Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi nchifukwa ninji 29 C.E. imawonedwa kukhala deti lalikulu m’mbiri ya Baibulo m’malo mwa 14 C.E., pamene ufumu wa Tiberiyo Kaisara unayamba, yemwe akutchulidwa pa Luka 3:1?
Baibulo silimatchula chiyambi cha ufumu wa Tiberiyo, koma chochitika chimene chinakhalako m’mbali yomalizira ya chaka chake cha 15. Ichi chimakhozetsa ophunzira Baibulo kuika deti la chochitikacho mu 29 C.E., limene lingalingaliridwe kukhala deti lalikulu m’lingaliro Labaibulo.
Ufumu wa wolamulira wachiŵiri wa Roma, Tiberiyo Kaisara, umalandiridwa bwino lomwe m’mbiri. The New Encyclopædia Britannica imanena kuti: “Mu AD 14, pa August 19, Augusto [wolamulira woyamba] anamwalira. Tiberiyo, tsopano wokhala wamkulu, anagwiritsira ntchito mwamachenjera Bungwe la Akuluakulu ndipo sanalole kuti amtchule monga wolamulira kwa pafupifupi mwezi umodzi, koma pa September 17 iye anakwera pamalowo.”a
Nthaŵi yokhazikitsidwa imeneyi monga chiyambi cha ufumu wa Tiberiyo njogwirizana ndi Baibulo chifukwa chakuti Luka 3:1-3 amati ponena za uminisitala wa Yohane Mbatizi: ‘Ndipo pachaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, . . . panadza mawu a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m’chipululu. Ndipo iye anadza ku dziko lonse la m’mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo.’
Yohane sanayambe kulalikira ndi kubatiza pamene Tiberiyo anakhala wolamulira koma anatero mu ‘chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara.’ Chaka cha 15 chimenecho chinayambira m’phukuto ya 28 C.E. mpaka m’phukuto ya 29 C.E. Komabe, kudziŵa zimenezi sikumakhozetsa munthu kudziŵa motsimikizirika pamene uminisitala wa Yohane unayamba mkati mwa chaka chimenecho kapena kuŵerengera nthaŵi ya zochitika zoukhudza.
Koma Baibulo limatipatsa mawu ofunika othandizira. Mwachitsanzo, ulosi wa Danieli wa ‘masabata makumi asanu ndi aŵiri’ unaloza ku 29 C.E. kaamba ka kufika kwa Mesiya. Unasonyezanso kuti uminisitala wa Yesu ukakhala wautali wa zaka zitatu ndi theka. (Danieli 9:24-27) Onjezani pazimenezi tsatanetsatane wa m’Baibulo uyu: Yesu anabadwa miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pa Yohane; pamene Yesu anabatizidwa, “anali monga wa zaka makumi atatu”; ndipo Yesu anamwalira m’ngululu ya 33 C.E. (nthaŵi ya Paskha), pamene anali wazaka 33 1/2 zakubadwa.—Luka 1:24-38; 3:23; 22:14-16, 54.b
Ndi chidziŵitso Chabaibulo cholondola choterocho, kuphatikizapo kuŵerengera kwakudziko kwa madeti a ufumu wa Tiberiyo, ophunzira Baibulo akhoza kuŵerengera kuti uminisitala wa Yohane unayamba m’ngululu ya 29 C.E. ndikuti miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake, m’phukuto ya 29 C.E., Yohane anabatiza Yesu. Chifukwa chake, si 14 C.E. koma 29 C.E. imene ikuwonedwa kukhala deti lalikulu malinga ndi lingaliro Labaibulo.
[Mawu a M’munsi]
a September 17 pakalenda ya Julius imalingana ndi September 15 pakalenda ya Gregory, kalenda imene imagwiritsiridwa ntchito mofala lerolino.
b Yerekezerani ndi Insight on the Scriptures, Volyumu 1, masamba 458, 463, 467; Volyumu 2, masamba 87, 899-902, 1099, 1100, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.