NYIMBO 129
Tipitirizebe Kupirira
Losindikizidwa
1. Tizipirira
Mayesero ngati Yesu.
Anavutika
Koma ankasangalala
Ndi chiyembekezo.
Analimba mtima.
(KOLASI)
Tikhale opirira.
Tizilalikira.
M’lungu amatikonda
Adzatithandiza kupirira.
2. Tingakumane
Ndi mavuto ochuluka,
Tidikirebe
Moyo wosatha m’tsogolo.
Tikulakalaka
Mtendere wosatha.
(KOLASI)
Tikhale opirira.
Tizilalikira.
M’lungu amatikonda
Adzatithandiza kupirira.
3. Sitimaopa
Kapena kukayikira.
Titumikire
Mpaka tsiku lomaliza.
Tsiku la Yehova
Lilidi pafupi.
(KOLASI)
Tikhale opirira.
Tizilalikira.
M’lungu amatikonda
Adzatithandiza kupirira.
(Onaninso Mac. 20:19, 20; Yak. 1:12; 1 Pet. 4:12-14.)