Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Amaliza Zonse Zimene Mulungu Afuna
PAMENE Mfumu Yesu Kristu Wankhondoyo achotsa Satana ndi dziko lake losalungama, padzakhala chochititsa chisangalalo chotani nanga! Pomalizira pake Ulamuliro wa Zaka Chikwi wamtendere wa Yesu uyamba!
Pansi pa chitsogozo cha Yesu ndi mafumu anzake, opulumuka Armagedo adzayeretsa mabwinja osiidwa ndi nkhondo yolungamayo. Mwachiwonekere, opulumuka apadziko lapansi adzabalanso ana mwakanthaŵi, ndipo ameneŵa adzakhala ndi phande m’ntchito yosangalatsa yosandutsa dziko lapansi kukhala munda wokongola wonga paki.
M’kupita kwanthaŵi, Yesu adzaukitsa mamiliyoni osaŵerengeka kuchokera m’manda awo kudzasangalala ndi Paradaiso wokongolayo. Adzachita chimenechi kukwaniritsa chitsimikizo chake chakuti: ‘Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] . . . adzatuluka.’
Pakati pa awo amene Yesu adzaukitsa padzakhala mpandu wakaleyo amene anafera pambali pake pamtengo wozunzirapo. Kumbukirani kuti Yesu anamlonjeza kuti: ‘Indetu, ndinena ndi iwe lerolino, udzakhala ndine m’Paradaiso.’ Ayi, mwamunayo sadzatengedwa kumwamba kukalamulira monga mfumu pamodzi ndi Yesu, ndipo Yesu sadzakhalanso munthu ndikukhala ndi moyo padziko lapansi Laparadaiso pamodzi naye. Mmalomwake, Yesu adzakhala ndi mpandu wakaleyo m’lingaliro lakuti Iye adzamuukitsa ku moyo m’Paradaiso ndi kuwona kuti zosoŵa zake, ponse paŵiri zakuthupi ndi zauzimu, zikusamaliridwa, monga kwasonyezedwera patsamba lino.
Tachilingalirani! Pansi pa chisamaliro chachikondi cha Yesu, banja lonse la anthu—opulumuka Armagedo, ana awo, ndi zikwi za mamiliyoni oukitsidwa kwa akufa omwe adzamvera iye—adzafikira ungwiro waumunthu. Yehova, kupyolera mwa Mwana wake wachifumu, Yesu Kristu, adzakhala mwauzimu ndi anthu. ‘Ndipo,’ monga momwe mawu omwe Yohane anamva kuchokera kumwamba akunenera, ‘adzaŵapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.’ Palibe munthu padziko lapansi yemwe adzavutika kapena kudwala.
Podzafika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Yesu, mkhalidwe udzakhala monga momwe Mulungu anafunira pachiyambi pamene anauza anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava, kuchuluka ndi kudzaza dziko lapansi. Inde, dziko lapansi lidzazala ndi fuko la anthu olungama angwiro. Ichi nchifukwa chakuti mapindu a nsembe yadipo ya Yesu adzakhala atagwiritsiridwa ntchito kwa aliyense. Imfa yodzetsedwa ndi tchimo la Adamu sidzakhalakonso!
Motero, Yesu adzakhala atakwaniritsa zonse zimene Mulungu anafuna kwa iye. Chifukwa chake, pamapeto a zaka chikwi, iye adzapereka Ufumu ndi banja la anthu angwiro kwa Atate wake. Ndiyeno Mulungu adzamasula Satana ndi ziŵanda zake ku phompho la mkhalidwe wosagwira ntchito wonga imfa. Kaamba ka chifuno chotani?
Eya, podzafika kumapeto kwa zaka chikwi, ambiri okhala ndi moyo m’Paradaiso adzakhala aja oukitsidwa amene chikhulupiriro chawo sichinayesedwepo nkalelonse. Asanafe, iwo sanadziŵe konse malonjezo a Mulungu ndipo motero sanakhoze kusonyeza chikhulupiriro mwa iwo. Kenaka, ataukitsidwa ndikuphunzitsidwa chowonadi Chabaibulo, kuli kosavuta kwa iwo m’Paradaiso, kutumikira Mulungu popanda chitsutso. Koma ngati Satana apatsidwa mwaŵi kuyesa kuŵaletsa kupitirizabe kutumikira Mulungu, kodi iwo akatsimikiza kukhala okhulupirika pansi pa chiyeso? Kuti funso iri liyankhidwe, Satana adzamasulidwa.
Chivumbulutso choperekedwa kwa Yohane chimavumbula kuti pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Yesu, Satana adzapambana kutembenuza chiŵerengero cha anthu chosadziŵika kuchoka pa kutumikira Mulungu. Komano, pamene chiyeso chomalizira chitha, Satana, ziŵanda zake, ndi onse amene iye adzakhoza kuwasokeretsa adzawonongedwa kosatha. Kumbali ina, opulumuka okhulupirika, oyesedwa kotheratu adzakhala ndi moyo kusangalala ndi madalitso a Atate wawo wakumwamba kwamuyaya.
Mowonekeratu, Yesu wachita mbali yaikulu, ndipo adzapitirizabe kutero, m’kukwaniritsa zifuno zaulemerero za Mulungu. Ha, ndimtsogolo mowala chotani nanga mmene tingasangalale namo monga chotulukapo cha zonse zimene iye akukwaniritsa monga Mfumu yaikulu yakumwamba ya Mulungu! Komabe, sitingaiŵale zonse zimene iye anachita pamene anali munthu.
Mofunitsitsa Yesu anabwera ku dziko lapansi natiphunzitsa ponena za Atate wake. Kupyola pamenepo iye anapereka chitsanzo cha mikhalidwe yapamwamba ya Mulungu. Mitima yathu imakhudzidwa pamene tilingalira kulimba mtima kwake ndi uchamuna wozizwitsa, nzeru yake yopanda ina yofanana nayo, luso lake loposa monga mphunzitsi, utsogoleri wake wopanda mantha, chifundo chake ndi kulingalira ena. Pamene tikumbukira mmene anavutikira mosaneneka pomwe ankapereka dipo, chinthu chokha chimene tingapezeremo moyo, ndithudi mitima yathu imakhudzidwa ndi chiyamikiro kwa iye!
Ndithudi, ndimunthu woposa chotani nanga amene tawona m’phunziro iri la moyo wa Yesu! Ukulu wake ngwowonekeratu ndi woposa. Timasonkhezeredwa kunena mawu a bwanamkubwa Wachiroma Pontiyo Pilato akuti: “Taonani munthuyu!”
Mwakulandira kwathu makonzedwe a nsembe yake yadipo, goli la tchimo ndi imfa lolandiridwa kuchokera kwa Adamu lingachotsedwe pa ife, ndipo Yesu angakhale “Atate [wathu] Wosatha.” Onse amene adzapeza moyo wosatha ayenera kupeza chidziŵitso osati cha Mulungu chokha komanso cha Mwana wake, Yesu Kristu. Tikhulupirira kuti kuŵerenga kwanu ndi kuphunzira mpambo wa nkhani za moyo ndi uminisitala za Yesu kwakuthandizani kupeza chidziŵitso chopatsa moyo choterocho! 1 Yohane 2:17; 1:7; Yohane 5:28, 29; 3:16; 17:3; 19:5; Luka 23:43; Genesis 1:28; 1 Akorinto 15:24-28; Chibvumbulutso 20:1-3, 6-10; 21:3, 4; Yesaya 9:6.
◆ Kodi mwaŵi wosangalatsa wa opulumuka Armagedo ndi ana awo udzakhala wotani?
◆ Kodi ndani amene adzasangalala ndi Paradaiso kuwonjezera pa opulumuka Armagedo ndi ana awo, ndipo kodi ndimlingaliro lotani limene Yesu adzakhalira nawo?
◆ Kodi mkhalidwe udzakhala wotani pamapeto pa zaka chikwi, ndipo kodi nchiyani chimene Yesu adzachita pamenepo?
◆ Kodi nchifukwa ninji Satana adzamasulidwa ku phompho, ndipo kodi nchiyani chimene pomalizira pake chidzachitika kwa iye ndi onse omtsatira?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu angakhalire “Atate [wathu] Wosatha”?