GAWO 4
Yembekezerani Tsiku la Yehova Mosangalala
Yehova anatumiza aneneri ake kuti achenjeze anthu za tsiku lake lamkwiyo limene likubweralo. Komabe, tisaganize kuti iye ndi Mulungu waukali. Iye ‘amafuula mosangalala chifukwa chokondwera’ ndi anthu ake. Pamene tikuyembekezera tsiku lake lalikulu, tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa ‘kusangalala ndiponso kukondwera ndi mtima wonse.’ (Zefaniya 3:14, 17) Kodi mungatani kuti musonyeze zimenezi pa zochita zanu komanso zimene mumaganiza? Ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kuthokoza Mulungu mukaganizira mfundo zimene mwaphunzira m’mabuku 12 a aneneri?