Zifanizo
Tanthauzo: Kaŵirikaŵiri, kuimiridwa kowoneka kwa anthu kapena zinthu. Chifanizo chimene chiri cholambiridwa ndicho fano. Awo amene amalambira pamaso pa zifanizo kaŵirikaŵiri amanena kuti kulambira kwawo kwenikweni kumalunjikitsidwa ku chamoyo chamzimu choimiridwa ndi chifanizirocho. Kugwiritsira ntchito zifanizo kotero nkozoloŵereka m’zipembedzo zambiri zosakhala Zachikristu. Ponena za chizoloŵezi cha Roma Katolika, New Catholic Encyclopedia (1967, Vol. VII, p. 372) imati: “Popeza kulambiridwa koperekedwa ku chifanizo kumafika ndipo kumathera kwa munthu woimiridwayo, mtundu umodzimodziwo wa kulambira woyenerera munthuyo ungakhoze kuperekedwa ku chifanizocho monga choimira munthuyo.” Sichiri chiphunzitso Chabaibulo.
Kodi Mawu a Mulungu amanena chiyani ponena za kupanga zifanizo zogwiritsiridwa ntchito monga zinthu zolambiridwa?
Eks. 20:4, 5, JB: “Usadzipangire iwe wekha fano losema kapena chifanizo chirichonse cha kanthu kalikonse kakumwamba kapena ka m’dziko lapansi kapena m’madzi pansi pa dziko; usadziŵeramire izo kapena kuzitumikira [“kuŵerama pamaso pake kapena kuzilambira,” NAB.] Pakuti ine, Yahweh Mulungu wako, ndiri Mulungu wansanje.” (Kanyenye wawonjezeredwa.) (Tawonani kuti panali kuletsa kupanga zifanizo ndi kuŵerama pamaso pake.)
Lev. 26:1, JB: “Simuyenera kupanga mafano; simuyenera kuimika chifaniziro chosema kapena mwala woimirira [“mlongoti wopatulika,” NW], musadziimikira mwala wosemedwa m’dziko lanu, kuugwadira inu uwo; pakuti ndine, Yahweh, amene ali Mulungu wanu.” (Palibe chifaniziro chimene anthu akanaŵeramira kuchilambira chimene chinafunikira kuimikidwa.)
2 Akor. 6:16, JB: “Kachisi wa Mulungu samadyerana ndi mafano, ndipo ndizo zimene ife tiri—kachisi wa Mulungu wamoyo.”
1 Yoh. 5:21, NAB: “Tiana, chenjerani ndi mafano [“mafano,” Dy, CC; “milungu yonama,” JB].”
Kodi zifanizo zingagwiritsiridwe ntchito monga zothandizira kokha m’kulambiridwa kwa Mulungu wowona?
Yoh. 4:23, 24, JB: “Olambira owona adzalambira Atate mu mzimu ndi chowonadi: ndiwo mtundu wa olambira amene Atate afuna. Mulungu ndi mzimu, ndipo awo olambira ayenera kulambira mu mzimu ndi chowonadi.” (Awo amene amadalira pa zifanizo monga zithandizo kukulambira sakulambira Mulungu “mu mzimu” koma akudalira pa zimene angawone ndi maso awo aumunthu.)
2 Akor. 5:7, NAB: “Timayenda mwa chikhulupiriro, osati mwa kuwona.”
Yes. 40:18, JB: “Kodi mudzayerekezera Mulungu ndi yani? Kodi nchifaniziro chotani chimene mungamuyerekezere nacho”?
Mac. 17:29, JB; “Popeza ndife ana a Mulungu, tiribe chodzikhululukira nacho cholingalirira kuti Mulungu amafanana ndi kanthu kalikonse konga golide, siliva kapena mwala wosemedwa ndi wolinganizidwa ndi munthu.”
Yes. 42:8, JB: “Dzina langa ndine Yahweh, sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina, kapena ulemu wanga kumafano [“zinthu zosemedwa,” Dy].”
Kodi tiyenera kulemekeza “oyera mtima” monga otitetezera kwa Mulungu, mwinamwake kugwiritsira ntchito zifanizo zawo monga zithandizo m’kulambira kwathu?
Mac. 10:25, 26, JB: “Pamene Petro anafika panyumbapo Korneliyo anatuluka kukakomana naye, anagwada pamapazi ake namuŵeramira. Koma Petro anamthandiza kunyamuka. ‘Nyamuka,’ iye anatero ‘ndiiko komwe ine ndiri munthu chabe!’” (Popeza Petro sanavomereze kuŵeramiridwa kotero pamene iye mwini analipo, kodi akanatilimbikitsa kugwada pamaso pa chifanizo chake? Wonaninso Chivumbulutso 19:10.)
Yoh. 14:6, 14, JB: “Yesu anati: ‘Ndine Njira, Chowonadi ndi Moyo. Palibe munthu adza kwa Atate kusiyapo kupyolera mwa ine. Ngati mupempha kanthu kalikonse m’dzina langa, ndidzakachita.’” (Panopa Yesu akufotokoza momvekera bwino kuti kuyandikira kwathu kwa Atate kungakhale kokha kupyolera mwa iye ndi kuti mapempho athu ayenera kupangidwa m’dzina la Yesu.)
1 Tim. 2:5, JB: “Pali Mulungu mmodzi yekha ndipo pali mtetezi mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, iye mwiniyo munthu, Kristu Yesu.” (Panopa palibe mpata wakuti ena atumikire paudindo wamtetezi kaamba ka ziŵalo za mpingo wa Kristu.)
Wonaninso tsamba 332, 333, pa mutu wakuti “Oyera Mtima.”
Kodi olambira amalingalira kwakukulukulu munthu woimiridwa ndi chifanizo, kapena kodi zifanizo zina zimawonedwa monga zapamwamba?
Maganizo a olambira ali mfundo yofunika kuilingalira. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kusiyana kwakukulu pakati pa “chifanizo” ndi “fano” ndiko mmene chifanizocho chikugwiritsidwira ntchito.
M’maganizo a wolambirayo, kodi chifanizo chimodzi cha munthu chimakhala chopindulitsa kwambiri kapena chofunika koposa chifanizo china cha munthu mmodzimodziyo? Ngati ziri choncho, chiri chifanizo, osati munthuyo, chimene wolambirayo akuchilingalira kwakukulukulu. Kodi nchifukwa ninji anthu amayenda maulendo aatali kumaiko achilendo kukalambira patiakachisi takutitakuti? Kodi sichifanizo chenicheni chimene chimawonedwa kukhala chiri ndi mphamvu “zozizwitsa?” Mwachitsanzo, m’bukhu lotchedwa Les Trois Notre-Dame de la Cathédrale de Chartres, lolembedwa ndi mtsogoleri wachipembedzo Yves Delaporte, tikuuzidwa ponena za zifanizo za Mariya m’tchalitchi chachikulu m’Chartres, Faransa kuti: “Zifanizo zimenezi, zosemedwa, zopakidwa utoto kapena zowonekera m’mazenera agalasi okhathamiritsidwa, siziri zotchuka mofanana. . . . Zinthu zitatu zokha ndizo zomwe ziri zolambiridwa kwenikweni: Dona Wathu wa Crypt, Dona Wathu wa Mlongoti, ndi Dona Wathu wa ‘Belle Verriere.’” Koma ngati olambira anali kwakukulukulu kulingalira munthuyo, osati chifanizo, chifanizo chimodzi chikanangolingaliridwa kukhala chabwino mofanana ndi china, kodi sichoncho?
Kodi ndimotani mmene Mulungu amawonera zifanizo zimene zimalambiridwa?
Yer. 10:14, 15, JB: “Wosula golide aliyense amachita manyazi kaamba ka fano limene walipanga, popeza zifanizo zake siziri kanthu kena koma chinyengo, zopanda mpweya mwa izo. Ziri Zachabe, zoseketsa.”
Yes. 44:13-19, JB: “Mmisiri wosema amayesa, nalemba chifanizirocho ndi choko, achisema ndi ntcherero, nachilemba ndi zolinganizira. Amachipanga kuti chikhale ndi mawonekedwe a munthu, nachipatsa nkhope ya munthu, kuti icho chikhale m’kachisi. Iye adula mkungudza, kaya mwinamwake anatenga mtengo wa mbaŵa, kapena wathundu umene anasankha pamitengo ya m’nkhalango, kapena mwinamwake iye anawoka mkungudza ndipo mvula inaukulitsa. Kwa munthu wamba uli kwenikweni nkhuni; amaugwiritsira ntchito kuwotha, iye amaukolezanso kuwotchera mkate wake. Koma bwenzi lake limapanganawo mulungu ndi kumlambira; amapanga nawo fano ndipo amaliŵeramira. Theka lake amalikoleza m’moto, pamakala oyakawo amawotchapo nyama, amaidya ndipo amakhuta. Ndiponso amadzikongonosa. ‘Aha!’ iye amatero ‘ndakongonoka; ndawona moto panopa!’ Ndi zotsalazo amapanga mulungu wake, fano lake; aliŵeramira nalilambira napemphera kwa ilo. ‘Ndipulumutse,’ iye amatero ‘chifukwa chakuti ndiwe mulungu wanga.’ Sadziŵa chirichonse, samazindikira chirichonse. Maso awo ngwotsekedwa sawona zirizonse, mtima suulingalira chirichonse. Samaganiza konse, alibe chidziŵitso ndi nzeru kuti anene kuti, ‘Ndawotcha theka lake pamoto, ndawotchera mkate pamakala ake oyaka, ndakazinga nyama ndi kuidya, ndipo kodi ndiyenera kupanga chonyansa ndi zotsalazo? Kodi ndiyenera kugwada pamaso pa thabwa?’”
Ezek. 14:6, JB: “Atero Ambuye Yahweh: Bwererani, kusiya mafano [“mafano onyansa,” NW] ndi kuleka machitachita anu onse auve.”
Ezek. 7:20, JB: “Anali kunyadira kukongola kwa majuwelo awo, amene anapanga nawo zifanizo ndi mafano onyansa. Ndicho chifukwa chake ndatsimikiza kukhala chinthu chonyasa [“chauve,” Dy; “chinyalala,” NAB] kwa iwo.”
Kodi tiyenera kulingalira motani ponena za zifanizo zirizonse zimene tingakhale titalemekeza kalero?
Deut. 7:25, 26, JB: “Muyenera kutentha zifanizo zonse zosemedwa za milungu yawo, musasirire golide ndi siliva amene zakutidwa naye; itengeni ndipo mudzagwidwa mu msampha: izi nzonyasa kwa Yahweh Mulungu wanu. Simuyenera kubweretsa chinthu chonyansa m’nyumba mwanu kuwopera kuti inu, mofanana nacho, mungakhalenso otembereredwa. Muyenera kuziwona kukhala zodetsedwa ndi zonyansa [“nyansidwa nachoni kotheratu ndi kuipidwa nacho kwakukulu,” NW].” (Pamene kuli kwakuti anthu a Yehova lerolino sakuvomeredwa kuwononga zifanizo za anthu ena, lamulo loperekedwa kwa Israyeli iri limapereka chitsanzo chonena za mmene ayenera kuwonera zifanizo zirizonse zimene ali nazo zimene angakhale atalemekeza. Yerekezerani ndi Machitidwe 19:19.)
1 Yoh. 5:21, Dy: “Tiana, dzilekanitseni ndi mafano [“milungu yonama,” JB].”
Ezek. 37:23, JB: “Iwo sadzadziipitsanso ndi mafano awo . . . Adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”
Kodi kugwiritsira ntchito zifanizo m’kulambira kungayambukire motani mtsogolo mwathu?
Deut. 4:25, 26, JB: “Ngati muchita modziluluza, mukumapanga chifanizo chosema mu mpangidwe uliwonse [“fano,” Kx; “chofanana nacho chirichonse,” Dy], kuchitira chosakondweretsa Yehova ndi kumkwiyitsa, patsikulo ndidzaitana kumwamba ndi dziko lapansi kuchitira umboni mokutsutsani; . . . mudzawonongedwa kotheratu.” (Lingaliro la Mulungu silinasinthe. Wonani Malaki 3:5, 6.)
1 Akor. 10:14, 20, JB: “Ndicho chifukwa chake, abale anga okondedwa, chimene muyenera kukhalira otalikirana ndi kulambira mafano. . . . Nsembe zimene amapereka amazipereka kwa ziwanda zimene siziri Mulungu. Ndiribe chikhumbo cha kukuwonani mukudyerana ndi ziwanda.”
Chiv. 21:8, JB: “Choloŵa cha amatha, awo amene samasunga mawu awo, kapena olambira zonyasa, ndi cha ambanda ndi adama, ndi owombeza, olambira mafano kapena abodza lamtundu uliwonse, ndiyo imfa yachiŵiri [mawu amtsinde, “imfa yamuyaya”] m’nyanja yamoto wa sulfure.”
Sal. 115:4-8, JB (113:4-8, mpambo wachiŵiri wa manambala, Dy): “Mafano awo, siliva ndi golide, ntchito ya luso la anthu, ali ndi pakamwa, koma samalankhula konse, maso, koma samawona konse, makutu, koma samamva konse, mphuno, koma samanukhiza konse, manja, koma samagwira konse, mapazi, koma samayenda konse, ndipo samatulutsa liwu kuchokera pammero pawo. Owapanga adzafanana nawo, ndipo chotero aliyense amene amawadalira.”