MUTU 44
Yesu Analetsa Mphepo Yamphamvu Panyanja
MATEYU 8:18, 23-27 MALIKO 4:35–5:1 LUKA 8:22-25
YESU ANALETSA MPHEPO NDI MAFUNDE AMPHAMVU PANYANJA YA GALILEYA
Yesu anali atachita zinthu zambiri ndipo ayenera kuti anali atatopa. Koma pamene kunja kunkada Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”—Maliko 4:35.
Kum’mawa kwa nyanja ya Galileya kunali dera lina lomwe linkatchedwa kuti Agerasa. Derali linali m’chigawo cha Dekapole. Ku mizinda ya m’chigawo cha Dekapole ndi kumene kunali kuchimake kwa chipembedzo komanso chikhalidwe cha Agiriki, ngakhale kuti Ayuda ambiri ankakhalanso m’mizinda imeneyi.
Pamene Yesu ankachoka ku Kaperenao kupita ku Dekapole, anthu ambiri anadziwa kuti wachoka. Pamene ankawoloka panyanjayo n’kuti palinso maboti ena omwe ankalowera kutsidya lina. (Maliko 4:36) Ndipotu kuchoka kutsidya lina la nyanjayo kupitanso kutsidya lina si unali ulendo wautali. Nyanja ya Galileya inali nyanja yaikulu yokhala ndi madzi opanda mchere. Nyanjayi inali ya makilomita pafupifupi 21 m’litali ndi makilomita pafupifupi 12 m’lifupi. Komabe m’malo ena nyanjayi inali yozama.
Ngakhale kuti Yesu anali munthu wangwiro, pa nthawiyi anali atatopa kwambiri chifukwa cha ntchito yolalikira imene anagwira. Choncho atangonyamuka ulendowu Yesu anagona kumbuyo kwa botilo atatsamiritsa mutu wake papilo.
Ngakhale kuti atumwi ambiri a Yesu ankadziwa bwino kuyendetsa boti, koma pa ulendowu anavutika kwambiri. Nyanja ya Galileya inazunguliridwa ndi mapiri ndipo chifukwa cha zimenezi nthawi zambiri madzi apamwamba a m’nyanjayi ankakhala otentha. Nthawi zina mphepo yozizira yochoka m’mapiri ikatsika m’munsi n’kukumana ndi madzi otentha a panyanjayi, pankachitika chimphepo ndi mafunde amphamvu. Ndipo izi ndi zimene zinachitikanso pamene Yesu ndi atumwi ake ankawoloka nyanjayi. Mafunde anayamba kuwomba botilo ndipo “madzi anayamba kudzaza m’ngalawamo moti akanatha kumira.” (Luka 8:23) Pamene zonsezi zinkachitika n’kuti Yesu ali m’tulo.
Ngakhale kuti m’mbuyomu atumwiwo anali atakumanapo ndi mphepo komanso mafunde amphamvu panyanja, paulendowu anayesetsa kuwongolera botilo koma zinakanika. Chifukwa cha mantha anadzutsa Yesu kwinaku akukuwa kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” (Mateyu 8:25) Ophunzirawo ankaona ngati akhoza kumira.
Yesu atadzuka anawauza kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?” (Mateyu 8:26) Kenako Yesu analamula mphepo komanso nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” (Maliko 4:39) Nthawi yomweyo chimphepo komanso mafunde amphamvu aja zinakhaladi bata. (Maliko ndi Luka analemba za nkhani yochititsa chidwiyi koma anayamba n’kufotokoza kuti Yesu analetsa mphepo yamphamvuyo mozizwitsa kenako anadzatchula zoti ophunzirawo anali ndi chikhulupiriro chochepa.)
Tangoganizani mmene ophunzirawo anamvera ataona zimenezi. Anaona nyanja yomwe poyamba panali chimphepo komanso mafunde amphamvu itakhala bata. Zimenezi zinawachititsa mantha kwambiri moti anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani kwenikweni, chifukwa ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera?” Kenako anafika bwinobwino kutsidya lina la nyanjayo. (Maliko 4:41–5:1) N’kuthekanso kuti mphepoyi itasiya maboti ena amene anali panyanjayo anabwerera bwinobwino kumadera a kumadzulo a nyanjayo.
Kunena zoona n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mwana wa Mulungu ali ndi mphamvu zolamulira zinthu za m’chilengedwe. Choncho Yesu akadzayamba kulamulira dziko lapansili monga Mfumu, anthu onse adzakhala otetezeka chifukwa sipadzakhalanso masoka a chilengedwe.