“Ndani Analonga Nzeru m’Mitambomo?”
“PAMENE pali ponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero. Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.” Mawu a Yesuwa, olembedwa ndi wolemba Uthenga Wabwino Luka, ndiwo zitsanzo za kudziŵiratu za nyengo kumene anthu anali kukuchita ku Palestina wakale. (Luka 12:54, 55) Nthaŵi zina, anthu akale anali kuneneratu kutatsala pang’ono kuti zinthuzo zichitike mwa kuyang’ana zizindikiro.
Lerolino, odziŵa za nyengo amagwiritsira ntchito ziŵiya zamphamvu kwambiri monga masetilaiti ozungulira dziko lapansi, Doppler radar, ndi makompyuta ena amphamvu, kuti adziŵiretu za nyengo masikuwo asanafike. Koma nthaŵi zambiri amalakwitsa. Chifukwa chiyani?
Pali zambiri zimene zimapangitsa kudziŵiratu za nyengo kukhala kovuta. Mwachitsanzo, kusintha kwa temperecha kwadzidzidzi, chinyontho cha mumpweya, mphamvu ya mpweya, ndiponso liŵiro la mphepo ndi kumene mphepoyo ikuchokera ndi kumene ikupita. Ndiponso pali kugwirizana kwa dzuŵa, mitambo, ndi nyanja kumene asayansi sakukumvetsabe. Pachifukwa chimenecho, sayansi yodziŵiratu za nyengo imangoyerekezera.
Chidziŵitso chochepa cha munthu ponena za nyengo chikutikumbutsa za mafunso amene Yobu anafunsidwa kuti: “Wabala ndani madontho a mame? Chipale chinatuluka m’mimba ya yani? . . . Kodi udziŵa kukwezera mawu ako kumitambo, kuti madzi ochuluka akukute? . . . Ndani analonga nzeru m’mitambomo? Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha? Adziŵa ndani kuŵerenga mitambo mwanzeru, ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani?”—Yobu 38:28-37.
Yankho la mafunso onsewa ndilo, Osati munthu koma Yehova Mulungu. Inde, anthu kaya asonyeze nzeru zotani, nzeru za Mlengi wathu nzazikulu kuposa ponsepo. Nchikondi chake chachikuludi kuti watipatsa nzeru zake m’masamba a Baibulo, kuti tipange njira yathu kukhala yachipambano.—Miyambo 5:1, 2.