Kodi Nyenyezi Imene Inatsogolera “Anzeru a Kum’mawa” Inali Yotani?
Nkhani zambiri zokhudza Khirisimasi zimasonyeza kuti nyenyezi imeneyi inatumizidwa ndi Mulungu. Koma kodi zimenezi ndi zoona?
◼ Mateyo, amene analemba nawo Baibulo, anafotokoza kuti nyenyeziyi inali yodabwitsa ndipo n’chifukwa chake “anzeru a kum’mawa” anachita nayo chidwi. Iwo anaitsatira mpaka kukafika kumene Yesu anali. (Mateyo 2:1-12) Nkhani zambiri zokhudza Khirisimasi zimasonyeza kuti nyenyezi imeneyi inatumizidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, buku lina limanena kuti nyenyeziyi “inatumizidwa ndi Mulungu n’cholinga choti . . . Yesu alemekezedwe ndi Atate ake monga Mwana wake wokondedwa.” Ndipo nyimbo zambiri za Khirisimasi zimatamanda nyenyeziyi. Koma kodi imeneyi inalidi nyenyezi?
Akatswiri ena amanena kuti siinali nyenyezi yeniyeni koma kunali kuwala kochokera ku mapulaneti awiri amene anakumana. Koma buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo limanena kuti “ngati zimenezi zikanakhala zoona, ndiye kuti kuwalaku si bwenzi kukutchedwa ‘nyenyezi.’” (The New Bible Dictionary) Mapulaneti atayandikana angaonekebe kuti ndi mapulaneti angapo osati nyenyezi imodzi. Anthu enanso amanena kuti “nyenyezi” imeneyi inali chimodzi mwa zinthu zakuthambo zimene zimawala kwambiri. Koma, n’zosatheka kuti zinthu zimenezi ziziyenda m’mlengalenga mpaka kuwalondolera “anzeru a kum’mawa” mumzinda komanso pa nyumba yeniyeni imene amafuna.
Kodi nyenyezi imeneyi inali kuwala chabe kwa zinthu zakuthambo, kapena inatumizidwa ndi Mulungu? Taganizirani mfundo izi: “Anzeru a kum’mawa” sanali anthu amene masiku ano tinganene kuti ndi ophunzira ndiponso sanali mafumu. Malinga ndi omasulira Baibulo ambiri, iwo anali “okhulupirira nyenyezi.” Ndipo ankachita zinthu zimene zinali zotsutsana ndi Malemba Opatulika. (Deuteronomo 18:10-12) Onani kuti palibe munthu wina kupatulapo okhulupirira nyenyeziwa amene “anaona” nyenyeziyo. Ngati nyenyeziyo ikanakhala yeniyeni, anthu ambiri akanaiona. Koma ngakhale Mfumu Herode anachita kufunsa kuti adziwe zambiri zokhudza nyenyeziyo. Iyo inalondolera anthuwo choyamba kwa Herode, ku Yerusalemu, yemwe anali mdani woopsa wa Mesiya ndipo ankafuna kupha Yesu. Kenako nyenyezi ija inaonekanso n’kuyamba kulowera kum’mwera ndipo inalondolera okhulupirira nyenyeziwo ku Betelehemu, kumene Yesu anali. Zimenezi zinaika pachiswe moyo wa Yesu.
Mfundo zimenezi zikusonyeza kuti nyenyezi imeneyi iyenera kuti inali yochokera kwa Satana Mdyerekezi. Baibulo limafotokoza kuti iye amachita “zizindikiro zabodza ndi zodabwitsa.” (2 Atesalonika 2:9) Choncho Akhristu oona sayenera kukaikira kuti Satana angachititse anthu okhulupirira nyenyezi kuona chinthu chooneka ngati nyenyezi ndipo iye angachititsenso “nyenyezi” imeneyo kuti iwatsogolere kwa Mwana wa Mulungu, yemwe iye ankafuna kumupha. Koma palibe munthu amene angalepheretse Yehova Mulungu kukwaniritsa cholinga chake. Choncho, n’zosadabwitsa kuti chiwembu cha Mdyerekezi choti aphe Yesu chinalephereka.
Komabe, n’zoona kuti Mulungu analengeza za kubadwa kwa Yesu mozizwitsa. Usiku umene Yesu anabadwa, mngelo anaonekera kwa abusa ndipo analengeza kuti kwabadwa “Mpulumutsi.” Mngeloyo anauzanso abusawo mmene angayendere kuti akafike kwa Yesu. Kenako angelo ambirimbiri anaonekera ndipo anayamba kutamanda Mulungu. (Luka 2:8-14) Mulungu anagwiritsa ntchito angelo amenewa, osati nyenyezi, polengeza za kubadwa kwa Yesu.