Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Kuchokera pa Tabori Kutsikira ku Chilakiko!
TANGOLINGALIRANI muli pa nsanja mukumayang’ana pansi pa malo amene njira za’mbiri zinadutsa! Inu mukawonadi ndi maso mbiri ikupangika.
Malo Abaibulo a Megido angalinge bwino lomwe kalongosoledwe kameneko, popeza kuti panadutsa njira zofunika kwambiri za malonda ndi za nkhondo. Chikhalirechobe, kutsidya la Chigwa cha Yezreeli kukuima Phiri la Tabori, loyang’ananso pansi pa Via Maris, njira yotchuka yopita ku mizinda ya ku Fertile Crescent.a
Ngati mupenya Tabori kuchokera kulikonse m’chigawocho, mungangosangalatsidwa. (Yerekezerani ndi Yeremiya 46:18.) Tabori akuima payekha mochititsa chidwi wosiyana ndi malo ozungulira, kaumbidwe kake kosongoka kakuwonekera kuchokera ku mbali zonse. Iye akuimirira pamwamba pa chidikha chodutsa patsogolo pake kum’mwera, Chigwa chachonde cha Yezreeli, chimene chimalumikiza gombelo ndi Chigwa za Yordano.
Kuchokera pa nsonga youlungika bwino ya Tabori, mungapenye kum’mwera kulinga ku mzinda wa Yezreeli, umene ungakukumbutseni kuthamanga pakavalo kwa Yehu ndi liŵiro laukali kulinga ku nyumba yachifumu ya Ahabu ndi kutha kwamanyazi kwa Yezebeli. (1 Mafumu 21:1; 2 Mafumu 9:16-33) Chapafupi pali Megido. Chakumadzulo mungawone Phiri la Kalimeli, kumene Eliya anachititsa chiyeso cha moto. (1 Mafumu, mutu 18) Kuchokera pa Tabori mungawonenso kumene mtsinje wa Kisoni umatsirira ku nyanja, ndipo chifupifupi makilomita asanu ndi atatu kumadzulo mbali yakumadzulo koma chakum’mpoto m’mapiri a kunsi kwa Galileya kuli Nazarete.
Koma kodi ndi nkhani ya m’Baibulo yotani imene ibwera m’maganizo anu pamene Tabori atchulidwa? Mwachiwonekere ndi ija ya Debora ndi Baraki. M’nthaŵi yawo, Akanani pansi pa Mfumu Yabini ya Hazori anapondereza Israyeli kwa zaka 20. Ndiyeno mneneri wamkazi Debora anasonkhezera Baraki kuchitapo kanthu. Iye, nayenso, anatenga Aisrayeli zikwi khumi, ambiri a iwo a fuko la Nafitali ndi Zebuloni napita nawo ku Galileya, nawasonkhanitsa pa Tabori. Iwo sanali ndi zida zokwanira, popeza kuti mu Israyeli munalibe chikopa nchimodzi chomwe kapena nthungo.—Oweruza 5:7-17.
Makina ankhondo owopsya anadza motsutsana nawo. Sisera kazembe wankhondo wa Yabini anabwera ndi Akanani okhala ndi zida zowopsya ku Chigwa cha Yezreeli. Iwo ayenera kukhala anawoneka ngati amuna okhala ndi zida zankhondo osonyezedwa pa zithunzi zozokotedwa pa chipupa zochokera ku Igupto patsamba lotsatira, pamwamba kulamanja. Ziwiya zankhondo za Igupto zinasonkhezera zija zogwiritsiridwa ntchito mu Kanani, kuphatikizapo mbali yowopsya koposa ya zida za Sisera—magareta ankhondo 900!
Magareta Achikanani amenewo analidi nsanja zoyenda zolasirapo. Woyendetsa angakhale ankamanga thondolo (zingwe zoyendetsera akavalo) m’chiuno mwake kotero kuti manja ake anali omasuka kumenya nkhondo ndi zida. Kapena akanasumika maganizo pa kutsogoza akavalo othamangawo pamene mnzake ankamenya nkhondo ndi zidazo. Magaretawo anali ndi zisenga zachitsulo zolumikizidwa ku milongoti ya ku magudumu. Kwa amuna a Baraki omapenya chapansi ali pa Tabori, magareta ochulukawo ayenera kukhala anawoneka mowopsya osakhoza kuimitsidwa, osagonjetseka.
Komabe, Yehova anali atalonjeza Baraki kuti: “Ndidzamkoka Sisera, . . . akudzere kumtsinje wa Kisoni . . . ndi magareta ake; ndi aunyinji ake.” Pa mphindi yoyenera, Aisrayeli olimbika mtimawo anatsikira ku mbali ya Tabori.—Oweruza 4:1-14.
Chofunika kwambiri kuposa mwaŵi wodabwitsawo chinali nthandizo limene Israyeli analandira kuchokera kwa Mulungu wawo wamphamvu wakumwamba. Debora pambuyo pake anayimba kuti: “Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m’mipata mwawo zinathirana ndi Sisera. Mtsinje wa Kisoni unawakokolola . . . Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.” (Oweruza 5:20, 21) Inde, ngakhale kuti Aisrayeli osakhala ndi zida zowopsya koma olimba mtima anabalalitsa Akanani, Mulungu anafunitsitsa chotulukapo chenicheni. Iye anachititsa mkokomo wamadzi wamwadzidzidzi m’mtsinje wouma, kuimitsa magareta owopsyawo.
Chapansi mukuwona mbali ya mtsinje wa Kisoni. M’nyengo yamvula, ungasefukire pa magombe ake ndi kupanga malowo kukhala dambo. Wonani m’diso lanu lamaganizo magareta ankhondo Achikananiwo akuyesera kuthaŵa kupyola m’matope oterowo. Madzi okokomokawo anatenga asilikari ena othawa kapena magareta, kapena zonse ziŵiri. Chilakiko cha Israyeli chinagwira ngakhale Kazembe Sisera, amene anataya gareta wake, nathamanga pansi kuthaŵa malo ankhondowo. Atabisala m’hema la mkazi Yaeli, mkaziyo anasankha nthaŵi yabwino ndi kupha mdaniyo.—Oweruza 4:17-22.
Motero, chaputala chofunika kwambiri ndi chachilakiko m’mbiri ya Israyeli chinatseguka pamaso pa Debora ndi ena alionse amene angakhale ankapenyerera kuchokera pa nsonga ya Phiri la Tabori.
[Mawu a M’munsi]
a Onani mapu ndi chithunzi chachikulu, chowonekera bwino cha Tabori mu 1990 Kalenda ya Mboni za Yehova.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 17]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.