Mpatuko
Tanthauzo: Mpatuko ndiko kusiya kapena kuleka kulambira ndi kutumikira Mulungu, kwenikweni ndiko kupandukira Yehova Mulungu. Ampatuko ena amadzinenera kukhala akudziŵa ndi kutumikira Mulungu koma amakana ziphunzitso kapena malamulo ondandalikidwa m’Mawu ake. Ena amanena kuti amakhulupirira Baibulo koma amakana gulu la Yehova.
Kodi tiyenera kuyembekeza kuti ampatuko adzabuka mkati mwa mpingo Wachikristu?
1 Tim. 4:1: “Mzimu unena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosokeretsa ndi maphunziro aziwanda.”
2 Ates. 2:3: “Munthu asakunyengeni konseko; kuti [tsiku la Yehova] silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa chiwonongeko.”
Zizindikiro zina za ampatuko—
Iwo amafunafuna kupanga ena kukhala otsatira awo, motero kuchititsa magaŵano a mpatuko
Mac. 20:30, NW: “Pakati panu penipeni padzabuka amuna olankhula zinthu zokhota kuti akope ophunzira awatsatire.”
2 Pet. 2:1, 3: “Padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzaloŵa nayo m’tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, . . . Ndipo m’chisiriro adzakuyesani malonda ndi mawu onyenga.”
Iwo angadzinenere kukhala okhulupirira Kristu koma nachita moluluza ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa imene anayigaŵira kwa otsatira ake
Luka 6:46: “Ndipo munditchuliranji ine Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena?”
Mat. 28:19, 20, NW: “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse, mukumawabatiza . . . mukumawaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndakulamulirani.”
Mat. 24:14: “Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu amitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”
Iwo angadzinenere kukhala akutumikira Mulungu koma amakana oimira ake, gulu lake lowoneka
Yuda 8, 11: “Momwemonso iwo m’kulota kwawo adetsa matupi awo, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero. Tsoka kwa iwo! pakuti . . . anataika m’chitsutsano cha Kora.”
Num. 16:1-3, 11, 19-21: “Kora . . . anauka pamodzi ndi amuna mazana aŵiri mphambu makumi asanu a ana a Israyeli, ndiwo akalonga a khamulo . . . ndipo anasonkhana motsutsana kwa Mose ndi Aroni, nanena nawo, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pawo; mudzikuza bwanji pamsonkhano wa Yehova? . . . [Mose anati:] Iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye? Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nawo kukhomo la chihema chokumanako; ndipo ulemerero wa Yehova unawoneka kwa khamu lonse. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Dzipatuleni pakati pa khamu lino kuti ndiwathe m’kamphindi.”
Sikokha kuti iwo amakana chikhulupiriro chowona koma iwo “amamenya” atsamwali awo oyambawo, akumagwiritsira ntchito chisulizo chapoyera ndi njira zina kudodometsa ntchito yawo; zoyesayesa za ampatuko amenewa zalunjikitsidwa pa kugwetsa, osati kumanga
Mat. 24:45-51: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya panthaŵi yake? . . . Koma kapolo woipa akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa; nadzayamba kupanda anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera, mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekezera iye, ndi nthaŵi yosadziŵa iye, nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga.”
2 Tim. 2:16-18: “Koma peŵa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo, ndipo mawu awo adzanyeka chironda; a iwo ali Humenayo ndi Fileto; ndiwo amene adasokera kunena za chowonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.”
Kodi Akristu okhulupirika akalandira ampatuko, kaya mwa kucheza nawo kapena mwa kuŵerenga mabukhu awo?
2 Yoh. 9, 10: “Yense wakupitirira, wosakhala m’chiphunzitso cha Kristu, alibe Mulungu; . . . munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musamlankhule.”
Aroma 16:17, 18: “Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani kwa iwo. . . . ndi mawu osalaza ndi osyasyalika kusokeretsa mitima ya osalakwa.”
Kodi chivulazo chowopsa chirichonse chingadze kuchokera m’kukhutiritsa chidwi cha munthuwe ponena za maganizo a ampatuko?
Miy. 11:9, NW: “Wampatuko abweretsa chiwonongeko pa munthu mnzake ndi mkamwa mwake.”
Yes. 32:6: “Wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusoŵetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.” (Yerekezerani ndi Yesaya 65:13, 14.)
Kodi mpatuko ngwaupandu motani?
2 Pet. 2:1: “Amene adzaloŵa nayo mtseri mipatuko yotaikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.”
Yobu 13:16, NW: “Wampatuko sadzafika pamaso pake [pa Mulungu].”
Aheb. 6:4-6: “Sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anawonetsedwa panthaŵi yake, nalaŵa mphatso yakumwamba, nakhala olandirana naye mzimu woyera, nalaŵa mawu okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthaŵi irinkudza, koma anagwa m’chisokero [“ngati panthaŵiyo achita mpatuko,” RS]; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.”