Kufunafuna Maulosi Odalirika
“MUNTHU amene angawoneretu zinthu masiku atatu pasadakhale angakhale wolemera kwa zaka zikwi zambiri.” Umatero mwambi wa ku China.
Anthu amafunadi kudziŵa zimene zidzachitika maŵa, ndipo ambiri amakhala achimwemwe kulipira ndalama zambiri kaamba ka chidziŵitso chodalirika choterocho. Iwo amafunafuna maulosi odalirika. Monga momwe kuneneratu za nyengo ndi zosonyeza mkhalidwe wa zachuma kumasonyezera, timafuna kudziŵa zochitika za mtsogolo. Ndiponso, chidziŵitso chodalirika cha mtsogolo chingatitheketse kukonzekera ndi kulinganiza miyoyo yathu.
Chikhumbo chofuna kudziŵa za mtsogolo chimasonkhezera ambiri kufikira alauli, atsogoleri achipembedzo Achihindu, openda nyenyezi, ndi asing’anga. Masitolo ogulitsa mabuku ndi magazini ngodzaza ndi zolembedwa zamakedzana ndi zamakono za amene amanena kuti akhoza kuneneratu za mtsogolo. Koma mitundu imeneyo ya kulosera imakaikiridwa. Nduna yaboma ya ku Roma, Cato, akunenedwa kuti anati: ‘Ndimadabwa kuti wolosera samaseka pamene awona wolosera wina.’
Ndithudi, pali maulosi amitundu yosiyanasiyana. Mu 1972 kagulu kapadziko lonse ka akatswiri amaphunziro ndi azamalonda kodziŵika monga Club of Rome kanafalitsa zofufuzidwa zolosera kuti posachedwapa dziko likakhala lopanda chuma chosakhoza kubwezeretsedwa. Likakhala lopanda golidi pofika 1981, mercury pofika 1985, zinc pofika 1990, mafuta pofika 1992, ndi zina zotero. Tsopano tikuwona kuti maulosi ameneŵa sanakwaniritsidwe.
Maulosi ambiri azikidwa pa zikhulupiriro zachipembedzo. Mwachitsanzo: Bishopu wa ku Saxon Wulfstan anakhulupirira kuti kuukira Mangalande kochitidwa ndi Denmark kuchiyambi kwa zaka za zana la 11 kunali chizindikiro chakuti mapeto a dziko anali pafupi. Mu 1525, Thomas Münzer anatsogolera kupanduka kwa alimi a ku Jeremani chifukwa chakuti iye anawona m’masomphenya angelo akunola mazenga kaamba ka kumene anakulingalira kukhala kututa kwakukulu. Mwachiwonekere, maulosi ameneŵa anali onama.
Monga mudziŵa, Baibulo lili ndi maulosi. Ndiponso, olemba Baibulo ananena kuti anauziridwa ndi Mulungu. Mtumwi Wachikristu Petro anati: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.”—2 Petro 1:20, 21.
Pakati pa zinthu zina, Baibulo linaneneratu zochitika zosiyanasiyana zozindikiritsa mbadwo umene ukawona kukhalapo kwa Yesu Kristu muulamuliro wa Ufumu wakumwamba. Nkhondo, njala, zivomezi, ndi kuzilala kwa mphamvu yachikumbumtima cha anthu zoposa ndi kalelonse zikakhala zochitika za amene Baibulo limawalongosola kukhala “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-14, 34) Malinga ndi kunena kwa Baibulo, kuchotsedwa kwa dongosolo lazinthu lilipoli kukatsegula njira ya chimwemwe cha anthu m’dziko latsopano la madalitso osatha.—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1-4.
Kodi mumawawona motani maulosi Abaibulo amenewo? Mofanana ndi zoneneratu zina zambiri, kodi ali ongopeka chabe? Tingapende kudalirika kwa maulosi ena Abaibulo amene sanakwaniritsidwebe mwakuwona ngati maulosi a Baibulo onena za zochitika zakale anali odalirika. M’nkhani yotsatira, tidzapenda ena a ameneŵa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Mwachilolezo cha National Weather Service