Mutu 125
Ululu Pamtengo
PAMODZI ndi Yesu achifwamba aŵiri akutsogozedwa kukaphedwa. Osati kutali ndi mzindawo, gululo likuima pamalo otchedwa Golgota, kapena Malo a Bade.
Andendewo akuvulidwa zovala zawo. Pamenepo vinyo wosanganiza ndi mure akuperekedwa. Mwachiwonekere wakonzedwa ndi akazi a m’Yerusalemu, ndipo Aromawo samakaniza chakumwa chimenechi chakupha ululu kwa odzapachikidwa. Komabe, pamene Yesu alaŵa, akukana kumumwa. Chifukwa ninji? Mwachiwonekere iye akufuna kukhala ndi nzeru zake zonse mkati mwa chiyeso chachikulu chimenechi cha chikhulupiriro chake.
Tsopano Yesu watambalalitsidwa pamtengopo manja ake ataikidwa pamwamba pa mutu wake. Pamene asilikaliwo akukhomera misomali yaikulu kupyoza m’manja ake ndi m’mapazi ake. Iye akudzungunyuka ndi ululu pamene misomaliyo ikuboola mnofu ndi minyewa. Pamene mtengowo ukuimikidwa chiriri, ululuwo ngwosapiririka, pakuti kulemera kwa thupi kukuwonjezera zilonda za m’misomali. Komabe, mmalo mwa kuwopseza, Yesu apempherera asilikali Achiromawo kuti: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.”
Pilato wakhomera pamtengopo chizindikiro chokhala ndi mawu akuti: “Yesu Mnazarayo, Mfumu ya Ayuda.” Mwachiwonekere, iye walemba zimenezi osati kokha chifukwa chakuti akulemekeza Yesu komanso chifukwa chakuti akunyansidwa ndi ansembe Achiyuda kaamba ka kuumiriza chiweruzo cha imfa ya Yesu kwa iye. Kuti onse athe kuŵerenga chizindikirocho, Pilato walemba chizindikirocho m’zinenero zitatu—m’Chihebri, m’Chilatini chaboma, ndi m’Chigiriki cha onse.
Akulu ansembe, kuphatikizapo Kayafa ndi Anasi, akudabwa. Chilengezo chotsimikizirika chimenechi chikuwononga ola lawo lachilakiko. Chotero iwo akutsutsa kuti: “Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti iyeyu anati, Ndiri Mfumu ya Ayuda.” Atakwiya chifukwa cha kutumikira monga chiŵiya cha ansembewo, Pilato akuyankha moipidwa kotheratu kuti: “Chimene ndalemba, ndalemba.”
Tsopano ansembewo, ndi khamu la anthu, akusonkhana pamalo opherawo, ndipo ansembewo akutsutsa umboni wa chizindikirocho. Iwo akubwereza umboni wonama umene unaperekedwa poyambirira pamlanduwo m’Sanhedrin. Chifukwa cha chimenecho, mosadabwitsa oyenda m’njira akuyamba kulankhula molalata, akumagwedeza mitu yawo monyodola namati: “Nanga iwe, wokupasula kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, [tatsika pamtengo wozunzirapo, NW].”
“Anapulumutsa ena sangathe kudzipulumutsa yekha,” akulu ansembe ndi mabwenzi awo achipembedzo akuwadula mawu motero. “Ndiye Mfumu ya Ayuda; atsike tsopano [pamtengo wozunzirapowo, NW], ndipo tidzamkhulupirira iye. Amakhulupirira Mulungu; iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.”
Atayambukiridwa ndi mzimu umenewu, asilikali nawonso akujeda Yesu. Iwo monyodola akumpatsa vinyo wosasa, mwachiwonekere akumuika chapafupi ndi milomo yake youma gwa. “Ngati iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda,” iwo akumtonza motero, “udzipulumutse wekha.” Ngakhale achifwambawo—mmodzi wopachikidwa kulamanja la Yesu, ndipo wina kulamanzere—akumnyodola. Tangoganizani! Munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, inde, amene anakhala ndi phande ndi Yehova Mulungu m’kulenga zinthu zonse, motsimikizirika akuvutika ndi nkhanza yonseyi!
Asilikaliwo akutenga zovala za Yesu nazigaŵa mbali zinayi. Iwo akuchita mayere kuti awone kuti zimenezi zidzakhala za yani. Komabe, chovala chamkati nchopanda msoko, champangidwe wapamwamba koposa. Chotero asilikaliwo akuuzana kuti: “Tisang’ambe aŵa, koma tichite mayere, aŵa akhale a yani.” Motero, mosa- dziŵa, akukwaniritsa lemba limene limati: “Anagaŵana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira mayere.”
M’nthaŵi yokwanira, mmodzi wa achifwambawo akufikira pakuzindikira kuti Yesu ayeneradi kukhala mfumu. Chifukwa chake, akumadzudzula mnzake, iye akuti: “Kodi suwopa Mulungu, powona uli m’kulangika komweku? Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tiri kulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachita kanthu kolakwa.” Pamenepo akulankhula ndi Yesu, mopempha kuti: “Ndikumbukireni mmene muloŵa ufumu wanu.”
‘Indetu, ndinena ndi iwe lerolino,’ Yesu akuyankha motero, “Udzakhala ndine m’Paradaiso.” Lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa pamene Yesu adzalamulira monga Mfumu kumwamba ndi kuukitsira wochita zoipa wolapa ameneyu kumoyo padziko lapansi la Paradaiso amene opulumuka Armagedo ndi atsamwali awo adzakhala ndi mwaŵi wa kulima. Mateyu 27:33-44; Marko 15:22-32; Luka 23:27, 32-43; Yohane 19:17-24.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akukana kumwa vinyo wosanganiza ndi mure?
▪ Mwachiwonekere, kodi nchifukwa ninji, chizindikiro chakhomeredwa pamtengo wa Yesu, ndipo chikupangitsa kukangana kotani pakati pa Pilato ndi akulu ansembe?
▪ Kodi ndinkhanza, yowonjezereka yotani imene Yesu akuchitiridwa pamtengopo, ndipo mwachiwonekere ikusonkhezeredwa ndi chiyani?
▪ Kodi ulosi ukwaniritsidwa motani ndi zimene zikuchitiridwa kuzovala za Yesu?
▪ Kodi ndikusintha kotani kumene wachifwamba mmodzi akupanga, ndipo ndimotani mmene Yesu adzakwaniritsira pempho la munthuyo?