Kupanikizika kwa Chikatolika
TCHALITCHI cha Chikatolika pa nthaŵi ino chikuyang’anizana ndi mavuto aŵiri m’chigwirizano ndi Mdyerekezi. Ku mbali imodzi, icho chikulimbana ndi chizoloŵezi pakati pa Akatolika amakono cha kukaikira kukhalapo kwa Mdyerekezi. Ku mbali ina, icho chikuchita ndi kachitidwe kochulukira kosakhala ka lamulo ka kuchotsa ziwanda, kapena kutulutsa mizimu yoipa.
Papa John Paul II anakumbutsa achichepere a Chikatolika kuti iwo ayenera kutenga Mdyerekezi mosamalitsa. M’kalata, iye analemba kuti: “Simuyenera kuwopa kuitana wogwira ntchito woyambirira wa kuipa ndi dzina lake: Woipayo. Iye wagwiritsira ntchito ndipo akupitirizabe kugwiritsira ntchito machenjera a kusadzivumbula iye mwini.”
Mofananamo, cardinal Joseph Ratzinger, woyang’anira wa Mpingo Wopatulika kaamba ka Chiphunzitso cha Chikhulupiriro, mu Roma, ananena kuti: “Chirichonse chomwe ozindikira mochepera a nthanthi yaumulungu anganene, mdyerekeziyo, ku ukulu umene chikhulupiriro cha Chikristu chimakhudzidwira, ali wodabwitsa koma weniweni, wa umunthu ndipo osati kukhalapo chabe kwa chizindikiro. Iye ali chenicheni champhamvu.”
Cardinal Ratzinger analongosolanso nkhaŵa yaikulu ponena za kukumana kokhudza Satana kosakhala kwalamulo kochitidwa ndi Akatolika m’maiko ambiri. M’kalata yosonyeza deti la September 29, 1985, yolembedwa kwa mabishopu onse a Chikatolika kuzungulira dziko lonse, iye analemba kuti: “Kwa zaka zingapo, m’matchalitchi ena, misonkhano ya kupemphera yowonjezerekawonjezereka ikuchitidwa ndi lingaliro la kumasula anthu kuchoka ku chisonkhezero cha ziwanda.” Iye anakumbutsa ndunazo kuti mogwirizana ndi lamulo la canon, palibe misonkhano yoteroyo ingachitidwe popanda chilolezo cholongosoledwa chochokera kwa bishopu wa kumaloko ndi kuti chilolezo choterocho chiyenera kuperekedwa kokha kwa ansembe. Palibe munthu wamba yemwe ali ndi kuyenera kwa kutchula “njira yotulutsira ziwanda molimbana ndi Satana ndi angelo opanduka.”
Nyuzipepala ya tsiku ndi tsiku ya ku France Le Figaro inasimba kuti: “‘Kukula’ m’kuchotsa ziwanda ndi machitachita okana Satana zatulukira poyera mkati mwa miyezi yoŵerengeka yapita mu Italy, makamaka mu Turin, kumene cardinal Anastasio Ballestrero wangosankha kumene otulutsa ziwanda atsopano asanu ndi mmodzi.” Kupatsa nkhaniyo kayang’anidwe kozungulira dziko lonse, International Herald Tribune ya tsiku ndi tsiku ya ku Paris inalemba kuti: “Chikondwerero m’kukhalapo kothekera kwa Satana mu Turin chiri kokha mbali ya kukambitsirana kokulira mkati mwa Tchalitchi cha Roma Katolika ponena za kuimiridwa monga munthu kwa kuipa kolozeredwa mosiyanasiyana m’Malemba ndi chiphunzitso cha tchalitchi monga ‘kalonga wa dziko lino,’ ‘mphamvu ya mdima,’ ‘chinjoka chakale,’ ‘woneneza.’”
Chiwalo cha Maphunziro Apamwamba cha ku France Jean Dutourd anapanga ndemanga zokondweretsa pa zikaikiro zamakono ponena za kukhalapo kwa Satana—ngakhale kochitidwa ndi nduna za Chikatolika. Iye analemba mu L’EstRepublicain ya tsiku ndi tsiku ya ku France kuti: “Chikhulupiriro mwa Mulungu chikukwinyiridwa pamaso masiku ano, koma sichikuloledwa mowonjezereka kapena mochepera. Chikhulupiriro mwa Mdyerekezi, ngakhale kuli tero, chikuwonedwa kukhala choseketsa kotheratu. Kutchulidwa kokha kwa dzina lakuti Satana . . . mokulira kumaseketsa anzeru, okonda zakuthupi, a ndale zadziko, ndiponso, mosakaikira, chiŵerengero chabwino cha mabishopu. Chiphwete chawo chikundidabwitsa ine mowonjezereka kwambiri chifukwa chikuwoneka kuti Mdyerekezi wakhala akutipatsa chisamaliro chapadera chiyambire 1914.”
Ngati Akatolika, kuphatikizapo atsogoleri achipembedzo ena, afunikira kukumbutsidwa ndi papa ndi ena kuti Satana ndithudi alipo, kodi sichiri chifukwa chakuti tchalitchi kwa mazana ambiri chaika chigogomezero chokulira pa mwambo, nthanthi, ndi nthanthi za sayansi, zosatsimikiziridwa kuposa pa Baibulo?
Kutchulidwa kwa pamwambapo kwa 1914 ndithudi kuli koyenerera. Chaka chimenecho chazindikiritsidwa mu ulosi wa Baibulo kukhala kuyamba kwa “masiku otsirizira” pamene Mdyerekezi, monga “wolamulira wa dziko,” akupanga kuyesetsa kwake komalizira kuwononga mtundu wonse wa anthu. (2 Timoteo 3:1; Yohane 14:30, NW) Monga mmene kutembenuzidwa kwa Baibulo kwa Chikatolika kukulongosolera: “Tsoka likubwera—chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu mu ukali, akudziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” Akatolika owona mtima akachita bwino kulandira chiphunzitso cha Baibulo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mikhalidwe ya dziko lerolino ikutsimikizira kuti “ufumu wa Mulungu uli pafupi.”—Chibvumbulutso 12:7-12; Luka 21:25-31, The New Jerusalem Bible.
Popeza kuti Ufumu umenewo ukulonjeza kuthetsa chisalungamo chonse ndi zochititsa zake, kuchotsedwa kwa Mdyerekeziyo ndi achirikizi ake kwayandika. Ngakhale kuli tero, kokha anthu amene akudziŵa kuti Mdyerekeziyo aliko angatenge kaimidwe motsutsana ndi ulamuliro wake ndi kuyembekezera kaamba ka chipulumutso. Motani? Osati kupyolera mwa kutulutsa ziwanda koma, m’malomwake, monga mmene mtumwi Paulo analembera, mwa kuvala “zida zonse za Mulungu.” Inde, Mawu a Mulungu ali omvekera bwino: “Kanizani mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.”—Aefeso 6:11-18; Yakobo 4:7.
[Chithunzi patsamba 26]
Mdyerekezi ndi ziwanda zake aponyedwa pansi pafupi ndi dziko lapansi.—Chibvumbulutso 12:9, 12
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Picture Book of Devils, Demons and Witchcraft/Ernst ndi Johanna Lehner/Dover