Chikhulupiriro Chawo cha Chisinthiko Chinagwedezedwa
Mwamuna wina wa ku Milwaukee, Wisconsin, U.S.A., analemba kalata chaka chatha kufotokoza chiyamikiro “kaamba ka chiŵiya chabwino koposa cha bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?” Iye anafotokoza kuti:
“Pafupifupi zaka ziŵiri zapitazo, ndinakumana ndi achichepere okwatirana ochokera ku Beijing, Chaina, omwe anabwera ku koleji yazamankhwala kuno ku Milwaukee. Iwo ndi akatswiri a biochemistry, ndipo sanabise chikhulupiriro chawo chenicheni cha chisinthiko.
“Ndinadzimvadi kukhala wochepa m’kulankhula nawo zasayansi, chotero ndinaganiza kulola bukhulo kuti liphunzitse lokha. Pamene tinapitiriza ndi phunziro lathu, ndinawona kuti chidaliro chawo m’chisinthiko chinayamba kugwedera.”
Phunziro la bukhu lonse linatha, ndipo mwamuna wa ku Milwaukee ameneyo anamaliza kuti: “Baibulo lakhala magwero owona a chidziŵitso kwa iwo. Ndiyamikiranso kaamba ka chiŵiya chabwino koposa chija.”
Ngati mungakonde kulandira bukhu la zithunzithunzi zokongola lamasamba 256 limeneli, chonde dzazani ndi kutumiza kapepalaka.
Ndingakonde kulandira bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakumaloko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)
[Zithunzi patsamba 32]
Wolinganiza anafunikira kaamba ka mutu wa muvi uwu
Kodi wolinganiza sanafunikire kaamba ka DNA iyi?