Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi kungakhale koyenera kulandira katemera kapena jekeseni ina iliyonse yamankhwala okhala ndi “albumin” yotengedwa m’mwazi wa munthu?
Kunena mosabisa mawu, Mkristu aliyense ayenera kusankha chochita iyemwini pankhaniyi.
Atumiki a Mulungu moyenerera amafuna kumvera lamulo lopezeka pa Machitidwe 15:28, 29, la kusala mwazi. Mogwirizana ndi zimenezo, Akristu samadya nyama yosakhetsedwa mwazi kapena zinthu zonga masoseji amwazi. Koma lamulo la Mulungu limagwiranso ntchito m’zamankhwala. Mboni za Yehova zimanyamula khadi lonena kuti zimakana ‘kuthiridwa mwazi, mwazi wathunthu, maselo ofiira, maselo oyera, ma platelet, kapena plasma ya m’mwazi.’ Komabe, bwanji ponena za majekeseni a serum okhala ndi mlingo wochepa wa maprotini a mwazi?
Kwa nthaŵi yaitali Mboni zazindikira kuti chosankha pankhani imeneyi chili cha munthu mwini mogwirizana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. Zimenezi zinatchulidwa mu “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” a mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1990, imene inafotokoza majekeseni a serum amene dokotala anganene kuti ali ofunikira ngati wina wapezeka mumkhalidwe umene ungamdwalitse matenda akutiakuti. Zinthu zogwira ntchito m’majekeseni otero sizili plasma ya m’mwazi yeniyeniyo koma mankhwala ophera tizilombo m’thupi otengedwa mu plasma ya m’mwazi ya awo amene akhala otetezereka ku matenda. Akristu ena amene amalingalira kuti ndi chikumbumtima chabwino akhoza kulandira majekeseni otero anena kuti mankhwala ophera tizilombo m’thupi a m’mwazi wa mkazi wokhala ndi pathupi amaloŵa m’mwazi wa mwana amene ali m’chibaliro chake. “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” anatchula zimenezi, ndi mfundo yakuti mlingo wakutiwakuti wa albumin umatuluka mwa mkazi amene ali ndi pathupi ndi kuloŵa mwa mwana wake.
Ambiri amaona zimenezi kukhala zofunika, popeza kuti akatemera ena amene samapangidwa ndi mwazi angakhale ndi mlingo wocheperapo wa albumin ya plasma imene inagwiritsiridwa ntchito kapena kuwonjezedwako kulinganizira zoikidwa mumsanganizowo. Pakali pano mlingo wochepa wa albumin ukugwiritsiridwanso ntchito m’majekeseni a homoni yopanga ya EPO (erythropoietin). Mboni zina zalandira majekeseni a EPO chifukwa chakuti ingafulumize kupangika kwa maselo ofiira a mwazi ndipo motero kuchotsera dokotala lingaliro lakuti kuthira mwazi kungafunikire.
Mwina misanganizo ina ya mankhwala ingayambe kugwiritsiridwa ntchito mtsogolo imene mofananamo ingakhale ndi mlingo wocheperapo wa albumin, popeza kuti makampani opanga mankhwala akupanga zinthu zatsopano kapena akusintha njira zopangira zinthu zimene zilipo. Chifukwa chake Akristu angafune kudziŵa kaya ngati albumin ilimo m’katemera kapena m’jekeseni iliyonse imene dokotala afuna kuti iperekedwe. Ngati akukayikira kapena ali ndi chifukwa chokhulupirira kuti albumin ili mbali yake, akhoza kufunsa dokotala wawo.
Monga momwe kwatchulidwira, Mboni zambiri sizinakane kulandira jekeseni imene ili ndi mlingo wochepa wa albumin. Komabe, aliyense amene afuna kudziŵa nkhaniyi mwakuya asanapange chosankha ayenera kupenda chidziŵitso choperekedwa mu “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” a Nsanja ya Olonda ya June 1, 1990.