Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Malinga ndi malipoti a nyuzi, khanda litabadwa, zipatala zina zimasunga nsapo ndi ntchofu kuti atengeko zinthu m’mwazi wake. Kodi zimenezi ziyenera kumdetsa nkhaŵa Mkristu?
Kumadera ambiri, zimenezo sizimachitika konse, chotero Akristu sayenera kuda nkhaŵa. Ngati pali chifukwa chabwino chokhulupirira kuti kuchipatala chimene Mkristu adzabalirako amachita zimenezo, kungakhale bwino kungouza sing’anga kuti ataye nsapoyo ndi ntchofu, osazigwiritsira ntchito mwanjira iliyonse.
Mankhwala amitundumitundu atengedwa ku zinthu za m’thupi, la nyama kapena la munthu. Mwachitsanzo, mahomoni ena atengedwa ku mkodzo wa akavalo amimba. Kumwazi wa akavalo atengako katemera wa tetanus, ndipo kwanthaŵi yaitali gamma globulin, katemera wa matenda, atengedwa ku mwazi wa m’nsapo ya munthu. Zipatala zatenga nsapozo ndi kuziumika mwa kuziziziritsa ndipo pambuyo pake malaboletale a mankhwala azitenga kuti akayenge mwazi wokhala ndi zotetezera thupi zambiriwo ndi kuchotsako gamma globulin.
Posachedwapa, ofufuza anena kuti akhoza kugwiritsira ntchito mwachipambano mwazi wotengedwa ku nsapo pochiritsa mtundu wina wa leukemia, ndipo anena kuti mwazi woterowo angaugwiritsire ntchito pamatenda a dongosolo loteteza matenda m’thupi kapena m’malo mwa mafuta a m’fupa amene angaikidwe mwa wina. Chifukwa chake, kwamveka nkhani zina zakuti makolo alola kuchotsa mwazi ku nsapo, kuuumika mwa kuuziziritsa, ndi kuusunga kuti mwina ungadzagwire ntchito pochiritsa mwana wawo zaka zakutsogolo.
Kuyesa malonda mwazi wa kunsapo koteroko sikumakopa Akristu oona, amene amatsogoza maganizo awo ndi lamulo langwiro la Mulungu. Mlengi wathu amaona mwazi kukhala wopatulika, woimira moyo wopatsidwa ndi Mulungu. Ntchito yokha ya mwazi imene analola inali ya paguwa, yokhudza nsembe. (Levitiko 17:10-12; yerekezerani ndi Aroma 3:25; 5:8; Aefeso 1:7.) Kusiyapo apo, mwazi wochotsedwa ku cholengedwa anayenera kuuthira panthaka, kuufotsera.—Levitiko 17:13; Deuteronomo 12:15, 16.
Pamene Akristu asaka nyama kapena kupha nkhuku kapena nkhumba, amakhetsa mwazi ndi kuufotsera. Sikuti afunikira kuuthira panthaka penipeni, pakuti mfundo yake njakuti autaye m’malo mougwiritsira ntchito pazinthu zilizonse.
Akristu ogonekedwa m’chipatala amazindikira kuti zinthu za m’thupi zochotsedwa kwa iwo zimatayidwa, kaya ndi zam’chimbudzi, minofu yamatenda, kapena mwazi. Zoona, dokotala choyamba angafune kupima, monga ngati kupima mkodzo, kupima nthenda m’minofu yamfundo, kapena mwazi. Koma pambuyo pake, zinthuzo amakazitaya mogwirizana ndi malamulo akumaloko. Wodwala m’chipatala safunika konse kupereka mapempho apadera okhudza zimenezi chifukwa kuli koyenera ndiponso kwanzeru malinga ndi zamankhwala kuwononga zinthu zotero za m’thupi. Ngati wodwalayo ali ndi zifukwa zomveka zokayikirira kuti mwina njira yozoloŵerekayo sidzatsatiridwa, iyeyo angauze sing’angayo zimenezo, kumtchulira kuti pazifukwa zachipembedzo akufuna kuti zinthu zonse zotero zitayidwe.
Komabe, monga momwe tatchulira, zimenezi sizimadetsa nkhaŵa wodwala aliyense chifukwa kumadera ambiri samaganiza konse zosunga nsapo kapena zinthu zina za m’thupi kuti akazigwiritsirenso ntchito, ndipo si chizoloŵezi chawo ayi.
Nkhani yakuti “Tidane Nacho Choipa,” mu “Nsanja ya Olonda” ya January 1, 1997, inachita ngati inali kufotokoza za “pedophilia.” Kodi chizoloŵezi chimenechi chingatanthauzidwe motani?
Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary imatanthauzira “pedophilia” kuti “chilakolako chonyansa chogona ana.” Mbali za chizoloŵezi chimenechi zikutsutsidwa pa Deuteronomo 23:17, 18. Pamenepo Mulungu analetsa kuti pasakhale wachigololo wa pakachisi (“kapena, ‘mnyamata waganyu,’ mnyamata womsungira chilakolako chonyansa,” NW, mawu amtsinde). Mavesi ameneŵa akuletsanso aliyense kubweretsa “m’nyumba ya Yehova” mtengo wa “galu” (“mwina wogona anyamata, wogona ena kumatako, makamaka anyamata,” NW, mawu amtsinde). Maumboni a m’Malemba ameneŵa ndi akudziko akutsimikiza kuti Nsanja ya Olonda inali kufotokoza za munthu wamkulu woyesa mwana ngati wogonana naye, kuphatikizapo kumgwiragwira ndi chilakolako.