PHUNZIRO 8
Yosiya Anali ndi Anzake Abwino
Kodi ukuganiza kuti kuchita zinthu zabwino n’kovuta?— Anthu ambiri amaganiza choncho. Baibulo limatiuza kuti zinali zovuta kwambiri kwa mnyamata wina, dzina lake Yosiya, kuti achite zinthu zabwino. Koma anali ndi anzake abwino amene anamuthandiza. Tiye tikambirane za Yosiya ndi anzakewo.
Abambo ake a Yosiya anali Amoni ndipo anali mfumu ya Yuda. Amoni anali munthu woipa kwambiri ndipo ankalambira mafano. Atamwalira, Yosiya anakhala mfumu ya Yuda. Koma pa nthawiyi n’kuti Yosiya ali ndi zaka 8 zokha. Kodi ukuganiza kuti nayenso anali woipa ngati bambo ake?— Ayi, sanali woipa.
Kuyambira ali mwana, Yosiya ankafuna kumvera Yehova. Choncho ankacheza ndi anthu okhawo amene ankakonda Yehova. Anthu amenewa anathandiza Yosiya kuti azichita zinthu zabwino. Kodi anzake ena a Yosiya anali ndani?
Mnzake wina anali Zefaniya. Zefaniya anali mneneri amene anachenjeza anthu a ku Yuda kuti adzakumana ndi zinthu zoopsa ngati angamalambire mafano. Yosiya anamvera Zefaniya ndipo ankalambira Yehova, osati mafano.
Mnzake wina wa Yosiya anali Yeremiya. Anali wofanana naye msinkhu ndipo ankakhala moyandikana komanso anakulira limodzi. Ankagwirizana kwambiri moti Yosiya atamwalira, Yeremiya analemba nyimbo yosonyeza kuti ankamusowa kwambiri Yosiya. Yeremiya ndi Yosiya ankathandizana kuti onse azilambira Yehova komanso kuti azichita zinthu zabwino.
Yosiya ndi Yeremiya ankathandizana kuti onse azichita zinthu zabwino
Kodi waphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yosiya?— Kuyambira ali wamng’ono, Yosiya ankafuna kuchita zabwino. Ankadziwa kuti ayenera kumacheza ndi anthu amene amakonda Yehova. Nawenso uzionetsetsa kuti ukucheza ndi anthu amene amakonda Yehova ndiponso amene angakuthandize kuti uzichita zinthu zabwino.