MUTU 101
Yesu Anakadya Chakudya ku Nyumba kwa Simoni ku Betaniya
MATEYU 26:6-13 MALIKO 14:3-9 YOHANE 11:55–12:11
YESU ANAPITANSO KU BETANIYA KUFUPI NDI KU YERUSALEMU
MARIYA ANATHIRA YESU MAFUTA ONUNKHIRA
Yesu atachoka ku Yeriko analowera ku Betaniya. Ulendo wochoka ku Yeriko kupita ku Betaniya unali wa makilomita 20 ndipo unali wovuta kwambiri chifukwa ankakwera zitunda. Lazaro ndi azichemwali ake awiri ankakhala m’mudzi wa Betaniya, womwe unali pamtunda wa makilomita pafupifupi atatu kuchokera ku Yerusalemu. Mudziwu unali chakum’mawa m’mphepete mwa phiri la Maolivi.
Ayuda ambiri anafika mofulumira ku Yerusalemu kuti akakhale nawo pa mwambo wa Pasika. Iwo anafika mofulumira “kuti akachite mwambo wa kudziyeretsa.” Ayudawo ankadziyeretsa ngati akhudza mtembo wa munthu kapena ngati achita chinachake chomwe chikanawachititsa kukhala odetsedwa. (Yohane 11:55; Numeri 9:6-10) Ena mwa anthu amene anafika mofulumirawa anasonkhana kukachisi. Anthuwa ankakambirana ngati Yesu abwere ku mwambo wa Pasika.—Yohane 11:56.
Anthu ambiri ankasiyana maganizo pa nkhani ya Yesu. Atsogoleri ena achipembedzo ankafuna kugwira Yesu kuti amuphe moti anauza anthu kuti aliyense amene angadziwe kumene Yesu ali, akawauze kuti “iwo akamugwire.” (Yohane 11:57) Atsogoleriwa ankafunanso kupha Yesu ataukitsa Lazaro. (Yohane 11:49-53) Chifukwa cha zimenezi anthu ena ankakayikira zoti Yesu abwera ku mwambowo.
Yesu anafika ku Betaniya Lachisanu, “kutangotsala masiku 6 kuti Pasika ayambike.” (Yohane 12:1) Popeza kuti tsiku linkayamba dzuwa likalowa ndiye kuti Yesu anafika ku Yerusalemu tsiku la Sabata la pa Nisani 8 lisanayambe. Yesu sakanachoka ku Yeriko pa tsiku la Sabata (kutanthauza kuti sakanachoka ku Yeriko Lachisanu madzulo n’kukafika ku Yerusalemu Loweruka madzulo) chifukwa chilamulo cha Ayuda sichinkalola munthu kuyenda pa tsiku la Sabata. N’kutheka kuti Yesu atafika ku Betaniya anapita ku nyumba kwa Lazaro ngati mmene ankachitira m’mbuyomo.
Simoni, yemwe ankakhalanso ku Betaniya, anaitana Yesu ndi ophunzira ake komanso Lazaro kuti akadye nawo chakudya Loweruka madzulo. Simoni ankadziwikanso kuti “wakhate” mwina chifukwa chakuti poyamba ankadwala khate ndipo Yesu anamuchiritsa. Chifukwa chakuti Marita ankakonda kugwira ntchito zapakhomo, anayamba kusamalira alendowo. Koma Mariya ankamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo pa nthawiyi anachita zinthu zina zimene zinayambitsa mkangano.
Mariya anatsegula botolo la alabasitala lomwe munali “mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado weniweni” ndipo anali “okwana magalamu 327.” (Yohane 12:3) Mafuta amenewa anali odula kwambiri moti ankagulitsidwa pa mtengo wa madinari 300. Ndalama zimenezi zinali zokwana malipiro a chaka chonse. Mariya anathira mafutawa pamutu komanso m’mapazi a Yesu ndipo ankapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake. Kafungo konunkhira ka mafutawo kanadzaza m’nyumba yonseyo.
Ophunzira a Yesu anakwiya kwambiri ndipo anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani akuwononga chonchi mafuta onunkhirawa?” (Maliko 14:4) Yudasi Isikariyoti sanagwirizane ndi zimene Mariya anachita chifukwa ananena kuti: “N’chifukwa chiyani mafuta onunkhirawa sanagulitsidwe madinari 300 ndi kupereka ndalamazo kwa anthu osauka?” (Yohane 12:5) Sikuti Yudasi ananena zimenezi chifukwa chakuti ankaganiziradi anthu osauka. Yudasi ankasunga bokosi la ndalama zimene ophunzira ankazigwiritsa ntchito ndipo ankaba ndalama za m’bokosilo.
Yesu anaikira kumbuyo Mariya ponena kuti: “N’chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino. Osaukawo muli nawo nthawi zonse, koma ine simudzakhala nane nthawi zonse. Pakuti pamene mayiyu wathira mafuta onunkhirawa pathupi langa chonchi, wachita zimenezi kukonzekera kuikidwa kwanga m’manda. Ndithu ndikukuuzani, Kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwe m’dziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzam’kumbukira.”—Mateyu 26:10-13.
Yesu anali atakhala ku Betaniya kwa pafupifupi masiku awiri ndipo anthu ambiri anadziwa zoti ali kumeneko. Ayuda ambiri ankapita kunyumba kwa Simoni kuti akaone Yesu komanso kuti akaone Lazaro “amene [Yesu] anamuukitsa kwa akufa.” (Yohane 12:9) Ndiyeno ansembe aakulu anakambirana zoti aphe Yesu komanso Lazaro. Atsogoleri achipembedzowa ankaona kuti anthu ambiri ankakhulupirira Yesu chifukwa chakuti Lazaro anali ataukitsidwa. Kunena zoona, atsogoleri achipembedzo amenewa anali oipa mtima kwambiri.