MUTU 75
Yesu Ananena Zimene Zimachititsa Munthu Kukhala Wodala
ANATULUTSA ZIWANDA NDI “CHALA CHA MULUNGU”
ZIMENE ZIMACHITITSA MUNTHU KUKHALA WODALA
Yesu atanenanso malangizo okhudza nkhani ya pemphero, panabukanso nkhani zina zomwe anali ataphunzitsapo kale m’mbuyomo pa nthawi imene ankalalikira. Pamene Yesu ankachita zozizwitsa ku Galileya, anthu anamuimba milandu yoti ankachita zozizwitsazo pogwiritsa ntchito mphamvu yochokera kwa wolamulira ziwanda. Ndiyeno Yesu atafika ku Yudeya anthu anamuimbanso mlandu wochita zozizwitsa ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.
Anthu anadabwa kwambiri Yesu atatulutsa chiwanda chimene chinkalepheretsa munthu wina kulankhula. Koma zimenezi sizinasangalatse anthu amene ankadana naye, moti anayambanso kumuimba milandu yabodza. Iwo anati: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule wolamulira wa ziwanda.” (Luka 11:15) Ndiyeno anthu enanso omwe ankafuna kudziwa kuti Yesu ndi ndani, anamupempha kuti awaonetse chizindikiro chakumwamba.
Yesu atazindikira kuti akungofuna kumuyesa, anawayankha ngati mmene anachitiranso ndi anthu amene anakumana nawo ku Galileya. Iye ananena kuti ufumu uliwonse wogawanika pakati umatha. Iye anafotokoza kuti: “Ngati Satana wagawanika, ufumu wake ungalimbe bwanji?” Kenako Yesu anawauza kuti: “Koma ngati ziwandazo ndikuzitulutsa ndi chala cha Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wakufikiranidi modzidzimutsa.”—Luka 11:18-20.
Pamene Yesu ananena kuti “chala cha Mulungu,” n’kutheka kuti anthuwo anakumbukira zimene zinachitika kalekale m’nthawi ya Aisiraeli. Anthu amene anaona Mose akuchita zozizwitsa m’bwalo la Farao anafuula kuti: “Chimenechi ndi chala cha Mulungu!” Komanso “chala cha Mulungu” ndi chimene chinalemba Malamulo Khumi omwe analembedwa pamiyala iwiri. (Ekisodo 8:19; 31:18) Mofanana ndi zimenezi, “chala cha Mulungu,” womwe ndi mzimu woyera kapena kuti mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu ndi umenenso unkathandiza Yesu kuti azitulutsa ziwanda komanso kuchiritsa odwala. Choncho Ufumu wa Mulungu unali utawafikiradi modzidzimutsa anthuwo chifukwa Yesu amene analonjezedwa kudzakhala Mfumu anali pakati pawo n’kumachita zozizwitsa.
Yesu anasonyeza kuti anali ndi mphamvu zoposa za Satana chifukwa ankakwanitsa kutulutsa ziwanda. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene munthu wamphamvu amene akufuna kulanda katundu wa m’nyumba ya mfumu amachita. Munthuyo amayamba wagonjetsa kaye mlonda wamphamvu wokhala ndi zida. Yesu anafotokozanso za fanizo lonena zimene zimachitika mzimu woipa ukatuluka mwa munthu. Ngati munthuyo sangaikemo zinthu zabwino, mzimuwo umabwereranso ndi mizimu ina 7 ndipo zimenezi zimachititsa munthuyo kukhala woipa kwambiri kuposa mmene analili poyamba. (Mateyu 12:22, 25-29, 43-45) Izi ndi zimene zinachitika ndi mtundu wa Aisiraeli.
Mzimayi wina amene ankamvetsera Yesu akulankhula pa nthawiyi anafuula kuti: “Ndi wodala mayi amene mimba yake inanyamula inu ndiponso amene munayamwa mabere ake!” Azimayi achiyuda ankafunitsitsa atakhala ndi mwana woti adzakhale mneneri komanso ankafunitsitsa atakhala mayi a Mesiya. Choncho mayiyu ayenera kuti ankaganiza kuti Mariya ndi wodala kwambiri chifukwa chobereka Yesu amene anali mphunzitsi waluso kwambiri. Koma Yesu anathandiza mayiyo kudziwa chimene chimachititsa munthu kukhaladi wosangalala kapena kuti wodala. Anauza mayiyo kuti: “Ayi, m’malomwake, Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!” (Luka 11:27, 28) Yesu sananenepo kuti Mariya ankafunika kupatsidwa ulemu wapadera. Choncho munthu amakhala wodala kapena kuti wosangalala ngati amatumikira Mulungu mokhulupirika osati chifukwa cha zinthu zimene wakwanitsa kuchita kapena chifukwa chokhala pa ubale ndi munthu wina.
Yesu anadzudzulanso anthuwo ngati mmene anachitira ndi anthu a ku Galileya chifukwa chomupempha kuti awaonetse chizindikiro chakumwamba. Iye anawauza kuti sadzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo “chizindikiro cha Yona.” Zimene zinachitika pamoyo wa Yona zinakhala ngati chizindikiro chifukwa Yona anakhala m’mimba mwa nsomba kwa masiku atatu komanso chifukwa analalikira molimba mtima, zomwe zinachititsa kuti anthu a ku Nineve alape. Ndiyeno Yesu anati: “Koma tsopano wina woposa Yona ali pano.” (Luka 11:29-32) Yesu analinso woposa Solomo yemwe mfumukazi ya ku Seba inabwera kuti idzamve za nzeru zake.
Ndiyeno Yesu ananenanso kuti: “Munthu akayatsa nyale saiika m’chipinda cha pansi kapena kuivundikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale, kuti onse olowa aone kuwala.” (Luka 11:33) N’kutheka kuti Yesu ankatanthauza kuti zimene ankachita pophunzitsa anthu komanso pochita zozizwitsa anthuwo akuona, zinali ngati akubisa kuwala kwa nyale. Zinali choncho chifukwa anthuwo sankafuna kuona kuwalako, zomwe zinawachititsa kuti asamvetse tanthauzo la zimene Yesuyo ankachita.
Pa nthawiyi Yesu anali atangotulutsa kumene chiwanda chimene chinkalepheretsa munthu wina kulankhula. Zimenezi zikanachititsa anthu azilemekeza komanso kuuza ena zimene Yehovayo ankachita kudzera mwa Yesu. Chifukwa cha zimenezi Yesu anachenjeza anthu amene ankamuimba milanduwo kuti: “Chotero khala tcheru. Mwina kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima. Choncho ngati thupi lako lonse lili lowala kwambiri, popanda mbali ina yamdima, thupi lonse lidzawala kwambiri ngati mmene nyale imachitira pokuunikira ndi kuwala kwake.”—Luka 11:35, 36.