Mau kwa Inu Makolo
Chikondi cha makolo kaamba ka ana ao chiri mkhalidwe wodabwitsa. Mofanana ndi makolo ochuruka, inuyo mosakaikira muli odera nkhawa ndi kumawapatsa ana anu chiyambi chabwino m’moyo.
Koma ife tiri otsimikizira kuti inu mukuzindikira kuti pali zochuruka ku chimenechi koposa chabe kuwapezera zakudya ndi zobvala ana anu ndi kumawatumiza iwo ku sukulu kuti aphunzitsidwe. Kuti ayang’anizane nawo moyo mwachipambano, ana afunikira chitsogozo chabwino ndi maprinsipulo amene angakhalire nawo moyo. Ndipo iwo amazifunikira zimenezi kuyambira pa ubwana wao kunkabe mtsogolo. Zinthu zochititsa chisoni mu mtima zingathe kuchitika ndipo zimachitika kumene ana amalandira chithandizo mochedwa kwambiri.
Mwinamwache, mofanana ndi makolo ambiri, mumaona kukhala ngati osowa chochita ponena za kumene mungayambire ndi chimene mungawaphunzitse ana anu. Ndithudi, maprinsipulo abwino kwambiri amene sangathe kupezedwa kuli konse amapezeka m’Baibulo. Chilangizo chozikidwa pa Baibulo chiri ndi mapindu otsimikizirika. Mwa ilo, ana amafika pozindikira kuti chimene iwo ali kumaphunzitsidwa sichiri chabe lingaliro la atate kapena la mai wao. Ndicho chimene Mlengi wao akuchinena; ndicho chifuniro chache. Ichi chimapereka nyonga ku uphungu wa makolo imene singathe kuyerekezeredwa m’njira ina iri yonse.
M’masamba a Baibulo Mulungu amawalimbikitsa makolo kukhala ndi chikondwelero chaumwini m’kumawakhomereza maprinsipulo oyenera pa maganizo a ana ao. Kungaonekere kukhala kwapafupi kwambiri kulipereka thayo limeneli kwa munthu wina wache. Koma kuteroko kumatanthauza kuchiphonya chokumana nacho chabwino kwambiri. Kumatanthauza kutaya mwai wa kuufika mtima wa mwana wanu m’njira imene inu ndipo osati wina ali yense akadatha.
M’mabanja ambiri lero lino makolo ndi ana ali kumagawanika mosalekeza. Pamene ana akukula, makolo kawirikawiri amapeza kukhala kobvuta moonjezereka kulankhula nawo zinthu zimene ziri zofunika kopambana. Bukhu ili lakuti, “Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo,” lalinganizidwa kuthandiza kuletsa mkhalidwe woterowo m’banja lanu. Ilo lalinganizidwa kotero kuti inu ndi ana anu mungathe kuliwerenga pamodzi. Koma, koposa chimenechi, ilo lalinganizidwa kusonkhezera kukambitsirana pakati pa makolo ndi ana.
Ichi chiri chifukwa chakuti ilo limafuna mayankho kwa anawo. Mudzawapeza mafunso ambiri oyalidwa bwino m’mau osindikizidwa. Pamene mufika ku amenewa, inu mudzaona dashi (—), kukukumbutsani kuima ndi kumlimbikitsa mwana wanu kuti ayankhe. Ana amakonda kulowetsedwamo. Popanda kulowetsedwamo kumeneko chikondwelero cha mwanayo chimatha mofulumira. Komabe, chofunika kwambiri, mafunso amenewa adzakuthandizani kuchidziwa chimene chiri pa maganizo a mwana wanu, Inde, mwanayo angaturutse mayankho amene ali osalondola. Koma mau osindikizidwa amene atsatira funso liri lonse alinganizidwa kumthandiza mwanayo kuzikulitsa njira zabwino za kuganizira.
Pamene mwanayo aphunzira kuwerenga, mlimbikitseni iye kukuwerengerani bukhulo, ndipo nthawi zina kudziwerengera yekha. Pamene iye aliwerenga ilo, ndi pamenenso uphungu wache wabwino udzakhomerezeka pa maganizo ache ndi mtima. Koma, kuti muzilimbikitse zomangira za chikondi ndi ulemu pakati pa makolo awirinu ndi mwana wanu, mwa njira iri yonse liwerengeni bukhulo pamodzi, ndipo kuchiteni iko mokhazikika.
Malemba ena a Baibulo asonyezedwa ku mapeto kwa chaputara chiri chonse. Bwanji osakhala ndi nthawi kuwafunafuna amenewa limodzi? Mwa njira imeneyo inuyo ndi mwana wanu mungathe kuphunzira kuligwiritsira nchito Baibulo bwino lomwe. Fotokozani chimene malemba amenewa ali kumachinena. Thandizani kuwamveketsa bwino mau ali onse obvuta m’malemba amene muwafunafuna, monga momwe kwachitidwira m’bukhu ili. Pomachita ichi, inu mudzakhala mukumachitsogolera chisamaliro cha mwana wanu ku magwero abwino kopambana a chitsogozo m’moyo, Baibulo.
Ife moona mtima tikukhulupilira kuti bukhu ili lidzakuthandizani inu ndi banja lanu kuiumba miyoyo yanu kuti mukhale okondweretsa kwa Mlengi, ku dalitso lanu lamuyaya.
—AFALITSI