Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso
Pamene Yesu anali padziko lapansi, anauza otsatira ake kupempherera Ufumu wa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Iye analankhulanso mosalekeza ponena za “mbiri yabwino yaufumu.” (Mateyu 4:23, NW) Ndithudi, iye analankhula zambiri ponena za Ufumu kuposa mmene anachitira za chinthu china chirichonse. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Ufumu ndiwo chiwiya chimene Mulungu adzagwiritsira ntchito kuthetsa mavuto amene amapangitsa moyo kukhala wovuta kwambiri lerolino. Kupyolera mwa Ufumuwo, posachedwapa Mulungu adzathetsa nkhondo, njala, matenda, ndi upandu, ndipo adzabweretsa umodzi ndi mtendere.
Kodi mukanakonda kukhala m’dziko lotero? Ngati ziri choncho, pamenepo muyenera kuwerenga kabukhu kano. Munomu, mudzaphunziramo kuti Ufumu ndiwo boma, koma liri labwino kwambiri loposa boma lirilonse limene linalamulirapo anthu. Mudzawonanso njira yochititsa chidwi imene Mulungu analongosolera atumiki ake mwapang’ono pang’ono zifuno zake zonena za Ufumuwo. Mkuwonjezera, mudzawona mmene Ufumu ungakuthandizireni ngakhale lerolino.
Ndithudi, mungakhale nzika ya Ufumu wa Mulungu tsopano lino. Koma musanasankhe kuchita ichi, mudzafunikira kudziwa zowonjezereka ponena za uwo. Chotero tikukulimbikitsani kupenda kabukhu kano. Chirichonse chimene kadzakuuzani ponena za Ufumu chatengedwa m’Baibulo.
Choyamba, tiyeni tiwone chifukwa chake timafuna Ufumu wa Mulungu kwambiri chotero.
Pachiyambi cha mbiri ya anthu, Mulungu anapanga munthu wangwiro namuika m’paradaiso. Panthawiyo panalibe kufunikira kwa Ufumu.
Komabe, Adamu ndi Hava, makolo athu oyamba, anamvetsera Satana, mngelo wopanduka. Iye anawauza bodza ponena za Mulungu ndipo anawachititsanso kupandukira Mulungu. Chotero iwo anayenera kufa, chifukwa chakuti “mphotho yake ya uchimo ndiyo imfa.”—Aroma 6:23.
Munthu wopanda ungwiro, wochimwa sangathe kubala ana angwiro. Chotero ana onse a Adamu anabadwa ali opanda ungwiro, ochimwa, omafa.—Aroma 5:12.
Kuyambira pamenepo kumkabe mtsogolo, anthu anafunikira Ufumu wa Mulungu kuwathandiza kuwonjoka kuthemberero la uchimo ndi imfa. Ufumuwo udzachotseranso dzina la Mulungu mabodza amene Satana ananena motsutsana nalo.
Yehova Mulungu analonjeza kuti “mbewu” yapadera (kapena mbadwa) ikabadwa kuwombola anthu kuuchimo. (Genesis 3:15) “Mbewu” imeneyi ikakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.
Kodi ameneyo akakhala yani?
Pafupifupi zaka 2,000 Adamu atachimwa, panali munthu wina wokhulupirika kwambiri wotchedwa Abrahamu. Yehova anauza Abrahamu kuchoka mu mzinda wakwawo ndi kukakhala m’mahema m’dziko la Palestina.
Abrahamu anachita zonse zimene Yehova anamuuza kuchita, kuphatikizapo chinthu chimodzi chovuta kwambiri. Yehova anamuuza kupereka nsembe mwana wake Isake paguwa lansembe.
Yehova sanafunedi nsembe ya munthu. Koma iye anafuna kudziwa mmene Abrahamu anamkondera. Abrahamu anafika pamfundo ya kupha Isake pamene Yehova anamletsa.
Chifukwa cha chikhulupiriro chachikulu cha Abrahamu, Yehova analonjeza kupereka dziko la Palestina kwa mbadwa zake nanena kuti Mbewu yolonjezedwa ikadzera mumzera wake, ndi uja wa mwana wake Isake.—Genesis 22:17, 18; 26:4, 5.
Isake anali ndi ana aamuna amapasa, Esau ndi Yakobo. Yehova ananena kuti Mbewu yolonjezedwayo ikadzera mwa Yakobo.—Genesis 28:13-15.
Yakobo, amene Yehova anamutchanso Israyeli, anali ndi ana aamuna 12, amene potsirizira pake onsewo anali ndi ana. Chotero ana a Abrahamu anayamba kuchuluka.—Genesis 46:8-27.
Pamene munali njala yaikulu m’dzikolo, Yakobo ndi banja lake anasamukira ku Igupto ataitanidwa ndi Farao, wolamulira wa Igupto.—Genesis 45:16-20.
Mu Igupto kunavumbulutsidwa kuti Mbewu yolonjezedwayo ikakhala mbadwa ya mwana wa Yakobo Yuda.—Genesis 49:10.
Potsirizira pake Yakobo anamwalira, ndipo mbewu yake inakula m’chiwerengero kufikira kuti anali ngati mtundu. Pamenepo Aigupto anagwidwa ndi mantha chifukwa cha iwo nawapanga kukhala akapolo.—Eksodo 1:7-14.
Potsirizira Yehova anatumiza Mose, mwamuna wokhulupirika kwambiri, kukaumiriza kuti Farao wapanthawiyo alole ana a Israyeli amuke mwaufulu.—Eksodo 6:10, 11.
Farao anakana, chotero Yehova anabweretsa miliri khumi pa Aigupto. Monga mliri wotsiriza iye anatumiza mngelo wowononga kukapha ana aamuna achisamba onse a Igupto.—Eksodo, mutu 7 kufikira 12.
Mulungu anauza Aisrayeli kuti ngati iwo akanapha mwana wankhosa kaamba ka chakudya chawo chamadzulo ndi kuwaza wina wa mwazi wake pamphuthu za nyumba, mngelo wowonongayo akalambalala nyumba zawo. Chotero mwana wachisamba Wachiisrayeli anapulumutsidwa.—Eksodo 12:1-35.
Monga chotulukapo, Farao analamula Aisrayeli kutuluka m’Igupto. Koma pambuyo pake iye anasintha maganizo ake nalondola kuti awabweze.
Yehova anatsegula njira kaamba ka Aisrayeli kuwoloka Nyanja Yofiira. Ndipo pamene Farao ndi makamu ake anayesa kuwatsatira, anamizidwa.—Eksodo 15:5-21.
Yehova anatsogolera ana a Israyeli kumka kuphiri lotchedwa Sinai m’chipululu. Kumeneko, iye anawapatsa Chilamulo chake nanena kuti ngati iwo akachisunga, akakhala ansembe achifumu ndi mtundu wopatulika. Chotero, m’kupita kwanthawi, Aisrayeli anali ndi mwayi wa kukhala mbali yofunika ya Ufumu wa Mulungu.—Eksodo 19:6; 24:3-8.
Aisrayeli atakhala pa Phiri la Sinai kwapafupifupi chaka chimodzi, Yehova anawatsogolera kumka ku Palestina, dziko limene anali atalonjeza Abrahamu kholo lawo.
Pambuyo pake m’Palestina, Mulungu analola Aisrayeli kulamulidwa ndi mafumu. Pamenepa, Mulungu anali ndi ufumu padziko lapansi.
Mfumu yachiwiri ya Israyeli anali Davide, mbadwa ya Yuda. Davide anagonjetsa adani onse a Israyeli, ndipo anapanga Yerusalemu kukhala likuru la mtunduwo.
Zochitika muulamuliro wa Davide zimasonyeza kuti pamene Yehova achirikiza mfumu, palibe wolamulira wa padziko lapansi amene angaigonjetse.
Yehova adanena kuti Mbewu yolonjezedwa ikakhala mmodzi wa mbadwa za Davide.—1 Mbiri 17:7, 11, 14.
Solomo, mwana wamwamuna wa Davide, analamulira pambuyo pake. Iye anali mfumu yanzeru, ndipo Israyeli analemerera pansi pa ulamuliro wake.
Solomo anamangiranso Yehova kachisi wabwino kwambiri m’Yerusalemu. Mikhalidwe m’Israyeli pansi pa ulamuliro wa Solomo imatisonyeza za ena a madalitso amene Ufumu wa Mulungu ulinkudza udzabweretsera anthu.—1 Mafumu 4:24, 25.
Komabe, ambiri a mafumu odza pambuyo pa Solomo anali osakhulupirika kwambiri.
Koma pamene mbadwa za Davide zinali kulamulirabe m’Yerusalemu, Yehova anagwiritsira ntchito mnereri wake Yesaya kuneneratu za Mwana wamtsogolo wa Davide amene akalamulira dziko lonse lapansi mokhulupirika. Ameneyu akakhala Mbewu yolonjezedwa.—Yesaya 9:6, 7.
Mneneri Yesaya analosera za ulamuliro Wake kukhaladi waulemerero kwambiri koposa wa Solomo.—Yesaya, mutu 11 ndi 65.
Tsopano, koposa ndi kale lonse, atumiki a Mulungu anadabwa amene Mbewu iyi ikakhala.
Komabe, Mbewuyo isanadze, mafumu a Israyeli anaipa kwambiri kotero kuti mu 607 B.C.E. Yehova analola mtunduwo kugonjetsedwa ndi Ababulo, ndipo unyinji wa anthuwo unatengeredwa kuukapolo ku Babulo. Koma Mulungu sanaiwale lonjezo lake. Mbewuyo ikawonekerabe mumzera wa Davide.—Ezekieli 21:25-27.
Zimene zinachitikira Israyeli zinasonyeza kuti ngakhale ngati mfumu yaumunthu yanzeru yokhulupirika, ingabweretse mapindu, mapindu amenewo anali operewera. Anthu okhulupirika amafa ndipo owalowa m’malo mwawo angakhale osakhulupirika. Kodi nchiyani chimene chinali njira yothetsera vutolo? Mbewu yolonjezedwa.
Potsirizira pake, pambuyo pazaka mazana ambiri, Mbewuyo inawonekera. Kodi iyo inali yani?
Mngelo wochokera kwa Mulungu anapereka yankho kwa msungwana wosakwatibwa Wachiisrayeli wotchedwa Mariya. Iye anamuuza kuti akakhala ndi mwana amene dzina lake likakhala Yesu. Nazi zimene mngeloyo adanena:
“Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: Ambuye Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate wake. Ndipo iye adzachita ufumu.”—Luka 1: 32, 33.
Chotero Yesu anali kudzakhala Mbewu yolonjezedwa ndipo potsirizira pake kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Koma kodi nchifukwa ninji Yesu anali wosiyana ndi amuna okhulupirika amene anali atakhala ndi moyo kalelo?
Yesu anabadwa mwanjira yozizwitsa. Amake anali namwali, chotero analibe atate waumunthu. Yesu anali atakhala ndi moyo kalelo m’mwamba ndipo mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, unasamutsira moyo wa Yesu kuchokera kumwamba kulowa m’mimba mwa Mariya. Chifukwa chake, iye sanalandira cholowa cha uchimo wa Adamu. Nthawi yonse ya moyo wake, Yesu sanachimwe.—1 Petro 2:22.
Pamene anali wazaka 30 zakubadwa, Yesu anabatizidwa.
Iye anauza anthu za Ufumu wa Mulungu ndipo potsirizira pake anadzidziwikitsa kukhala Mfumu ya Ufumuwo.—Mateyu 4:23; 21:4-11.
Iye anachitanso zozizwitsa zambiri.
Anachiritsa odwala.—Mateyu 9:35.
Iye mozizwitsa anadyetsa anjala.—Mateyu 14:14-22.
Iye anaukitsa ngakhale akufa.—Yohane 11:38-44.
Zozizwitsa izi zimasonyeza mtundu wa zinthu zimene Yesu adzachitira anthu monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.
Kodi mukukumbukira mmene Mfumu Davide anali atapangira Yerusalemu kukhala likulu la ufumu wake? Yesu analongosola kuti Ufumu wa Mulungu sukakhala padziko lapansi, koma kumwamba. (Yohane 18:36) Ndicho chifukwa chake Ufumuwo umatchedwera “Ufumu wakumwamba.”—Ahebri 12:22, 28.
Yesu anatchula malamulo amene anthu omwe akakhala nzika za Ufumuwo akafunikira kumvera. Malamulo amenewa tsopano ali m’Baibulo. Malamulo ofunika kopambana anali akuti anthu ayenera kukonda Mulungu ndi kukondana wina ndi mnzake.—Mateyu 22:37-39.
Yesu anaululanso kuti sakakhala yekha polamulira mu Ufumu wake. Pakakhala anthu osankhidwa kupita kumwamba ndi kukalamulira komweko limodzi naye. (Luka 12:32; Yohane 14:3) Kodi ndiangati amene akakhala kumeneko? Chivumbulutso 14:1 chimayankha kuti: 144,000.
Ngati a 144,000 okha amapita kumwamba kukalamulira ndi Yesu, kodi nchiyani chimene otsala a anthu onse akuchiyembekezera?
Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Awo amene adzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi amatchedwa “nkhosa zina.”—Yohane 10:16.
Chotero pali ziyembekezo ziwiri. Pali a 144,000 oitanidwa ndi Yehova Mulungu kupita kumwamba kukalamulira ndi Yesu Kristu. Koma mamiliyoni ambiri a otsalawo ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kukhala ndi moyo padziko lapansi kosatha monga nzika za Ufumu wake.—Chivumbulutso 5:10.
Satana anada Yesu namtsutsa. Yesu atalalikira kwazaka zitatu ndi theka, Satana anamchititsa kuti agwidwe ndi kuphedwa mwa kukhomereredwa pamtengo. Kodi nchifukwa ninji Mulungu analola ichi?
Kumbukirani, kuti chifukwa cha kukhala mbadwa zochokera kwa Adamu, tonsefe timachimwa ndipo timayenera kufa.—Aroma 6:23.
Kumbukiraninso, kuti, chifukwa cha njira yozizwitsa mwa imene Yesu anabadwira, anali wangwiro ndipo sanafunikire kufa. Komabe, Mulungu analola Satana ‘kuzunzunda Yesu kuchitende,’ kumupha. Koma Mulungu anamuukitsiranso kumoyo monga cholengedwa chosakhoza kufa chauzimu. Popeza kuti iye anali chikhalirebe ndi kuyenera kwa kukhala ndi moyo wangwiro waumunthu, iye tsopano akanagwiritsira ntchito moyowu kuwombolera anthufe kuuchimo.—Genesis 3:15; Aroma 5:12, 21; Mateyu 20:28.
Kutithandiza kuzindikira mokwanira chimene nsembe ya Yesu imatanthauza, Baibulo limalankhula za iyo mwanjira ya zitsanzo zolosera.
Mwachitanzo, kodi mukukumbukira mmene Yehova anauzira Abrahamu kupereka mwana wake nsembe, monga chiyeso cha chikondi chake?
Ichi chinali chitsanzo cholosera cha nsembe ya Yesu. Chinasonyeza mmene chikondi cha Yehova kaamba ka anthu chinaliri chachikulu kwambiri kotero kuti analola Mwana wake, Yesu, kutifera kuti tikhale ndi moyo.—Yohane 3:16.
Kodi mukukumbukira njira imene Yehova anaombolera nayo Aisrayeli kuchokera m’Igupto ndi kupulumutsa ana awo achisamba mwa kuchititsa mngelo wakupha kuwalambalala?—Eksodo 12:12, 13.
Ichi chinali chitsanzo cholosera. Monga momwedi mwazi wa mwana wa nkhosa unatanthauzira moyo kwa ana achisamba Achiisrayeli, mwazi wokhetsedwa wa Yesu umatanthauza moyo kaamba ka awo amene amamkhulupirira. Ndipo monga momwe zochitika pausikuwo zinatanthauzira chimasuko kwa Aisrayeli, imfa ya Yesu imapereka kwa anthuwo chimasuko kuuchimo ndi imfa.
Ndicho chifukwa chake Yesu akutchedwera “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa uchimo wa dziko.”—Yohane 1:29.
Komabe, pamene Yesu anali padziko lapansi anasonkhanitsanso ophunzira nawaphunzitsa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu, ngakhale pambuyo pa imfa yake.—Mateyu 10:5; Luka 10:1.
Amenewa anali anthu oyamba kusankhidwa ndi Mulungu kudzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wake.—Luka 12:32.
Kodi mukukumbukira kuti Mulungu analonjeza Ayuda kuti ngati akasunga Chilamulo, iwo akakhala “ufumu wa ansembe”? Tsopano iwo anali ndi mwayi wa kukhala mbali ya Ufumu wa Mulungu ndi kutumikira monga ansembe akumwamba ngati akanavomereza Yesu. Koma unyinji wa iwo unakana Yesu.
Chotero kuyambira panthawiyo kunkabe mtsogolo, Ayuda sanalinso mtundu wosankhidwa wa Mulungu; Palestina silinalinso Dziko Lolonjezedwa.—Mateyu 21:43; 23:37, 38.
Kuyambira m’tsiku la Yesu kufikira m’lathu, Yehova wakhala akusonkhanitsa anthuwa amene akalamulira kumwamba limodzi ndi Yesu. Padakali chikhalirebe zikwi zochepekera za iwo zamoyo padziko lapansi lerolino. Timawatcha otsalira odzozedwa.—Chivumbulutso 12:17.
Tsopano, mukuyamba kuwona chimene Ufumu wa Mulungu uli. Ndiro boma lakumwamba, Mfumu yake ndiye Yesu Kristu, ndipo ngwogwirizanitsidwa ndi anthu 144,000 ochokera padziko lapansi. Uwo udzalamulira pa anthu okhulupirika padziko lapansi ndipo udzakhala ndi mphamvu ya kubweretsa mtendere padziko lapansi.
Pambuyo pa imfa yake, Yesu anaukitsidwa napita kumwamba. Kumeneko, iye anayembekezera Mulungu kunena imene ikakhala nthawi yoti ayambe kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Salmo 110:1) Kodi nthawiyo ikakhala liti?
Nthawi zina Yehova anatumiza maloto kwa anthu kuti awauze zinthu zonena za Ufumu wake.
M’tsiku la Danieli, Yehova anatumiza loto lotero kwa Nebukadinezara, mfumu ya Babulo. Linali la mtengo waukulu.—Danieli 4:10-37.
Mtengowo unadulidwa ndipo chitsa chinamangidwa mikombero kwazaka zisanu ndi ziwiri.
Mtengowo unaimira Nebukadinezara. Monga momwe chitsa chidamangidwa mikombero kwazaka zisanu ndi ziwiri, Nebukadinezara anapenga kwazaka zisanu ndi ziwiri. Ndiyeno kupenga kwake kunatha.
Zonsezi zinali chitsanzo cholosera. Nebukadinezara anaphiphiritsira ulamuliro wa Yehova wapadziko lonse lapansi. Poyamba, umenewu unachitidwa kudzera mwa mbadwa za Mfumu Davide m’Yerusalemu. Pamene Babulo anagonjetsa Yerusalemu mu 607 B.C.E., mzera umenewo wa mafumu unadodometsedwa. Sipakakhalanso mfumu ina mumzera wa Davide “kufikira akadza iye mwini chiweruzo.” (Ezekieli 21:27) Ameneyo anali Yesu Kristu.
Kodi pakapita zaka zingati kuchokera 607 B.C.E. kufikira pamene Yesu akayamba kulamulira? Zaka zolosera zisanu ndi ziwiri. Ndiko kuti, zaka 2,520. (Chivumbulutso 12:6, 14) Ndipo zaka 2,520 kuchokera 607 B.C.E. zikutifikitsa ku 1914 C.E.
Chotero Yesu anayamba kulamulira m’miyamba mu 1914. Kodi zimenezo zinatanthauzanji?
Baibulo limatiuza kupyolera mwa masomphenya owonedwa ndi mtumwi Yohane.
Iye anawona mkazi m’mwamba ali kubala mwana wamwamuna.—Chivumbulutso 12:1-12.
Mkaziyo anaphiphiritsira gulu lakumwamba la Mulungu, lopangidwa ndi atumiki aungelo onse a Mulungu m’mwamba. Mwana wamwamunayo amaphiphiritsira Ufumu wa Mulungu. Umenewu “unabadwa” mu 1914.
Kodi nchiyani chimene chinachitika kenako? Chinthu choyamba chimene Yesu anachita monga Mfumu chinali kuchotsa Satana, ndi angelo opanduka aja limodzi naye, kuwagwetsera padziko lapansi kuchokera m’mwamba.—Chivumbulutso 12:7.
Baibulo limatiuza chotulukapo: “Kondwerani, miyambi inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.”—Chivumbulutso 12:12.
Chotero pamene Yesu anayamba kulamulira m’mwamba, adani ake anafikira kukhala okangalika kwambiri padziko lapansi. Monga momwe Baibulo linaneneratu, iye anayamba kulamulira pakati pa adani ake.—Salmo 110:1, 2.
Kodi ichi chikatanthauzanji kwa anthu?
Yesu anatiuza kuti: nkhondo, kuperewera kwa zakudya, matenda, ndi zivomezi.—Mateyu 24:7, 8; Luka 21:10, 11.
Tawona zinthu izi zikumachitika chiyambire 1914, chimene chiri chifukwa china chotidziwitsa kuti Ufumu unayamba kulamulira panthawiyo.
Buku la Chivumbulutso limatiuza kuti anthu akakhala “akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:18) Taonanso zimenezo, makamaka chiyambire 1914.
Mtumwi Paulo anawonjezera kuti anthu akakhala “odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osamvera akuwabala, . . . osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa.”—2 Timoteo 3:1-5.
Tsopano mukudziwa chifukwa chake moyo uli wovuta kwambiri lerolino. Satana wakhala wokangalika kwambiri. Koma Ufumu wa Mulungu wakhalanso wokangalika.
Mwamsanga pambuyo pa 1914, otsalira a awo oyembekezera kukalamulira kumwamba ndi Yesu anayamba kulengeza mbiri yabwino yakuti Ufumuwo unali utakhazikitsidwa. Ntchitoyi tsopano yafalikira padziko lonse lapansi, monga momwe Yesu adanenera kuti ikachitira.—Mateyu 24:14.
Kodi chifuno cha ntchito yolalikirayi nchiyani?
Choyamba, ndicho kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu.
Chachiwiri, ndicho kuthandiza anthu kusankha kuti kaya akufuna kukhala nzika za Ufumu umenewo.
Yesu ananena kuti m’masiku athu anthu onse akalekanitsidwa kukhala anthu onga nkhosa ndi anthu onga mbuzi.—Mateyu 25:31-46.
“Nkhosa” zikakhala awo amene akamkonda iye ndi abale ake. “Mbuzi” zikakhala awo amene sakatero.
“Nkhosa” zikalandira moyo wosatha ndipo “mbuzi” sizikatero.
Ntchito yolekanitsa imeneyi ikukwaniritsidwa mwa kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu.
Nawu ulosi woperekedwa ndi mneneri Yesaya.
“Ndipo padzakhala masiku otsirizira kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.”—Yesaya 2:2.
Anthu tsopano ali mu “Masiku otsiriza.”
“Nyumba” ya Yehova yolambirira iri ‘kukwezedwa’ pamwamba pa zipembedzo zonyenga.
“Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kumka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.”—Yesaya 2:3.
Chotero ochuluka ochokera m’mitundu yonse akudza kudzalambira Yehova ndipo akuitana ena kugwirizana nawo. Iwo amaphunzira mmene angachitire m’njira imene Yehova afuna.
“Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo zadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.
Awo amene amalambira Yehova ali ogwirizana ndi amtendere.
Chotulukapo cha ntchitoyi yochitidwa ndi Ufumu wa Mulungu nchakuti tsopano pali anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi amene ali nzika za Ufumuwo.
Iwo asonkhanitsidwa mozinga otsalira, otsala a awo amene chiyembekezo chawo chiri cha kupita kumwamba ndi kukalamulira limodzi ndi Kristu.
Iwo amalandira chakudya chauzimu kupyolera mwa gulu la Mulungu.—Mateyu 24:45-47.
Iwo ali Akristu okhala paubale wa m’mitundu yonse amene amakondanadi wina ndi mnzake.—Yohane 13:35.
Iwo ali ndi mtendere wamaganizo, chiyembekezo cha mtsogolo.—Afilipi 4:7.
Posachedwa, mbiri yabwino idzakhala italalikiridwa. “Nkhosa” zidzakhala zitasonkhanitsidwa. Pamenepo kodi Ufumuwo udzachitanji?
Kodi mukukumbukira kuti Mfumu Davide yokhulupirikayo inagonjetsa adani onse a anthu a Mulungu? Eya, Mfumuyo Yesu idzachita zofanana.
Mfumu Nebukadinezara panthawi ina analota fano lalikuru limene linaphiphiritsirira maulamuliro onse adziko kuyambira panthawi yake mpaka yathu.
Ndiyeno iye anawona mwala ukusemedwa m’phiri, ndipo unaphwanya fanolo kukhala tizidutswa. Mwalawo unaimira Ufumu wa Mulungu.
Ichi chikutanthauza chiwonongeko cha dongosolo loipa liripoli lazinthu.—Danieli 2:44.
Nazi zinthu zina zimene Ufumuwo udzawononga.
Chipembedzo chonyenga chidzazimiririka, mofanana ndi mwala wamphero woponyedwa m’nyanja.—Chivumbulutso 18:21.
Ndicho chifukwa chake onse okonda Mulungu akulimbikitsidwa kutuluka m’chipembedzo chonyenga TSOPANO LINO.—Chivumbulutso 18:4.
Kenako Mfumu Yesu “adzakantha mitundu . . . ndipo adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo.”—Chivumbulutso 19:15.
Ndicho chifukwa chake, ngakhale kuli kwakuti Mboni za Yehova zimakhoma misonkho yawo ndi kumvera malamulo adziko, izo sizimalowa m’ndale zadziko.
Potsirizira pake, Satana iyemwiniyo, “chinjoka chachikulu,” akuponyedwa m’phompho.—Chivumbulutso 20:2, 3.
Ziri “nkhosa” zokha zimene zimagonjera kwa Yesu monga Mfumu, zimene zidzapulumuka chisautso ichi.—Mateyu 25:31-34, 41, 46.
Mtumwi Yohane adawona masomphenya a “nkhosa” zimene zikupulumuka chisautso.
“Ndinawona, ndipo, tawonani! khamu lalikuru limene palibe munthu anakhoza kuliwerenga, lochokera m’mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, lirinkuimirira pamaso pampando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, lovala miinjiro yoyera; ndipo m’manja mwawo munali makhwatha akanjedza.”—Chivumbulutso 7:9, NW.
“Khamu lalikuru” lapangidwa ndi onse amene akulabadira ku kulalikidwa kwa mbiri yabwino.
Iwo “akutuluka m’chisautso chachikulu.”—Chivumbulutso 7:14, NW.
“Makhwatha akanjedza amasonyeza kuti iwo amavomereza Yesu monga Mfumu yawo.
Kuvala kwawo “miinjiro yoyera” kumachitira chithunzi kuti iwo ali ndi chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu.
“Mwanawankhosayo” ndiye Yesu Kristu.
Kodi ndi madalitso otani amene iwo akusangalala nawo panthawiyo? Kodi mukukumbukira chimwemwe mu Israyeli pamene Mfumu Solomo wokhulupirika anali kulamulira? Ichi chinapereka chithunzi chaching’ono cha chimwemwe padziko lapansi lolamulidwa ndi Mfumu Yesu.
Padzakhala mtendere weniweni pakati pa mtundu wa anthu ndi pakati pa anthu ndi zinyama, monga momwedi Yesaya adaneneratu.—Salmo 46:9; Yesaya 11:6-9.
Monga momwedi Yesu anachiritsira odwala pamene anali padziko lapansi, chotero iye adzachotsa matenda mwa anthu onse.—Yesaya 33:24.
Monga momwedi iye anadyetsera makamu a anthu, chotero iye adzathetsa kuperewera kwa zakudya pa mtundu wonse wa anthu.—Salmo 72:16.
Monga momwedi iye anaukitsira akufa, chotero adzaukitsa akufa amene analibe mwayi wokwanira wa kudzigonjetsera ku Ufumu wa Mulungu.—Yohane 5:28, 29.
Pang’ono pang’ono, adzabwezeretsera anthu kuungwiro umene Adamu adataya.
Kodi m’menemo sindimo mtsogolo mwabwino kwambiri? Kodi mukakonda kumuwona? Ngati ziri choncho, gwirani ntchito kotero kuti inu tsopano mudzigonjetsere ku Ufumu wa Mulungu ndi kukhala mmodzi wa “nkhosa.”
Phunzirani Baibulo ndi kufikira pa kudziwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu.—Yohane 17:3.
Sonkhanani ndi ena amenenso ali nzika za Ufumu.—Ahebri 10:25.
Phunzirani malamulo a Ufumu ndi kuwamvera.—Yesaya 2:3, 4.
Patulirani moyo wanu ku kutumikira Yehova, ndipo batizidwani.—Mateyu 28:19, 20.
Pewani zinthu zoipa, monga kuba, kunama, chisembwere, ndi kuledzera, zimene sizimakondweretsa Yehova Mulungu.—1 Akorinto 6:9-11.
Khalani ndi phande m’kulalikiridwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu.—Mateyu 24:14.
Pamenepo mwachithandizo cha Mulungu, inu mudzawona Paradaiso amene Adamu anataira mbadwa zake akubwezeretsedwa, ndipo mudzawona lonjezo iri likumakwaniritsidwa: “Ndinamva mawu ofuula ochokera kumpando wachifumu akuti: ‘Tawonani! Chihema cha Mulungu chiri ndi anthu, ndipo iye adzakhala pamodzi ndi iwo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Ndipo Mulungu mwiniyo adzakhala limodzi nawo. Ndipo iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira ngakhale kulira maliro ngakhale kupweteka sizidzakhalakonso. Zinthu zoyambazo zapita.’”—Chivumbulutso 21:3, 4, NW.
[Tchati patsamba 20]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
607 B.C.E. 1914 C.E.
B.C.E. | C.E.
500 1,000 1,500 2,000 2,520
[Zithunzi patsamba 11]
Abrahamu
Isake
Yakobo
Yuda
Davide
[Chithunzi patsamba 14]
144,000
[Zithunzi patsamba 16]
Adamu
Yesu