“Musawatsekere Kunja!”
“NGATI mmodzi wa Mboni za Yehova, kapena ngakhale aŵiri, aliza belu lanu lapachitseko, musawatsekere kunja!” ikutero Corriere della Sera. Nyuzipepalayi inkanena za chochitika chimene chinachitika ku Treviso, kumpoto kwa Italy, kumene wamalonda wina akanataya ma lire oposa miliyoni imodzi (ndalama zoposa madola 600 a United States) chifukwa cha kupitikitsa Mboni ziŵiri zimene zinapita kukamuona.
Malinga ndi nyuzipepalayo, Mboni ziŵiri zinadzidziŵikitsa kwa mwamunayo ndi mawu akuti: “Lero ndi tsiku labwino kwa inu. Ndife Mboni za Yehova, ndipo tili ndi chinthu china chofunika choti tikupatseni.” Atamva zimenezo, wamalonda wopanda ubwenzi ameneyo anatseka chitseko, osawalola kutsiriza.
Mwamunayo akanamvetsera, akanazindikira kuti Mbonizo zinapita kunyumba kwake kukambwezera chikwama chake chandalama, chimene anapeza pa benchi ina ya m’paki. Chotero palibe chinanso chimene Mbonizo zikanachita choposa kupereka chikwamacho ndi zamkati mwake ku polisi yapafupi. Tsiku lotsatira, apolisi anachibwezera kwa mwini wakeyo.
“Wina wake akanakhala mumkhalidwe wa [Mboni] ziŵirizo zatsoka,” inatero Il Gazzettino di Treviso, “mwinamwake . . . akanasunga chuma chambiricho chamkati. Koma osati Mboni za Yehova, zimene ziyenera kukhala zokhulupirika kotheratu.”
Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera Mboni za Yehova kukhala “zokhulupirika kotheratu”? Ndi chikondi chawo cha Mulungu ndi mnansi, mogwirizana ndi ziphunzitso za Yesu Kristu. (Mateyu 22:37-39) Ndicho chifukwa chakenso Mboni za Yehova zimapita kunyumba ndi nyumba kukalengeza uthenga wabwino wonena za “dziko lapansi latsopano” labwino kwambirilo lolonjezedwa ndi Yehova Mulungu. Uthenga umenewu wa chiyembekezo ngofunika kwambiri koposa chinthu chakuthupi chilichonse!—2 Petro 3:13.