Tanthauzo la Pemphero
“Mu Chihebri, liwu lalikulu lotembenuzidwa pemphero limachokera ku liwu lotanthauza, ‘kuweruza’, ndipo m’kalembedwe kamasiku onse kodziloza wekha . . . m’lingaliro lenileni limatanthauza, ‘kudziweruza wekha.’” Imanena motero The Authorised Daily Prayer Book. Tanthauzo nlakuti imodzi ya ntchito za pemphero njakuti ilo liyenera kuthandiza munthu kuwona ngati akufitsa miyezo yolungama ndi ziyeneretso za Mulungu.
Pachifukwa chimenechi, timauzidwa m’Baibulo lonse kuti, mapemphero a munthu amamvedwa moyanja kokha ngati munthuyo amachita chifuniro cha Mulungu. “Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.”—Miyambo 15:29; 1 Yohane 5:14.
Kudzisanthula pamaso pa Yehova Mulungu kuyeneradi kupangitsa wopempherayo kukhala wodzichepetsa ndi wolapa. Ichi chimagogomezera tanthauzo la fanizo la Yesu la Mfarisi wodzitama ndi wamsonkho wolapa omwe anabwera kukachisi kudzapemphera.—Luka 18:9-14.
Chotero, kaya ngati tikupemphera kwa Yehova kumyamikira, kumtamanda, kapena kumpempha, pemphero nthaŵi zonse limakhala nthaŵi yakudzisanthula. Mwanjirayi, pemphero limatiyandikiritsa kwa Yehova ndi kulimbitsa unansi wathu ndi iye.