Kupeza Chuma M’Malo Akutali
Kufunafuna golidi, kapena chuma china chakuthupi, kwapangitsa ambiri kupita ku malo akutali. Koma ena apita kukapeza chinachake chofunika koposa—anthu okhala ndi mikhalidwe imene imawapanga kukhala okhumbika kwa Mulungu. Ŵerengani mu 1990 Yearbook of Jehovah’s Witnesses ponena za chuma chenicheni chimenechi.
Munthu amene anaŵerenga Yearbook yachaka chatha analemba kuti: “Nzodabwitsa kuwona mmene mumayandikirira kwa awo amene simunakumanepo nawo, ndi mmene mumagawanira nawo zisoni zawo ndi chisangalalo! Ndimalimbikitsidwa kwambiri ndi zolembera zimenezi.”
Yearbook yachaka chino iri ndi maripoti osangalatsa onena za ntchito ya Mboni za Yehova mu Colombia, Finland, ndi Suriname, limodzinso ndi chithunzi chaposachedwapa cha ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita pa dziko lonse.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, 1990 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Ndatumiza K16 (Zambia).