Nyimbo Zomwe Zimachiritsa
Mayi wachichepere wa ku Iowa, U.S.A., akulongosola kuti: “Ndiyenera kulemba kukuuzani ndi mokulira chotani mmene matepi anu a [piano] a ‘Sing Praises to Jehovah’ amatanthauza kwa ine ndi banja langa. Tsiku lirilonse, ndimasisita mwana wanga wa zaka zitatu kuti agone. Koma choyamba timaikapo imodzi ya matepi, ndipo kenaka ndimatenga bukhu langa la nyimbo ndi kuimba limodzi pamene iye apita kukagona.”
Mayi ameneyu akupitiriza kulongosola kubadwa kosakwanira masiku kwa mwana wake wa posachedwapa ndi vuto lake la m’dongosolo lopumira, kumene anafunikira kukhala ndi chubu kum’mero kwake. Iye akunena kuti: “Ndinafunsa a namwino ngati chikanakhala chotheka kubweretsa wailesi yoseŵerera matepi ndi matepi ena a nyimbo kaamba ka iye. Iwo anati chinali chotheka. Anamwinowo sanakhulupirire mmene matepiwo anamthandizira iye kupumula. Iwo anapereka ndemanga yakuti nthaŵi iriyonse imene iye anavutitsa, zonse zimene iwo anakhoza kuchita zinali kumuimbira iye nyimbozo. Namwino mmodzi anakhoza ngakhale kunena kuti: ‘Ndikukhumba kuti tikanakhala ndi mtundu uwu wa nyimbo kaamba ka ana onse. Ziri zokongola koposa. Zonse zimene makandawa amamva ali mawu otonthonza a oyang’anira awo.’”
Ndithudi, ambiri apeza nyimbo zimenezi kukhala zochiritsa ku moyo wawo. Alubamu yokongola yokhala ndi mutu wakuti “Sing Praises to Jehovah,” yokhala ndi makaseti asanu ndi atatu, iripo pa K120.00 yokha. Mungalandire alubamu yanu mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka limodzi ndi malipiro anu.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, alubamu ya “Sing Praises to Jehovah” yokhala ndi makaseti tepi asanu ndi atatu a nyimbo. Ndatsekeramo K120.00. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)