Satana Mdyerekezi
Tanthauzo: Cholengedwa chauzimu chimene chiri mdani wamkulu wa Yehova Mulungu ndi onse amene amalambira Mulungu wowona. Dzinalo Satana linaperekedwa kwa iye chifukwa cha kukhala kwake wotsutsa Yehova. Satana amadziŵikanso monga Mdyerekezi, chifukwa chakuti ndiye woneneza wamkulu wa Mulungu. Satana amalongosoledwa kukhala njoka yoyambilira, mwachiwonekere chifukwa cha kugwiritsira ntchito kwake njoka m’Edene kunyenga Hava, ndipo chifukwa cha chimenechi “chinjoka” chinafikira pa kutanthauza “wonyenga.” M’bukhu la Chivumbulutso, chinjoka cholikwira chophiphiritsira chimatanthauzanso Satana.
Kodi tingadziŵe motani kuti munthu wauzimu wotero alikodi?
Baibulo ndiro magwero aakulu a umboni. Mmenemo watchulidwa mobwerezabwereza ndi dzina (nthaŵi 52, monga Satana, nthaŵi 33 monga Mdyerekezi). Umboni wa mboni yowona ndi maso wonena za kukhalako kwa Satana walembedwanso mmenemo. Kodi ndani amene anali mboni yowona ndi maso? Yesu Kristu, amene anali kumwamba asanadze kudziko lapansi, analankhula mobwerezabwereza za woipa ameneyo mwa kumtchula dzina.—Luka 22:31; 10:18; Mat. 25:41.
Zimene Baibulo limanena ponena za Satana Mdyerekezi nzomveka. Zoipa zimene anthu amakomana nazo ziri zazikulu koposa poyerekezera ndi zoipa za anthu oloŵetsedwamowo. Malongosoledwe a Baibulo a chiyambi cha Satana ndi ntchito zake amamveketsa bwino chifukwa chake, mosasamala kanthu za chikhumbo cha anthu ambiri cha kukhala mu mtendere, chifukwa chake anthu akanthidwa ndi udani, chiwawa, ndi nkhondo m’zaka zikwi zambiri ndi chifukwa chake zimenezi zafika pamlingo wotere kotero kuti tsopano zikuwopseza kuwononga anthu onse.
Ngati kunalibedi Mdyerekezi, kuvomereza zimene Baibulo limanena ponena za iye sikukanabweretsa mapindu osatha kwa munthu. Komabe, m’zochitika zambiri, anthu amene kale anali omwerekera m’kuchita matsenga kapena amene anali m’timagulu togwiritsira ntchito kulankhula ndi mizimu akusimba kuti panthaŵiyo iwo anali opsinjika kwakukulu chifukwa cha kumva “mawu” ochokera kumagwero osawoneka, ali “ogwidwa” ndi mizimu yoposa anthu, ndi zina zotero. Mpumulo weniweni unapezedwa pamene anaphunzira zimene Baibulo limanena ponena za Satana ndi ziŵanda zake, anagwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo wa kuleka machitachita a kukhulupirira mizimu, ndi kufunafuna chithandizo cha Yehova m’pemphero.—Wonani tsamba 190-195, pamutu wakuti “Kulambira Mizimu.”
Kukhulupirira kuti Satana aliko sikumatanthauza kuvomereza lingaliro lakuti iye ali ndi nyanga, mchira wosongoka, ndi foloko yaitali ndi kuti iye amawotcha anthu m’helo wamoto. Baibulo silimapereka malongosoledwe otero a Satana. Chimenecho chiri chithunzi cha malingaliro a ojambula zithunzi amakedzana amene anasonkhezeredwa ndi zithunzi za mulungu wanthanthi za Agiriki wotchedwa Pan ndi Inferno (ng’anjo) lolembedwa ndi wolemba ndakatulo Wachitaliyana Dante Alighieri. Mmalo mwa kuphunzitsa helo wa moto, Baibulo momvekera bwino limanena kuti “akufa sadziŵa kanthu bi.”—Mlal. 9:5.
Kodi Satana mwinamwake ali lingaliro loipa chabe lokhala m’kati mwa anthu?
Yobu 1:6-12 ndi 2:1-7 amasimba za kukambitsirana pakati pa Yehova Mulungu ndi Satana. Ngati Satana anali lingaliro loipa mwa munthu, m’chochitikachi lingaliro loipalo likanakhala mwa Yehova. Koma chimenechi chiri chosagwirizana kotheratu ndi zimene Baibulo limatiuza ponena za Yehova monga Uyo ‘mwa amene mulibe chisalungamo.’ (Sal. 92:15; Chiv. 4:8) Kuli kokondweretsa kuwona kuti malemba a pamanja Achihebri amagwiritsira ntchito liwu lakuti has·Sa·tanʹ (Satanayo) m’zolembedwa za Yobu, kusonyeza kuti wotchulidwayo ndiye wotsutsa wapadera wa Mulungu.—Wonaninso Zekariya 3:1, 2, mawu amtsinde a kope la Malifarensi la NW.
Luka 4:1-13 ikusimba kuti Mdyerekezi anayesayesa kunyenga Yesu kuchita zikhumbo zake. Cholembedwacho chikusimba mawu olankhulidwa ndi Mdyerekezi ndi mayankho operekedwa ndi Yesu. Kodi Yesu pamenepo anali kuyesedwa ndi lingaliro loipa lokhala mwa iyemwini? Lingaliro lotero silimagwirizana ndi malongosoledwe a Baibulo onena za Yesu akuti anali wopanda uchimo. (Aheb. 7:26; 1 Pet. 2:22) Ngakhale kuli kwakuti pa Yohane 6:70 liwu Lachigiriki lakuti di·aʹbo·losʹ likugwiritsiridwa ntchito kulongosola mkhalidwe woipa umene unabuka mwa Yudasi Isikariote, mu Luka 4:3 liwulo ho di·aʹbo·los (Mdyerekeziyo) likugwiritsiridwa ntchito, motero kusonyeza munthu weniweni.
Kodi kusuliza Mdyerekezi kwakhala njira yamachenjera yogwiritsiridwa ntchito kuyesayesa kuzemba thayo kaamba ka mikhalidwe yoipa?
Anthu ena amasuliza Mdyerekezi kaamba ka zimene iwo eni amachita. Mosiyana, Baibulo limasonyeza kuti kaŵirikaŵiri anthu ali ndi liwongo lalikulu la zoipa zimene amakomana nazo, kaya kuchokera kwa anthu ena kapena monga chotulukapo cha khalidwe la iwo eni. (Mlal. 8:9; Agal. 6:7) Komabe, Baibulo silimatisiya tiri osadziŵa za kukhalapo ndi machenjera za mdani woposa munthu amene wadzetsa nsautso yaikulu pa anthu. Limasonyeza mmene tingatulukire mu ulamuliro wake.
Kodi Satana anachokera kuti?
Ntchito zonse za Yehova nzangwiro; iye saali magwero a chisalungamo; chotero sanalenge munthu aliyense woipa. (Deut. 32:4; Sal. 5:4) Uyo amene anakhala Satana anali poyambirira mwana wauzimu wangwiro wa Mulungu. Polankhula kuti Mdyerekezi “sanaime m’chowonadi,” Yesu anasonyeza kuti panthaŵi ina ameneyo anali “m’chowonadi.” (Yoh. 8:44) Koma, monga momwe ziliri ponena za zolengedwa zonse za luntha za Mulungu, mwana wauzimu ameneyu anapatsidwa ufulu wakudzisankhira. Iye anagwiritsira ntchito molakwa ufulu wake wakudzisankhira, analola malingaliro akuzikudza kukula mu mtima mwake, nayamba kulakalaka kulambiridwa kumene kunali kwa Mulungu yekha, ndipo chotero ananyenga Adamu ndi Hava kuti amvere iye mmalo mwakumvera Mulungu. Motero mwa njira yake yakachitidwe anadzipanga kukhala Satana, dzina limene limatanthauza “Mdani.”—Yak. 1:14, 15; wonaninso tsamba 358, pamutu wakuti “Tchimo.”
Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanawononge Satana mwamsanga atangopanduka?
Nkhani zazikulu zinadzutsidwa ndi Satana: (1) Kulungama ndi kuyenera kwa Ufumu wa Yehova. Kodi Yehova anali kumana anthu ufulu umene ukanawonjezera chimwemwe chawo? Kodi luso la anthu la kulamulira zochitika zawo mwachipambano ndi kupitirizabe kwawo kukhala ndi moyo zinadaliradi pakumvera kwawo Mulungu? Kodi Yehova anachita mwachinyengo m’kupereka lamulo limene linafotokoza kuti kusamvera kukatsogolera ku imfa yawo? (Gen. 2:16, 17; 3:3-5) Chotero, kodi Yehova analidi ndi kuyenera kwa kulamulira? (2) Umphumphu wa zolengedwa za luntha kulinga kwa Yehova. Mwa kuchimwa kwa Adamu ndi Hava funso linadzutsidwa lakuti: Kodi atumiki a Yehova anammveradi iye chifukwa cha kumkonda kapena kodi iwo onse akasiya Mulungu ndi kulondola chitsogozo cha Satana? Nkhani yotsirizira imeneyi inakulitsidwa ndi Satana pambuyo pake m’masiku a Yobu. (Gen. 3:6; Yobu 1:8-11; 2:3-5; wonaninso Luka 22:31.) Nkhanizi sizikanathetsedwa kokha mwa kupha opandukawo.
Sichifukwa chakuti Mulungu anafunikira kutsimikizira kanthu kalikonse kwa iyemwini. Koma kuti nkhani zimenezi zisakadodometsenso mtendere ndi ubwino za chilengedwe chonse, Yehova waloleza nthaŵi yokwanira kuti izo zithetsedwe popanda chikaikiro chirichonse. Kuti Adamu ndi Hava anafa chifukwa cha kusamvera Mulungu kunafikira kukhala kwachiwonekere m’nthaŵi yokwanira. (Gen. 5:5) Koma zambiri zinaphatikizidwa. Chotero, Mulungu walola onse aŵiri Satana ndi anthu kuyesa mipangidwe iriyonse ya maboma odzipangira okha. Palibe lirilonse limene ladzetsa chimwemwe chosatha. Mulungu walola anthu kuchita zonse zothekera m’kulondola njira za moyo zimene zimanyalanyaza miyezo Yake yolungama. Zotulukapo zikuzilankhulira zokha. Monga momwe mowonadi Baibulo limanenera kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yer. 10:23) Panthaŵi imodzimodziyo Mulungu wapatsa atumiki ake mwaŵi wa kutsimikizira kukhulupirika kwawo kwa iye mwa ntchito zawo za kumvera kwachikondi, ndipo zimenezi azichita atayang’anizana ndi mayeso ndi chizunzo zosonkhezeredwa ndi Satana. Yehova akulimbikitsa atumiki ake, kumati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miy. 27:11) Awo otsimikizira kukhala okhulupirika amatuta mapindu aakulu patsopano lino ndipo ali ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya mu ungwiro. Iwo adzagwiritsira ntchito moyo woterowo m’kuchita chifuniro cha Yehova, amene umunthu wake ndi njira zake amazikondadi.
Kodi Satana ali munthu wamphamvu motani m’dziko lamakono?
Yesu Kristu ananena za iye kukhala “wolamulira wa dziko,” amene anthu onse amamvera mwa kulabadira zisonkhezero zake za kunyalanyaza malamulo a Mulungu. (Yoh. 14:30, NW; Aef. 2:2) Baibulo limamtchanso “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” amene amatamandidwa ndi zizoloŵezi za anthu amene amamamatira kudongosolo lino la zinthu.—2 Akor. 4:4; 1 Akor. 10:20.
Poyesa kupereka chiyeso kwa Yesu Kristu, Mdyerekezi “anakwera naye, namuwonetsa iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m’kamphindi kakang’ono. Ndipo Mdyerekezi anati kwa iye, Ine ndidzapatsa inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemelero wawo; chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna. Chifukwa chake ngati inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.” (Luka 4:5-7) Chivumbulutso 13:1, 2 chimasonyeza kuti Satana amapereka ‘mphamvu, mpando wachifumu ndi ulamuliro waukulu’ ku dongosolo la ulamuliro wa ndale zadziko padziko lonse. Danieli 10:13, 20 amavumbula kuti Satana wakhala ali ndi akalonga auchiŵanda olamulira pamaufumu aakulu a dziko lapansi. Aefeso 6:12 amasonya kwa ameneŵa kukhala ‘maboma, maulamuliro, olamulira a dziko amdima uno, makamu a mizimu yoipa mmalo akumwamba.’
Mposadabwitsa kuti 1 Yohane 5:19 amati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Koma mphamvu yake iri kokha ya nyengo yochepa ya nthaŵi ndipo iri kokha mwa chilolezo cha Yehova, amene ali Mulungu Wamphamvuyonse.
Kodi Satana adzaloledwa kusocheza anthu kwautali wotani?
Kaamba ka umboni wakuti ife tsopano tiri m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipa la Satana, wonani tsamba 231-234, pamutu wakuti “Madeti,” ndi mutu waukulu wakuti “Masiku Otsiriza.”
Makonzedwe a mpumulo ku chisonkhezero choipa cha Satana afotokozedwa mophiphiritsira motere: “Ndinawona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthaŵi.” (Chiv. 20:1-3) Ndiyeno chiyani? “Mdyerekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure.” (Chiv. 20:10) Kodi uku kutanthauzanji? Chivumbulutso 21:8 chikuyankha: “Ndiyo imfa yachiŵiri.” Adzawonongedwa kosatha!
Kodi ‘kuponyedwa kuphompho’ kwa Satana kumatanthauza kuti adzabindikiritsidwa kudziko lapansi lapululu lopanda munthu aliyense wooti iye anyenge kwa zaka 1 000?
Anthu ena matchula Chivumbulutso 20:3 (chogwidwa mawu pamwambapa) kuchirikiza lingaliro limeneli. Iwo amanena kuti “phompho,” kapena “dzenje lopanda mapeto” (KJ), limaimira dziko lapansi mu mkhalidwe wapululu. Kodi limatero? Chivumbulutso 12:7-9, 12 (KJ) chimasonyeza kuti panthaŵi ina kuikidwa kwake kuphompho kusanachitike Satana “akuponyedwa” kuchokera kumwamba kudza kudziko lapansi, kumene akudzetsa masoka owonjezereka pa anthu. Chotero, pamene Chivumbulutso 20:3 (KJ) chimanena kuti Satana ‘akuponyedwa . . . m’dzenje lopanda mapeto,’ iye ndithudi sakungosiyidwa pamene iye ali kale—wosawoneka koma wobindikiritsidwira kumalo a dziko lapansi. Iye ali kutali ndi kumeneko, “kuti asanyengenso amitundu, kufikira zikatha zaka chikwi.” Tawonani kuti Chivumbulutso 20:3 chimanena kuti, pamapeto a zaka chikwi, ndiye Satana, osati amitundu, amene amasulidwa kuphompho. Pamene Satana amasulidwa, anthu amene kalelo anapanga mitundu imeneyo adzakhala aliko kale.
Yesaya 24:1-6 ndi Yeremiya 4:23-29 (KJ) nthaŵi zina amatchulidwa kuchirikiza chiphunzitso chimenechi. Ameneŵa amati: “Tawonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula . . . dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova ananena mawu ameneŵa.” “Ndinawona dziko lapansi, ndipo tawona linali lopasuka lopanda kanthu . . . ndinawona, ndipo tawona panalibe munthu . . . pakuti Yehova atero dziko lonse lidzakhala bwinja . . . midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu mmenemo.” Kodi nchiyani chimene maulosi ameneŵa amatanthauza? Anali ndi kukwaniritsidwa kwawo koyamba pa Yerusalemu ndi padziko la Yuda. M’kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu, Yehova analola Ababulo kugonjetsa dzikolo. Potsirizira pake linasiyidwa lonse labwinja ndi lapululu. (Wonani Yeremiya 36:29.) Koma Mulungu sanakhalitse labwinja dziko lonse panthaŵiyo, ndiponso iye sadzatero tsopano. (Wonani tsamba 131-133, pamutu wakuti “Dziko Lapansi,” ndiponso mutu waukulu wakuti “Kumwamba.”) Komabe, iye adzapululutsa kotheratu ponse paŵiri mnzake wamakono wa Yerusalemu wosakhulupirika, Dziko Lachikristu, limene limatonza dzina la Mulungu mwa makhalidwe ake oipa, ndi mbali yonse yotsala ya gulu lowoneka la Satana.
Mmalo mwa kukhala lapululu ndi labwinja, mkati mwa Zaka Chikwi za Kulamulira kwa Kristu, ndipo pamene Satana ali chiponyedwere m’mphompho, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. (Wonani “Paradaiso.”)