“Kusakaza Kochitidwa Kudzakhala Kwakukulu Kwambiri”
NKHONDO YADZIKO 1 inatenga mbali yaikulu ya miyoyo ya anthu ndi katundu. Kodziwika bwino pang’ono, ngakhale kuli tero, kuli kusakaza kumene nkhondo inachita ku chithunzi cha amishonale a Dziko la Chipembedzo mu Africa. Malinga ndi mishonale wa Chikatolika Francis Schimlek mu bukhu lake Medicine Versus Witchcraft, mbiri ya kusakaza kwa dziko lonse kumeneku “kunali monga chivomezi, kunjenjemera kwake kumene kunamveka kufikira ku mishoni yomalizira ya mu Africa ku nkhalango. . . . Athenga a Kristu anachititsidwa manyazi, ndipo Akristu Akuda anazizwitsidwa.”
Nchifukwa ninji chiri tero? Schimlek akugwira mawu mishonale Albert Schweitzer pamene akulongosola: “Ife tiri, tonse a ife, ozindikira kuti Anthu Akuda ambiri akuzizwa kwambiri ponena za funso lakuti kodi chingakhale chotheka motani kuti azungu, amene anabweretsa Uthenga Wabwino wa Chikondi, tsopano akuphana wina ndi mnzake, ndi kumataya malamulo a Ambuye Yesu. Pamene iwo afunsa funsoli kwa ife timakhala opanda thandizo. . . . Ndikuwopa kuti kusakaza kochitidwa kudzakhala kwakukulu kwambiri