Kuthawa kwa Akristu Kupita ku Pella
MU 33 C.E., Yesu Kristu anapereka chenjezo kwa otsatira ake “kuyamba kuthawira ku mapiri” pamene anaona “Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo.” (Luka 21:20-24) Koma kodi nkuti kumene iwo kweni kweni anathawira? Wophunzira wa zakummawa ndi mbiri zakale wa Chifrechi Joseph Ernest Renan akuyankha: “Malo osankhidwa ndi oyang’anira a mbumba za [Chikristu] kutumikira monga malo a akulu osungira anthu osowa thandizo a Tchalitchi chozembera anali Pella, umodzi wa mizinda ya Decapolis, womangidwa pafupi ndi gombe la kumanzere kwa Yordani pamalo okhumbirika, kuyang’ana ku mbali imodzi ya chigwa cha Ghoro, yokhala kumbali ina therezi lozyolika koposa pandomo pake pomwe pamapita madzi othamanga mwamphamvu. Panalibe kusankha kwa nzeru komwe kukanachitidwa. Yudeya, Idumeya, Pereya ndi Galileya anali mkuphinduka; Samaria ndi ku doko zinali mu mkhalidwe wosakhalika . . . Motero Sikutopolisi ndi Pella inali mizinda yachete yapafupi ndi Yerusalemu. Pella, kaamba ka malo ache apatsidya pa Yordani, akanayenera kupereka bata lokulira kupambana Sikutopolisi, yemwe anakhala mmodzi wa linga la Aroma. Pella anali mzinda wa ufulu monga mizinda ina ya Decapolisi . . . Kupeza pothawira kumeneko kunali kudziwulula mwapoyera mwa mantha kuchipanduko cha [ChiYuda] . . . Munali mu mzinda uwu wokana-ChiYuda komwe Tchalitchi la Yerusalemu linapeza pothawirapo m’nthawi ya ziopsezo za kuzingidwa.”