Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Mtundu Wotaika, Koma Osati Wonse
MWAMSANGA pambuyo pa kukambitsirana kwa Yesu ndi awo omwe anasonkhana kunja kwa nyumba ya Afarisi, ena akumuuza iye “ponena za Agalileya amene mwazi wawo [nduna ya Chiroma Pontiyo] Pilato anasanganiza ndi nsembe zawo.” Agalileya amenewa ali mwinamwake amene anaphedwa pamene Ayuda zikwi zingapo anatsutsa kugwiritsira ntchito ndalama kwa Pilato kuchokera m’thumba la kachisi kumanga ngalande yobweretsera madzi m’Yerusalemu. Awo olongosola nkhaniyi kwa Yesu angakhale akulingalira kuti Agalileya anavutika ndi tsoka chifukwa cha kachitidwe kawo koipa.
Yesu, ngakhale kuli tero, awalungamitsa iwo, akumafunsa kuti: “Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akuchimwa koposa Agalileya onse chifukwa anamva zowawa izi? Ndinena kwa inu, laitu,” Yesu akuyankha tero. Kenaka iye akugwiritsira ntchito chochitikacho kuchenjeza Ayuda kuti: “Koma ngati simutembenuka mtima, mudzawonongeka nonse momwemo.”
Akumapitiriza, Yesu akumbukiranso tsoka lina la kumaloko, mwinamwakenso logwirizanitsidwa ndi kumangidwa kwa ngalande. Iye akufunsa: “Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu amene nsanja yaitali ya m’Siloamu inawagwera, ndi kuwapha, kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu?” Ayi, sichinali chifukwa cha kuipa kwa anthu amenewa kumene kunawapangitsa iwo kufa, Yesu akutero. M’malomwake, “zomgwera m’nthaŵi mwake” ziri mwachisawawa zathayo kaamba ka matsoka oterowo. Yesu, ngakhale kuli tero, kachiŵirinso akugwiritsira ntchito chochitikacho kuchenjeza: “Koma, ngati simutembenuka mtima, mudzawonongeka nose chimodzimodzi.”
Yesu kenaka akupitiriza kupereka fanizo loyenera, akumalongosola kuti: “Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m’munda wake wamphesa, ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe. Ndipo anatai kwa wosungira munda wamphesa, ‘Tawona zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe. Taulikha! Uyeseranjinso nthaka yopanda pake?’ Ndipo iye anayankha nanena naye, ‘Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete ndithirepo ndowe; ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.’”
Yesu watsiriza zoposa zaka zitatu akuyesera kulimirira chikhulupiriro pakati pa mtundu wa Chiyuda. Koma kokha ophunzira mazana oŵerengeka angakhoze kuŵerengedwa kukhala zipatso za kugwira ntchito kwake. Tsopano, mkati mwa chaka chchinayi chimenechi cha utumiki wake, iye akukulitsa zoyesayesa zake, mophiphiritsira kukumba ndi kuika ndowe mozungulira “mtengo wa mkuyu” wa Chiyuda mwakulalikira mwachangu ndi kuphunzitsa m’Yudeya ndi Pereya. Komabe popanda chotulukapo! Mtunduwo ukukana kulapa ndipo chotero uli mumzera kaamba ka chiwonongeko. Kokha otaslira a mtunduwo akuvomereza.
Mwamsanga pambuyo pake Yesu akuphunzitsa m’sunagoge pa Sabata. Kumeneko iye awona mkazi amene, chifukwa cha kukanthidwa kwake ndi ziwanda, iye wapetekedwa kwa zaka 18. Mwachifundo, Yesu akunena ndi iye: “Mkaziwe, wamasulidwa ku kudwala kwako.” Pa chimenecho iye atambasula manja ake pa mkaziyo, ndipo panthaŵi yomweyo iye atambasuka ndi kuyamba kumekeza Mulungu.
Mkulu wa sunagoge, ngakhale kuli tero, wakwiyitsidwa. “Alipo masiku asanu ndi limodzi m’memeno anthu ayenera kugwira ntchito,” iye akutsutsa tero, “Chifukwa chake, idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la sabata ayi.” Mkuluyo chotero akuvomereza mphamvu ya Yesu ya kuchiritsa koma atsutsa anthu kaamba ka kudza kudzachiritsidwa pa Sabata!
“Onyenga inu,” Yesu akuyankha tero, “kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng’ombe yake kapena buru wake ku chodyeramo tsiku la sabata kupita nayo kukaimwetsa madzi? Ndipo mkazi uyu ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani! zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imenyi tsiku la sabata?”
Chabwino, pa kumva ichi, awo otsutsa Yesu ayamba kumva manayazi. Khamu, ngakhale kuli tero, lisangalala pa zinthu za ulemerero zonse zimene akuwona Yesu akuzichita. M’kuyankha Yesu abwereza mafanizo aŵiri a ulosi onena za Ufumu wa Mulungu, amene iye anawanena ali m’bwato pa Nyanja ya Galileya chifupifupi chaka chimodzi kumayambiriro. Luka 13:1-21; Mlaliki 9:11; Mateyu 13:31-33.
◆ Ndi matsoka otani omwe akutchulidwa pano, ndipo ndi phunziro lotani limene Yesu akukoka kuchokera ku iwo?
◆ Ndi kugwira ntchito kotani komwe kungapangidwe ponena za mtengo wa mkuyu wosabala zipatso, limodzinso ndi kuyesera kuwupanga iwo kukhala wobala zipatso?
◆ Ndimotani mmene mkulu akuvomerezera kuthekera kwa kuchiritsa kwa Yesu, komabe ndimotani mmene Yesu akuvumbulira chinyengo cha munthu?