MUTU 12
Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankabatizidwa
MATEYU 3:13-17 MALIKO 1:9-11 LUKA 3:21, 22 YOHANE 1:32-34
YESU ANABATIZIDWA KENAKO N’KUDZOZEDWA
YEHOVA ANALENGEZA KUTI YESU NDI MWANA WAKE
Patangotha miyezi 6 kuchokera pamene Yohane M’batizi anayamba ntchito yolalikira, Yesu yemwe pa nthawiyi anali ndi zaka pafupifupi 30 anapita ku mtsinje wa Yorodano komwe Yohane ankabatizira anthu. Kodi Yesu ankakatani kumeneko? Sikuti anangopita kuti akacheze ndi Yohane kapena kuti akaone mmene ntchito ya Yohane ikuyendera. Yesu anapita kuti Yohane akamubatize.
Poyamba Yohane anakana kubatiza Yesu ndipo zimenezi n’zomveka. Iye anati: “Ine ndiye wofunika kubatizidwa ndi inu, nanga inu mukubweranso kwa ine kodi?” (Mateyu 3:14) Yohane ankadziwa kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu wapadera. Kumbukirani kuti Mariya atapita kunyumba kwa Elizabeti, Yohane anadumpha akadali m’mimba mwa mayi ake. Elizabeti ayenera kuti anauza Yohane za nkhani imeneyi. N’kuthekanso kuti Yohane anadziwa za mngelo amene ananena za kubadwa kwa Yesu komanso za angelo amene anaonekera kwa abusa usiku umene Yesu anabadwa.
Yohane ankadziwanso kuti ankabatiza anthu amene alapa machimo. Koma Yesu analibe tchimo lililonse. Ngakhale kuti Yohane anakana, Yesu anamuuza kuti: “Pa nthawi ino lola kuti zikhale choncho, chifukwa n’koyenera kwa ife kutero kuti tikwaniritse chilungamo chonse.”—Mateyu 3:15.
Ndiyeno n’chifukwa chiyani Yesu anafunika kuti abatizidwe? Sikuti Yesu ankabatizidwa posonyeza kuti walapa machimo, koma anabatizidwa pofuna kusonyeza kuti akudzipereka kuti achite chifuniro cha Atate wake. (Aheberi 10:5-7) M’mbuyo monsemu, Yesu ankagwira ntchito ya ukalipentala koma tsopano inali nthawi yoti ayambe ntchito imene Atate wake wakumwamba anamutumizira kuti adzagwire padziko lapansi. Kodi Yohane ankadziwa kuti chinachake chichitika pobatiza Yesu?
Patapita nthawi Yohane analemba kuti: “Amene anandituma kudzabatiza m’madzi anandiuza kuti: ‘Ukadzaona mzimu ukutsika ndi kukhazikika pa munthu wina, ameneyo ndiye wobatiza ndi mzimu woyera.’” (Yohane 1:33) Choncho, Yohane ankayembekezera kuti mzimu wa Mulungu udzafika pa winawake amene iyeyo adzamubatize. Mpake kuti pamene Yesu ankavuuka m’madzi, Yohane sanadabwe kuona “mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzatera [pamutu pa Yesu].”—Mateyu 3:16.
Koma si zokhazi zomwe zinachitika. ‘Kumwamba kunamutsegukira.’ Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti pa nthawi imene Yesu ankabatizidwa anayambanso kukumbukira zonse zimene zinkachitika pa nthawi imene anali kumwamba. Yesu anakumbukira moyo wake monga mwana wauzimu wa Yehova, kuphatikizapo mfundo za choonadi zimene anamuphunzitsa ali kumwambako.
Komanso pamene Yesu ankabatizidwa, kumwamba kunamveka mawu akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mateyu 3:17) Kodi mawu amenewa anali a ndani? Sakanakhala mawu a Yesu chifukwa Yesu anali pomwepo ndi Yohane. Choncho mawuwo anali a Mulungu. Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, osati Mulungu.
Apa n’zoonekeratu kuti Yesu anali mwana wa Mulungu amene anabadwa monga munthu ngati mmene munthu woyamba Adamu analili. Atafotokoza zimene zinachitika pamene Yesu ankabatizidwa, Luka analemba kuti: “Pamene Yesu anayamba ntchito yake, anali ndi zaka pafupifupi 30. Anthu ankakhulupirira kuti Yesu anali mwana wa Yosefe, mwana wa Heli, . . . mwana wa Davide, . . . mwana wa Abulahamu, . . . mwana wa Nowa, . . . mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.”—Luka 3:23-38.
Mofanana ndi Adamu, Yesu anali munthu komanso “mwana wa Mulungu.” Pamene Yesu ankabatizidwa, anayamba ubale watsopano ndi Mulungu ndipo anakhala mwana wauzimu wa Mulungu. Choncho Yesu akanatha kuphunzitsa anthu choonadi chonena za Mulungu komanso kuwathandiza kudziwa zoyenera kuchita kuti adzapeze moyo wosatha. Pa nthawi imeneyi, Yesu anadzipereka kuti achite zofuna za Mulungu zomwe pamapeto pake zinachititsa kuti apereke moyo wake waumunthu monga nsembe m’malo mwa anthu ochimwa.