthawi inadutsa mofulumira chifukwa cha macheza awowo. Kenaka, Joseph anayamba kuwodzera chifukwa cha kutopa ndi ntchito. Popeza anthu anathinana kwambiri m’bogili, sitimayo itaima pa siteshoni ina, Claudius ananyamuka pa mpando kuti atsike ngakhale kuti anali asanafike kumene anali kupita. Ataimirira pafupi ndi mpando womwe anakhalawo, Joseph anauka kuti atsanzikane ndi mnzakeyo. Ndiyeno Claudius anasuntha n’kugwira chitsulo cha m’mbali mwa mpando kuti alankhulane bwino. Zimenezitu mwina n’zimene zinapulumutsa moyo wa Claudius. Mwadzidzidzi, kunamveka chiphokoso chosaneneka. Bogi lonselo linagwedezeka mochititsa mantha, mkati monse munadzadza utsi wokhawokha, ndiponso munali chimdima cha ndiweyani. Claudius anagwera pansi pakatikati pamipando, ndipo chiphokoso chogonthetsa m’khutu cha kuphulikako chinam’chititsa kuti azingomva ngati kuti timabelu tikulira m’makutu mwake. Pamalo pamene iyeyu anaima poyamba m’bogimo panaphwasukiratu moti njanji imachita kuonekera. Anthu onse amene anali pamalowo anagwera pansi n’kuferatu ndipo ena anagwera m’njanji. Ndi mwayi kuti Claudius anapulumuka. Limenelitu linali bomba lachisanu mwa mabomba seveni amene anaphulitsidwa m’sitima patsikuli, lomwe linali Lachiwiri.
Claudius anapititsidwa ku chipatala zovala zake zonse zili magazi okhaokha. Sikuti magaziwa onsewa anali ake, koma ambiri anali a anthu ena amene anavulala kwambiri kapena kufa kumene. Iye anangovulala pang’ono m’khutu, padzanja, ndiponso anawauka tsitsi. Ali ku chipatalako, anakumana ndi Joseph komanso mkazi wake Angela, amenenso anakwera sitima yomweyo koma m’bogi lina la akazi ndipo sanavulale. Koma Joseph anavulala pang’ono pa diso ndiponso anagontha m’khutu. Anthu atatu a Mboniwa anathokoza kwambiri Yehova chifukwa choti anapulumuka ngoziyi. Claudius ananena kuti mfundo yomwe aziyendera akangochira ndiyoti: ‘N’kupusa ndiponso kupanda nzeru kuyesa kufunafuna ndalama zochuluka ndiponso chuma chambirimbiri m’dongosolo lino limene munthu angathe kufa mwadzidzidzi m’kamphindi kamodzi.’ Ndipotu iye n’ngokondwa chifukwa ali paubwenzi wabwino ndi Yehova, womwe ndi chinthu chofunika kwambiri pamoyo wake.
M’nyengo yaifupi kwambiri, mumzinda wa Mumbai mwachitika zinthu zoopsa monga kusefukira kwa madzi, ziwawa, ndiponso kuphulitsidwa kwa mabomba. Ngakhale zinthu zili choncho, Mboni za kumeneko zoposa 1,700 zimakonda kwambiri choonadi ndiponso n’zolimbikira. Zimalalikira kwa anansi awo za chiyembekezo chabwino kwambiri cha dziko latsopano, limene simudzakhalanso chiwawa.—Chivumbulutso 21:1-4.
[Mawu Otsindika patsamba 23]
Pamalo pamene iyeyu anaima poyamba m’bogimo panaphwasukiratu moti njanji imachita kuonekera
[Chithunzi patsamba 23]
Anita
[Chithunzi patsamba 23]
Claudius
[Chithunzi patsamba 23]
Joseph ndi Angela
[Mawu a Chithunzi patsamba 22]
Sebastian D’Souza/AFP/Getty Images