“Ndine Wamtengo Wapatali Pamaso pa Yehova!”
MU “NTHAŴI zoŵaŵitsa zovuta kuchita nazo” zino, atumiki a Yehova amapirira nkhondo yosatha yolimbana ndi malingaliro a kudziyesa opanda pake. (2 Timoteo 3:1, NW) Zimenezi si zodabwitsa, popeza amodzi a “machenjerero” a Satana ndiwo kutichititsa kulingalira kuti ndife osakondedwa, ngakhale ndi Mlengi wathu! (Aefeso 6:11) Nchifukwa chake, kope la Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995 linali ndi nkhani ziŵiri zophunzira mumpingo zakuti “Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!” ndi “Fulumizanani ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino—Motani?” Nkhani zimenezi zinalembedwa kutikumbutsa kuti Yehova amaŵerengera zoyesayesa zathu. Zotsatirapozi ndizo ndemanga zoyamikira zimene tinalandira:
“M’zaka zanga 27 monga mmodzi wa Mboni za Yehova sindinakhudzidwepo motere ndi magazini. Sindinathe kulimbikira ndipo ndinalira—nkhani zimenezi zinandipatsa mpumulo waukulu. Tsopano ndikumva kukhala wokondedwa kwambiri ndi Yehova. Zili ngati kuti chikatundu chachikulu chachotsedwa pamsana panga.”—C. H.
“Ndinaŵerenga magazini ameneŵa kanayi patsiku limodzi. Ndinasangalala ndi mmene nkhaniyo inanenera kuti munaphunzitsidwa bodza ngati mukhulupirira kuti muli opanda pake. Nkhani imeneyi ndidzaigwiritsira ntchito pamaulendo a ubusa ndi polalikira kukhomo ndi khomo.”—M. P.
“Satana wagwira ntchito yaikulu ya kuchititsa ngakhale aja omwe amakonda Yehova kumva kukhala opanda pake ndi osakondedwa. Kukumbutsidwa ndi gulu la ‘kapolo wokhulupirika’ kuti Yehova amatikonda kwambiri ndi kuti amayamikira tinthu tonse tating’ono timene timamchitira kuli chimodzi cha zinthu zolimbikitsa kwambiri zimene ndaŵerengapo. Kwa zaka zambiri ndinali ndi malingaliro omwe munafotokoza m’nkhanizi. Ndinaganiza kuti sindinali woyenerera chikondi cha Yehova, motero ndinayesa kuwonjezera zochita zanga mu utumiki kwa iye monga njira yopezera chikondicho. Koma liwongo ndi manyazi ndizo zimene zinandisonkhezera. Motero ngakhale ndinathera maola ambiri mu utumiki, kapena kuthandiza anthu ambiri, ndinaganiza kuti sizinali zokwanira. Zopereŵera zanga zokha nzimene ndinaona. Tsopano pamene nditumikira Yehova chifukwa cha chikondi, ndimalingalira kuti akumwetulira ndi kuti akusangalala nane. Zimenezi zimachititsa chikondi changa pa iye kukulirako ndipo zimandichititsa kufuna kuchita zochulukirapo. Tsopano ndili wachimwemwe kwambiri chifukwa cha utumiki wanga kwa Yehova.”—R. M.
“Zimenezi ndizo nkhani zabwino koposa, zolimbikitsa koposa, inde, zapadera zokhudza mtima zimene ndaŵerengapo! Kwa zaka 55 ndakhala ndikuŵerenga Nsanja ya Olonda, ndipo pakhala nkhani zapadera zambiri. Koma kope limeneli liposa lililonse limene tinakhalapo nalo lotithandiza kuchotsa zikayikiro zathu, nkhaŵa, ndi mantha akuti tili ‘opanda pake’ ndi ‘osakondedwa’ ndipo sitingathe kuchita zokwanira kuti ‘tipeze’ chikondi cha Yehova. Nsanja ya Olonda imeneyi ili ndi mtundu wa chithandizo chauzimu chimene abale athu akufunadi. Cholinga changa ndicho kugwiritsira ntchito nkhani zimenezi nthaŵi ndi nthaŵi pamaulendo aubusa.”—F. K.
“Kwa ife ena amene tikulimbana ndi kusadzidalira, kapena ngakhale ndi malingaliro a kudzida ife eni, kungakhale kovuta kwambiri kupeza nyonga kuti tipitirizebe m’choonadi. Nkhani imeneyi inasonyeza chifundo ndi kuzindikira kwakuya kwambiri kwakuti, inali ngati kupaka mankhwala otonthoza ndi ochiritsa ku mtima. Nkotonthoza chotani nanga kuŵerenga mawu ameneŵa mu Nsanja ya Olonda ndi kudziŵa popanda kukayikira kulikonse kuti Yehova amamvetsetsa! Zikomo kaamba ka kutikumbutsa kuti Yehova samayesa kusonkhezera anthu ake mwa kuwachititsa kumva kukhala aliwongo, manyazi, kapena mantha. Ngakhale kuti mbali yanga mu ntchito yolalikira yachepa kwambiri chifukwa cha mavuto a zandalama ndi matenda m’banja lathu, ndili wokhutirabe ndi zimene ndikwanitsa kuchita. Ndimaona kuti ndimakhala wachimwemwe kwambiri mu utumiki pamene ndimalola chikondi kukhala mphamvu yondisonkhezera.”—D. M.
“Ndangomaliza kumene kuŵerenga ‘Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!’ Ndime iliyonse inandiliritsa misozi. Ndinachokera ku banja limene silinasonyeze chikondi. Ndinachepetsedwa, kunyodoledwa, ndi kusekedwa. Motero, kuyambira paubwana ndinadziyesa wopanda pake. Ndidakali ndi malingaliro ozama akale amene amandichititsa tondovi pamene ndikumana ndi mavuto. Pamene ndinaleka kutumikira monga mkulu pa mpingo, monga mwa nthaŵi zonse ndinamva ngati wolephera—kwa Mulungu, banja langa, ndi abale anga mumpingo. Malingaliro ameneŵa samatha msanga, koma nkhani ya panthaŵi yake imeneyi yandithandiza kukhalanso wokhazikika. Yawongolera maganizo anga.”—D. L.
“Ndikuyamikani kaamba ka nkhani yakuti ‘Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!’ Ndikulimbana ndi kudzida kwakukulu ndi malingaliro akuya a kukhala wopanda pake, chifukwa cha kuchitiridwa nkhanza kwa paubwana. Kulidi koyenera kuona nkhani imeneyi monga machenjera a Satana iyemwini. Zingathetse ngakhale chifuno cha munthu cha kukhala ndi moyo. Tsiku lililonse ndimayesayesadi kulimbana ndi bodza lakuti sindili wokondedwa. Nkhaniyi ilidi yapadera kwa ine kuposa ndi mmene mungadziŵire.”—C. F.
“Lerolino abale amasonkhezeredwa makamaka ndi lingaliro lakuti Yehova amayamikira ntchito zochitidwa chifukwa cha chikondi m’malo mokakamizidwa. Kudziŵa za umunthu wa Yehova wosangalatsa ndi wachikondi, kukondwera kwake mwa anthu ake mmodzi ndi mmodzi, ndi kudzipereka kwake kwachikondi kumene amachita nkotonthoza ndi kolimbikitsa. Polingalira za zimenezi, pamene tinangolandira nkhani yakuti ‘Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!’ ambiri anayamikira. Kukuoneka kuti ikutsegulira ambiri njira yakuti akulitse unansi waumwini kwambiri ndi Yehova. Ine ndi mkazi wanga tikuyamikira kaamba ka malembedwe ake ndi mzimu wa kulingalira ena zimene zimakhala mu magazini a Nsanja ya Olonda aposachedwapa. Tikuyesayesa kugwiritsira ntchito zambiri za mfundozi pamene tichezera mipingo.”—Yochokera kwa woyang’anira woyendayenda.
“Ndakhala muŵerengi wokhulupirika kwa zaka pafupifupi 30, koma sindinaŵerengepo chilichonse chosonkhezera motero, cholimbikitsa motero. Malemba amphamvu, ogwiritsiridwa ntchito mwaluso andithandiza kuchotsa mabodza obisala m’malingaliro anga, zikumandithandiza kuyandikira pafupi ndi Yehova. Kwa zaka zambiri ndatumikira Yehova chifukwa cha kumva kukhala waliwongo. Ndinali ndi chidzŵitso cha m’mutu chabe ponena za dipo ndi chikondi cha Mulungu. Ndikuyamikani kaamba ka nkhani zopatsa chidziŵitso ndi zabwino zimenezi. Ndikhulupirira kuti ndidzaŵerenga zina zambiri zonga zimenezi.”—M. S.
“M’zaka zanga 29 zimene ndakhala m’choonadi, sindingakumbukire pamene nkhani inandichititsa kukhala ndi chiyamikiro chachikulu motero ndi kukhudzika mtima kwambiri. Ngakhale kuti ndinaleredwa ndi chikondi chachikulu ndi banja losamala, kukhala ndi moyo sikunakhalepo kwa tanthauzo kwa ine, ndipo ndinaganiza kuti sindili woyenera kutumikira Yehova. Pambuyo poŵerenga nkhani imeneyi, ndinagwada, ndipo ndi kusisima kwakukulu ndinayamika Yehova. Nkhaniyi ndidzaikonda kosatha. Ndidzadziona mosiyana ndi kale chifukwa tsopano ndikudziwa kuti ndili wamtengo wapatali pamaso pa Yehova.”—D. B.