Chipembedzo cha ‘Chikhulupiriro Chosinthasintha’
“Luso la chipembedzo cha Mormon lakupeza maziko m’mademokrase aufulu ndi m’zitaganya zotsendereza nlodabwitsa.” Inanena tero nyuzipepala ya The Wall Street Journal pamene boma la Hungary linalola mwalamulo Church of Jesus Christ of Latter-day Saints. Kodi tchalitchicho chimapeza motani zimenezi? Malinga ndi Journal imeneyo, “Mfungulo sindiyo kubala kwambiri kwa Amormon kapena kufalitsa mwachangu uthenga wawo wabwino. Mmalomwake, ndiyo kusinthasintha kwa chikhulupiriro chawo.” Motani?
Polankhula za nyengo yokhalako kusintha kwa zandale kusanachitike Kum’maŵa kwa Yuropu, Journal imeneyo inati: “Pokhala amagwiritsira ntchito magulu oimba ndi ovina ochokera pa Yunivesiti ya Brigham Young, Amormon apyola chitsenderezo ndi kusalandiridwa komwe kaŵirikaŵiri kumayang’anizana ndi amishonale m’maiko ochuluka a Chikomyunizimu.” Magulu awo ovina apita ku Romania, Chekosolovakiya, Hungary, Poland, Russia, ndi Tchaina, kuphatikizapo Saudi Arabia, Libya, Egypt, Jordan, Somalia, ndi Israel. Ndiponso, “chuma cha Tchalitchi cha Mormon chagwiritsiridwa ntchito monga ulalo woloŵera m’maiko otsatira nthanthi za Marx ndi Maiko Osatukuka.” Zinthu zina zochirikizidwa ndi zopereka za Amormon ndizo kumangidwa kwa maiŵe ndi zitsime.
M’dziko lamakonoli lokonda zosangulutsa ndi losusukira ndalama, nzosadabwitsa kuti maluso otero akuvina ndi kuimba ndi chithandizo cha ndalama ali okopa kwambiri. (2 Timoteo 3:2, 4) Koma anthu onga nkhosa enieni amakopeka ndi mawu a Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. (Yohane 10:27) Chifukwa chake, pamene analamula ophunzira ake “kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse,” sananene kutero mwanjira iriyonse kapena pamtengo uliwonse koma ‘kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene iye anawalamulira.’ (Mateyu 28:19, 20, NW) Pochita ntchito imeneyi, sipayenera kukhala chifukwa chirichonse chololera molakwa miyezo ya Baibulo.