PHUNZIRO 19
Kuwafika Pamtima Anthu
MMENE MUNGACHITIRE:
Muzithandiza anthu kuti azidzifufuza. Muzifunsa mafunso othandiza anthu kudzifufuza mumtima.
Muzithandiza anthu kukhala ndi zolinga zabwino. Thandizani anthu kudzifufuza kuti adziwe chifukwa chimene amachitira zinthu zabwino. Athandizeni kuti azichita zinthu chifukwa chokonda Yehova, anzawo komanso Mawu a Mulungu. Muzikambirana ndi anthu osati kuwauza zochita. Nkhani yanu ikamatha, anthu azikhala atalimbikitsidwa osati atachititsidwa manyazi. Azifunitsitsa kuchita zonse zimene angathe.
Muzithandiza anthu kuganizira za Yehova. Nkhani yanu izithandiza anthu kuona kuti malamulo komanso mfundo za m’Baibulo zimasonyeza makhalidwe a Yehova monga chikondi. Muzithandiza anthu kudziwa kuti zochita zawo zimakhudza Yehova ndipo azifunitsitsa kumusangalatsa.