Mutu 109
Yesu Atsutsa Adani Ake
YESU wagonjetsa kotheratu adani ake achipembedzo kotero kuti iwo akuwopa kumfunsa kanthu kena kowonjezereka. Chotero iye akuyamba kuvumbula umbuli wawo. “Muganiza bwanji za Kristu?” iye akufunsa motero. “Ali mwana wa yani?”
“Wa Davide,” Afarisiwo akuyankha.
Ngakhale kuti Yesu sakukana kuti Davide ali kholo lakuthupi la Kristu, kapena Mesiya, iye akufunsa kuti: “Davide mumzimu [pa Salmo 110] amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, Ukhale padzanja lamanja langa, kufikira ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako? Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji?”
Afarisiwo angoti chete, pakuti sakudziŵa amene kwenikweni ali Kristu, kapena wodzozedwayo. Mesiya sali chabe mbadwa ya Davide yaumunthu, monga mmene Afarisiwo mwachiwonekere amakhulupililira, koma anakhalako kumwamba ndipo anali mbuye wa Davide, kapena Ambuye.
Tsopano potembenukira kumakamuwo ndi kwa ophunzira ake, Yesu akuchenjeza za alembi ndi Afarisi. Popeza kuti ameneŵa amaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu, pokhala “akhala pa mpando wa Mose,” Yesu akufulumiza kuti: “Zinthu ziri zonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge.” Koma iye akuwonjezera kuti: “Koma musatsanza ntchito zawo; pakuti amalankhula koma samachita.”
Iwo ali onyenga, ndipo Yesu akuwadzudzula mofanana kwambiri ndi mmene anachitira pamene analinkudya m’nyumba ya Mfarisi wina miyezi ingapo yapitayo. “Amachita ntchito zawo zonse,” iye akutero, “kuti awonekere kwa anthu.” Ndipo iye akupereka zitsanzo, akumati:
“Akulitsa chitando chake cha njirisi zawo.” Zotengeramo malembo zazing’ono zimenezi, zovalidwa pamphumi kapena pamkono, ziri ndi zigawo zinayi za Chilamulo: Eksodo 13:1-10, 11-16; ndi Deuteronomo 6:4-9; 11:13-21. Koma Afarisiwo akuwonjezera ukulu wa zotengera zimenezi kuti apereke lingaliro lakuti iwo ngachangu pa Chilamulo.
Yesu akupitirizabe kunena kuti ‘nakulitsa mphonje za mikanjo yawo.’ Pa Numeri 15:38-40 Aisrayeli akulamulidwa kupanga mpendero pamikanjo yawo, koma Afarisiwo amapangitsa yawo kukhala yaikulu koposa ya wina aliyense. Zonsezi zimachitidwa kuti adziwonetsere! “Nakonda malo aulemu,” Yesu akulengeza motero.
Mwachisoni, ophunzira a iye mwini ayambukiridwa ndi chikhumbo cha kulemekezeka kumeneku. Chotero iye akupereka uphungu wakuti: “Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wakumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.” Ophunzirawo ayenera kudzichotsera chikhumbo cha kukhala nambala wanu! “Koma Wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu,” Yesu akulangiza motero.
Kenako iye akulengeza mpambo wa masoka pa alembi ndi Afarisi, mobwerezabwereza akumawatcha kuti onyenga. Iwo ‘amatsekerezera anthu ufumu wakumwamba,’ iye akutero, ndipo “alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mawu ambiri.”
“Tsoka inu, atsogoleri akhungu,” Yesu akutero. Iye akutsutsa kupanda mkhalidwe wauzimu kwa Afarisi, kowonekera mwa kudzilekanitsa kumene amapanga. Mwachitsanzo, iwo amanena kuti, ‘Sikanthu kwamunthu aliyense kuti alumbire m’dzina la kachisi, koma munthu amakhala ndi mlandu ngati alumbira m’dzina la golidi wa pakachisi.’ Mwa kugogomezera kwawo kwambiri golidi wa pakachisi koposa phindu lauzimu la malo amenewo a kulambira, iwo amavumbula kukhala kwawo akhungu pa makhalidwe abwino.
Pamenepo, monga momwe anachitira poyambilira, Yesu akutsutsa Afarisi kaamba ka kunyalanyaza “zolemera za Chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo ndi chikhulupiliro” pamene akusumika chisamaliro chachikulu pa kupereka chakhumi, kapena gawo la khumi, la timbewu tonunkhira.
Yesu akutcha Afarisiwo kukhala ‘atsogoleri akhungu, akukuntha touluka, koma nameza ngamila!’ Iwo amakuntha kouluka pavinyo wawo osati kokha chifukwa chakuti iko nkachilombo koma chifukwa chakuti nkodetsedwa mwamwambo. Komabe, kunyalanyaza kwawo nkhani zofunika za Chilamulo nkofanana ndi kumeza ngamila, imenenso mwamwambo iri yodetsedwa. Mateyu 22:41–23:24; Marko 12:35-40; Luka 20:41-47; Levitiko 11:4, 21-24.
▪ Kodi nchifukwa ninji Afarisi akhala chete pamene Yesu akuwafunsa za zimene Davide ananena m’Salmo 110?
▪ Kodi nchifukwa ninji Afarisi amakulitsa zotengeramo zawo za Malemba ndi mpendero wa mikanjo yawo?
▪ Kodi Yesu akupereka uphungu wotani kwa ophunzira ake?
▪ Kodi ndikudzilekanitsa kotani kumene Afarisi amapanga, ndipo kodi Yesu akuwatsutsa motani chifukwa cha kunyalanyaza kwawo nkhani zofunika?