Kodi Baibulo Lili ndi Mtengo Wanji?
BRITISH Library posachedwapa inavomereza kulipira pafupifupi $1,600,000 kugula kope limodzi la matembenuzidwe Achingelezi a William Tyndale a Malemba Achigiriki Achikristu. Lofalitsidwa zaka 468 zapitazo, ndilo kope lokha loyamba lathunthu la Baibulo la Tyndale limene linapulumuka zoyesayesa za kuliwononga. Baibulo limeneli lakhala lili m’malo oonetsera zinthu mu London.
Baibulo la Tyndale linagulidwa ku Bristol Baptist College ku England, kumene lasungidwa chiyambire 1784. Dr. Roger Hayden, wachiŵiri kwa tcheyamani wa komiti ya pakoleji anati: “Ichi ndi cholembedwa cha mtundu, chamwambo ndi Chachikristu chokhala ndi kufunika kwakukulu ndipo tinafuna kuti chikhale chopezeka kwa ambiri, pakuti tachisungira m’malo obisika.”
Kwa zaka mazana ambiri Baibulo linalipo kwakukulukulu m’Chilatini ndipo linali kuŵerengedwa kokha ndi atsogoleri achipembedzo ndi anthu apamwamba ophunzira. Mofanana ndi John Wycliffe, iye asanakhaleko, Tyndale anafuna kuchititsa Baibulo kukhala lopezeka kuti liŵerengedwe ndi kumvedwa ndi onse. Nthaŵi ina iye anauza mtsogoleri wachipembedzo amene anali womtsutsa kuti: ‘Ngati Mulungu angandilole kukhala ndi moyo kwa zaka zambiri, ndidzachititsa mnyamata wolima ndi pulawo kudziŵa zambiri za Malemba kuposa iwe.’
Imeneyi inali ntchito yodzetsa ngozi, popeza kuti atsogoleri achipembedzo anatsutsa kowopsa kuyesayesa kulikonse kwa kuchititsa Malemba kukhala opezeka kwa anthu wamba. M’kupita kwa nthaŵi, Tyndale anathaŵa ku England kumka ku Germany. Kumeneko anatembenuza “Chipangano Chatsopano” kuchokera ku Chigiriki choyambirira. Makope pafupifupi 3,000 anasindikizidwa ndi kuloŵetsedwa mobisa mu England. Bishopu wa ku London anagula makope onse amene anapeza ndi kuwatentha pamaso pa anthu m’bwalo la tchalitchi cha St. Paul. Potsirizira pake, Tyndale anagwidwa, kuzengedwa mlandu, ndi kupezedwa ndi mlandu wa kupanduka. Mu 1536 ananyongedwa ndi kutenthedwa pamtengo. Nkosangalatsa chotani nanga kuona kuti Baibulo limene linkadedwa kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo tsopano lili pamtengo woterowo!
Mboni za Yehova zikuyesayesa moona mtima kupereka chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo kwa onse ochifunafuna. Kuwonjezera pa kusindikiza ndi kufalitsa matembenuzidwe ena, iwo atulutsa kuchokera ku zinenero zoyambirira matembenuzidwe a Baibulo lonse lathunthu limene lili lolondola ndi losavuta kuŵerenga. Podzafika mu 1995, makope oposa 74,000,000 a New World Translation of the Holy Scriptures imeneyi anafalitsidwa m’zinenero 12. Ndithudi, mtengo weniweni wa Baibulo lililonse ndiwo uthenga wake wopatsa moyo.
[Chithunzi patsamba 32]
William Tyndale
[Mawu a Chithunzi]
Chojambulidwa ku chithunzi chakale cha mu Bibliothèque Nationale