Kuchoka ku Igupto Kupita ku Dziko Lolonjezedwa
ANTHU kulikonse amadziŵa za ulendo wa Aisrayeli wochoka ku Igupto. Koma kodi Mose ndi anthu a Mulungu anakumana ndi zotani atawoloka Nyanja Yofiira? Kodi analoŵera kuti, ndipo anakafika bwanji pa Mtsinje wa Yordano kuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa?
Ulendo wawo unali wa ku Kanani, koma Mose sanatsate njira yaifupi kwambiri, ya makilomita pafupifupi 400 yodutsa kugombe lamchenga, yomwe ikanawadutsitsa m’Filistiya mwenimweni, m’dziko la adani. Komanso iye sanaloŵere pakati pa dera lalikulu la Sinai, komwe nsangalabwi ndi mapiri ake a miyala ya njereza n’zotentha kwambiri. M’malo mwake, Mose analoŵera nawo kum’mwera anthuwo, n’kudutsa nawo mu mkwasa wa kuchigwa kugombe la nyanja. Anamanga msasa woyamba ku Mara, pamene Yehova anasandutsa madzi owawa kukhala okoma.a Atachoka ku Elimu, anthuwo anadandaula pofuna chakudya; Yehova n’kutumiza zinziri ndipo kenako anatumiza mana. Ku Refidimu, nkhani ya madzi inavutanso, Aamaleki omwe anaputa Aisrayeli anagonjetsedwa, ndipo mpongozi wa Mose analangiza Mose kuti amuna anzeru azimuthandiza ntchito.—Eks., machap. 15-18.
Mose kenako anatsogolera Israyeli kumapiri a kum’mwera kwenikweni, n’kukamanga msasa ku Phiri la Sinai. Kumeneko, anthu a Mulungu analandira Chilamulo, anakonza chihema, komanso anapereka nsembe. Chaka chachiŵiri cha ulendowu, iwo anapita kumpoto podzera ‘m’chipululu chachikulu ndi choopsa,’ ulendo wopita kudera la Kadesi (Kadesi Barinea) womwe mwachionekere unatenga masiku 11. (Deut. 1:1, 2, 19; 8:15) Chifukwa chochita mantha ndi nkhani yolakwika imene azondi khumi anabweretsa, anthuwo anayamba kumangoyendayenda zaka 38. (Num. 13:1–14:34) Ena mwa malo omwe anaimako ndi monga ku Abirona ndi ku Ezioni Geberi, kenako anabwerera ku Kadesi.—Num. 33:33-36.
Nthaŵi itakwana tsopano yoti Israyeli apite ku Dziko Lolonjezedwa, Aisrayeliwo sanapite mwachindunji kumpoto. M’malo mwake anazungulira dziko la Edomu n’kuloŵera kumpoto motsata “msewu wachifumu.” (Num. 21:22; Deut. 2:1-8) Kwa mtundu wonsewo, womwe unkayenda ndi ana, ziŵeto, mahema, sunali ulendo wamaseŵera kuyenda mu msewu umenewu. Anadutsa njira yokhotakhota kutsika ndi kukwera zigwembe zoipa kwambiri, m’zigwa monga Zaredi ndi Arinoni (zakuya pafupifupi mamita 520).—Deut. 2:13, 14, 24.
Kenako Aisrayeli anafika pa Phiri la Nebo. Miriamu anali atamwalira ku Kadesi, ndipo Aroni anamwalira pa Phiri la Hori. Koma Mose anamwalirira pamenepa pafupi penipeni ndi dziko lomwe ankalakalaka ataloŵamo. (Deut. 32:48-52; 34:1-5) Yoswa ndiye anapatsidwa udindo wotsogolera Israyeli kuloŵa m’dzikolo, kutsiriza ulendo womwe unayambika zaka 40 m’mbuyomo.—Yos. 1:1-4.
[Mawu a M’munsi]
a Malo ambiri amene anamangapo misasa sakudziŵika bwinobwino kuti anali pati.
[Bokosi patsamba 8]
MABUKU A M’BAIBULO OLEMBEDWA NTHAŴIYI:
Genesis
Eksodo
Levitiko
Numeri
Deuteronomo
Yobu
Masalmo (mbali yake ina)
[Mapu patsamba 9]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Njira Imene Israyeli Anadutsa yotchulidwa m’buku la Ekisodo
Njira Imene Israyeli Anadutsa
A7 IGUPTO
A5 Ramese?
B5 Sukoti?
C5 Etamu?
C5 Pihahiroti
D6 Mara
D6 Elimu
E6 CHIPULULU CHA SINI
E7 Dofika
F8 Refidimu
F8 Phiri la Sinai (Horebe)
F8 CHIPULULU CHA SINAI
F7 Kibiroti Hatava
G7 Hazeroti
G6 Rimon Perezi
G5 Risa
G3 Kadesi
G3 Bene Yaakana
G5 Hori Hagidigadi
H5 Yotibata
H5 Abirona
H6 Ezioni Geberi
G3 Kadesi
G3 CHIPULULU CHA ZINI
H3 Phiri la Hori
H3 Tsalimona
I3 Punoni
I3 Iyebarimu
I2 MOABU
I1 Diboni
I1 Alimoni Diblataimu
H1 Yeriko
[Malo Ena]
A3 GOSENI
A4 Oni
A5 Mofi (Nofi)
B3 Zoani
B3 Tapanesi
C5 Migidoli
D3 SURI
D5 CHIPULULU CHA ETAMU
F5 CHIPULULU CHA PARANA
G1 FILISTIYA
G1 Asidodo
G2 Gaza
G2 Beereseba
G3 Azimoni
G3 NEGEBU
H1 Yerusalemu
H1 Hebroni (Kiriyati Araba)
H2 Aradi (Mkanani)
H4 SEIRI
H4 EDOMU
I7 MIDYANI
Njira Zazikulu
Njira ya Dziko la Afilisti
Njira ya ku Suri
I4 Msewu Wachifumu
Njira ya Apaulendo
Njira ya El Haj
[Mapiri]
F8 Phiri la Sinai (Horebe)
H3 Phiri la Hori
I1 Phiri la Nebo
[Nyanja]
E2 Mediterranean (Nyanja Yaikulu)
D7/G7 Nyanja Yofiira
I1 Nyanja Yamchere
[Mitsinje]
A6 Mtsinje wa Nile
F3 C. cha Igupto
I2 Arinoni
I3 Zaredi
[Chithunzi patsamba 8]
Apaulendo ankadutsa m’kati mwa dera la Sinai
[Chithunzi patsamba 8]
AIsrayeli anamanga msasa pafupi ndi Phiri la Sinai
[Chithunzi patsamba 9]
Anapeza madzi pa akasupe ku Kadesi kapena m’madera a kufupi
[Chithunzi patsamba 9]
Aisrayeli onse anawoloka chigwa cha Arinoni