Lipoti la Olengeza Ufumu
Kulemekeza Kupatulika kwa Moyo
BAIBULO limasonyeza kuti mwazi ngwamtengo wapatali kwa Mulungu ndi kuti iye amatsutsa kuugwiritsira ntchito molakwa. (Levitiko 17:14; Machitidwe 15:19, 20, 28, 29) Mboni za Yehova zimakana kuthiridwa mwazi chifukwa cha malangizo a Baibulo ameneŵa.
Pofuna kuthandiza madokotala ndi ogwira ntchito pachipatala kumvetsetsa kaimidwe kachipembedzo ka Mboni za Yehova pankhaniyi ndi kuwadziŵitsa kuti Mboni zikhoza kulandira chithandizo china chosiyana, Watch Tower Society yapanga makomiti ambiri otchedwa Hospital Liaison Committee (HLC) m’maiko osiyanasiyana. Ziŵalo za makomiti ameneŵa zimapita kuzipatala kukakambitsirana ndi ogwira ntchito ya m’chipatala. Posachedwapa, misonkhano yoposa 200 inachitidwa m’mizinda 12 m’Poland, ndipo kunafika madokotala oposa 500, makamaka oyang’anira makiliniki ndi mawadi a m’zipatala. Zotsatirazi zinachitika paumodzi wa ulendo umenewo:
“Msonkhano umene unachitidwa pa Cardio-Surgical Clinic ku Zabrze unali wachipambano kwambiri. Kuyambira 1986 gulu la madokotala a pakilinikipo lakhala likuchita maopaleshoni pa abale athu popanda mwazi. Panthaŵi inoyo, maopaleshoni otero okwanira 40 achitidwa. Ogwira ntchito pakilinikipo ngokonzekera kugoneka odwala ochokera m’Poland monse ndiponso ngakhale ochokera kumaiko akutali. Pambuyo pakukambitsirana kwa mphindi 50, wachiŵiri kwa mkulu woyang’anira wadi anadziŵikitsa ziŵalo za gulu la HLC kwa gulu la odwala nati: ‘Anthu awa ndi Mboni za Yehova. Iwo amachita zinthu mogwirizana ndi kiliniki yathu, ndipo amatithandiza. Iwo samathandiza okhulupirira anzawo okha komanso odwala ena onse amapindula ndi chithandizo chawo. Chifukwa cha Mboni za Yehova tili okhutira kuti maopaleshoni aakulu a mtima angachitidwe popanda mwazi.
“‘Mwachitsanzo, tinachita opaleshoni pa mayi uyu [akumaloza mmodzi wa odwala ake] popanda mwazi, ndipo Lolembali adzatulutsidwa m’chipatala. Ndingakonde kukudziŵitsani kuti timagwiritsira ntchito mwazi mwakamodzikamodzi kuposa kale chifukwa cha maupandu omwe uli nawo. Ngwogwirizanitsidwa ndi HIV, kutupa chiŵindi, ndi kuchedwa kuchira.
“‘Ndine Mkatolika, koma nthaŵi zonse m’banja mwathu timalolera malingaliro a ena. Tsiku lina ndinali kuyendayenda mu Slaski Stadium ndi ana anga. Kalelo, stediyamu imeneyi inanyalanyazidwa, koma tinaona kuti tsopano inasinthiratu. Ndinafunsa mmodzi wa ogwira ntchito pamenepo kuti masinthidwe ameneŵa anachitika motani. Iye anati akuluakulu oyang’anira malowo analibiretu chiyembekezo chokonza stediyamuyo, koma inabwerekedwa kwa Mboni za Yehova, ndipo zinaikonza.
“‘Chotero tonsefe tingaphunzire zochuluka kwa anthu ameneŵa. Ndiganiza kuti muwadi ino tiyenera kulolera malingaliro a ena.’ Ndiyeno, akumalozanso kwa Mboni imene inali pafupi kuchitidwa opaleshoni m’masiku oŵerengeka, iye anati: ‘Mayi uyu ndimmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo adzachitidwa opaleshoni popanda mwazi.’”
Pamene kuli kwakuti Mboni za Yehova sizimayesa kukakamiza zikhulupiriro zawo pa ena, izo zimatsatira chitsanzo cha atumwi ndipo ‘zimamvera Mulungu koposa anthu.’ (Machitidwe 5:29) Zimenezi zimaphatikizapo kulemekeza mwazi. Izo zimayamikira ngati ena alemekeza zikhulupiriro zawo zachipembedzo pankhaniyi.