Kuona Mtima Mwamwaŵi Kapena Mosankha?
“NGAKHALE kuti mwachibadwa sindine woona mtima, nthaŵi zina ndimakhala wotero mwamwaŵi.” Akutero Autolycus wachinyengo mu The Winter’s Tale yolembedwa ndi William Shakespeare. Ichi chimasonyeza kufooka koyambirira kwa munthu, kufuna kwathu kuchita zoipa, zomwe zimachokera mu ‘mtima wonyenga.’ (Yeremiya 17:9; Salmo 51:5; Aroma 5:12) Koma kodi ichi chikutanthauza kuti tilibe mwina mochitira? Kodi khalidwe labwino limangochitika mwamwaŵi? Kutalitali!
Ana a Israyeli asanaloŵe Dziko Lolonjezedwa, Mose analankhula nawo atamanga misasa m’chigwa cha Moabu. Anaŵapatsa zosankha ziŵiri zomveka bwino. Anayenera kumvera malamulo a Mulungu ndi kulandira madalitso kapena kuwakana ndi kukolola zipatso zoŵaŵa za uchimo. (Deuteronomo 30:15-20) Kusankha kunali kwawo.
Monga anthu aufulu wodzisankhira, ifenso tiyenera kusankha. Palibe aliyense—kuphatikazapo Mulungu—amatikakamiza kuchita chabwino kapena kuchita choipa. Komabe ena angafunsedi kuti, ‘Ngati mitima yathu imafuna kuchita zoipa, kodi tingachite bwanji chabwino?’ Ee, dokotala wamano amayang’ana kuti aone kukungudzika kapena kuwola kwa mano zisanafike poipa. Mofananamo, tiyenera kuyang’ana mumtima wathu wophiphiritsira kufufuza zofooka ndi kuvunda kwa makhalidwe. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano,” anatero Yesu.—Mateyu 15:18-20.
Kuti asamale dzino, dokotala wa mano ayenera kuchotsa zowola zonse zimene wapeza. Mofananamo, kuganiza kokhazikira kufunika kuti tichotse “maganizo oipa” ndi zilakolako zoipa mumtima. Mwa kuŵerenga ndi kutsatira Mawu a Mulungu, Baibulo, sikuti timangofika pakudziŵa njira za Mlengi zokha komanso timaphunzira kuchita chomwe chiri chabwino.—Yesaya 48:17.
Davide, Mfumu ya Israyeli, anagwiritsira ntchito thandizo loyenera pankhondo yofuna kuchita chabwino. Iye anapemphera kuti: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga.” (Salmo 51:10) Inde, kudalira pa Yehova Mulungu mwapemphero, ifenso tingagonjetse chikhoterero chathu chofuna kuchita choipa ndi kukulitsa “mzimu watsopano” wochita chabwino. Mwanjira imeneyi, sitidzalekerera kuona mtima kungokhala kwa mwamwaŵi. Kudzakhala kochita kusankha.
[Chithunzi patsamba 21]
Monga momwe zinalili ndi Davide, pemphero kwa Yehova lingatithandize kuchita zabwino