Mutu 96
Yesu ndi Woweruza Wachichepere Wachuma
PAMENE akudutsa m’chigawo cha Pereya kumka ku Yerusalemu, mnyamata wina akumthamangira ndi kudzagwada pamaso pake. Munthuyo akutchedwa woweruza, mwinamwake kutanthauza kuti iye ali ndi malo antchito otchuka m’sunagoge wamomwemo kapena kuti iye ali chiŵalo cha Sanhedrin. Ndiponso, ngwachuma kwambiri. “Mphunzitsi wabwino,” iye akufunsa motero, “ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
“Unditcha ine wabwino bwanji?” Yesu akuyankha motero. “Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.” Mwachiwonekere mnyamatayo akugwiritsira ntchito “wabwino” monga dzina laulemu, chotero Yesu akumuuza kuti dzina laulemu loterolo liri la Mulungu yekha.
“Koma, ngati,” Yesu akupitiriza motero, “ufuna kuloŵa m’moyo, sunga malamulo.”
“Otani?” munthuyo akufunsa.
Akumatchula asanu a Malamulo Khumi, Yesu akuyankha kuti: “Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza Atate wako ndi amako.” Ndipo akumawonjezera ngakhale lamulo lofunika kwambiri, Yesu akuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.”
“Izi zonse ndizisunga kuyambira ubwana wanga,” munthuyo akuyankha motero ndi kuwona mtima konse. “Ndisoŵanso chiyani?”
Akumamvetsera pempho lalikulu, ndi lowona mtima la munthuyo, Yesu akukopeka naye mtima. Koma Yesu akuzindikira kuphatikizidwa kwa munthuyo kuchuma chakuthupi ndipo motero akumsonyeza chimene afunikira kuchita: “Chinthu chimodzi chikusoŵa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphaŵi, ndipo chuma udzakhala nacho m’mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate ine.”
Yesu akuyang’anitsitsa, mosakayikira ndi chisoni, pamene munthuyo akunyamuka ndi kutembenuka ali wachisoni kwambiri. Chuma chake chamchititsa khungu kuti asawone phindu la chuma chowona. “Okhala nacho chuma,” Yesu akudandaula motero, “adzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvutika nanga!”
Mawu a Yesu akudabwitsa ophunzira. Koma iwo akudabwadi kwambiri pamene iye akupitiriza kutchula lamulo lozoloŵereka kuti: “Pakuti nkwapafupi kwa ngamila apyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kuloŵa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.
“Ndipo angathe kupulumuka ndani?” ophunzirawo akufuna kudziŵa.
Powayang’anitsitsa, Yesu akuyankha kuti: “Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.”
Atawona kuti apanga chosankha chosiyana kwambiri ndi cha woweruza wachichepereyo, Petro akuti: “Wonani, ife tinasiya zonse ndi kutsata inu.” Chotero iye akufunsa kuti: “Nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?”
“M’kubadwanso,” Yesu akulonjeza motero, “pamene Mwana wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemelero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iŵiri, kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” Inde, Yesu akusonyeza kuti padzakhala kulengedwanso kwa mikhalidwe padziko lapansi kotero kuti zinthu zidzakhala monga mmene zinaliri m’munda wa Edene. Ndipo Petro ndi atumwi ena adzalandira mphotho ya kulamulira ndi Kristu padziko lapansi la Paradaiso lino. Ndithudi, mphotho yaikulu yoteroyo njoyenerera kudzimana kulikonse!
Komabe, ngakhale tsopano pali mphotho, monga mmene Yesu akunenera mwamphamvu kuti: “Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi irinkudza, moyo wosatha.”
Monga momwe Yesu akulonjezera, kulikonse m’dziko kumene ophunzira ake amukako, amasangalala ndi unansi wa Akristu anzawo umene uli wathithithi ndi wamtengo wapatali koposa umene umapezedwa m’ziŵalo zabanja lachibadwa. Woweruza wachichepereyo mwachiwonekere akutayikiridwa ndi zonse ziŵiri mphotho imeneyi ndi ija ya moyo wosatha mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu.
Pambuyo pake Yesu akuwonjezera kuti: “Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.” Kodi akutanthauzanji?
Iye akutanthauza kuti anthu ambiri amene ali “oyamba” kulandira mwaŵi wa chipembedzo, monga ngati woweruza wachichepere uja, sadzaloŵa mu Ufumu. Adzakhala “akuthungo.” Koma ambiri, kuphatikizapo ophunzira odzichepetsa a Yesu, amene amanyozedwa ndi Afarisi odzilungamitsa kukhala “akuthungo”—monga anthu a m’fumbi, kapena ‛am ha·’aʹrets—adzakhala “oyamba.” Kukhala kwawo “oyamba” kumatanthauza kuti adzalandira mwaŵi wa kukhala olamulira limodzi ndi Kristu Muufumu. Marko 10:17-31; Mateyu 19:16-30; Luka 18:18-30.
▪ Mwachiwonekere, kodi wachuma wachichepereyo ali wolamulira wamtundu wanji?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akukana kutchedwa wabwino?
▪ Kodi ndimotani mmene chochitika cha woweruza wachichepereyo chimafotokoza mwafanizo upandu wa kukhala wachuma?
▪ Kodi ndimphotho zotani zimene Yesu akulonjeza otsatira ake?
▪ Kodi oyamba akukhala akuthungo, ndipo akuthungo kukhala oyamba motani?