Kodi Muli Monga Imodzi ya Izi?
‘KULI kwabwinopo kukhala mkango kwa tsiku limodzi koposa kukhala mwana wa nkhosa kwa zaka zana limodzi.’ Mawu amenewo anenedwa kuti analankhulidwa ndi Benito Mussolini, amene nthaŵi ina anali wolamulira wotsendereza ufulu wa Italiya.
Mofanana ndi Mussolini anthu ambiri akatsutsa kukhala odziŵika monga ana a nkhosa ndi nkhosa. Komabe, Davide mfumu yakale ya Israyeli amenenso anali wamasalmo anati: “Yehova ndiye Mbusa wanga; . . Anditsogolera ku madzi odikha.” (Salmo 23:1, 2) Inde, Yehova Mulungu ali Mbusa Wamkulu, amene amapatsa anthu ake chisamaliro chokoma mtima monga ngati kuti iwo anali nkhosa zosavulaza.
Anthu a Mulungu amanenedwa kukhala nkhosa zophiphiritsira pa Salmo 95:7, pamene timaŵerenga kuti: “Pakuti Iye [Yehova] ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m’dzanja mwake.” Ena angakhale atayembekezera wamasalmoyo kulankhula za “nkhosa za pabusa pake” ndi “anthu am’dzanja mwake.” Komatu panopa zinthu zinatembenuzidwa, ndipo chotero anthu a Yehova enieniwo akutchulidwa monga nkhosa zake. Iwo akusangalala ndi mapindu a pabusa pa Mulungu ndipo akutsogozedwa ndi dzanja lake lachikondi.
Mwana wa Yehova, Yesu Kristu, ndiye Mbusa Wabwino. Kaŵirikaŵiri iye anasonya anthu kukhala nkhosa. Mwachitsanzo, Yesu analankhula za “kagulu ka nkhosa” ndi “nkhosa zake zina.” (Luka 12:32, Yohane 10:14-16) Ponena za ophunzira ake odzichepetsa onga nkhosa, Yesu anati: “Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine. Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzawonongeka ku nthaŵi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa.” (Yohane 10:27, 28) M’dzanja la wolamulira wachifundo, nzika zinapindula ndi ulamuliro wake, chiyanjo, chitsogozo, ndi chitetezo.—Chivumbulutso 1:16, 20; 2:1.
Palibe munthu amene angakwatule anthu onga nkhosa owona m’dzanja lotetezera la Yesu. Lelolino, iye akulekanitsa anthu kaya monga “mbuzi” zopanda chiyanjo chake kapena monga “nkhosa” zimene zidzasangalala ndi moyo wamuyaya mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Mateyu 25:31-46) Kodi inu mudzatsimikizira kukhala mmodzi wa nkhosa zodalitsidwa zimenezo?
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Garo Nalbandian