NYIMBO 41
Imvani Pemphero Langa
Losindikizidwa
1. Atate mumve pempheroli.
M’lungu wanga ine ndi wanu.
Ndidzatamanda dzina lanu.
(KOLASI)
Yehova mumve pempheroli.
2. Ndathokoza mphatso ya moyo.
Mumandisamalira ndithu.
Mumandithandiza mu zonse.
(KOLASI)
Yehova mumve pempheroli.
3. Ndizichita zinthu zabwino.
Ndiyende mukuwala kwanu.
Ndipirire mavuto onse.
(KOLASI)
Yehova mumve pempheroli.
(Onaninso Eks. 22:27; Sal. 106:4; Yak. 5:11.)