Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano—Monga Kunanenedwera
“Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, . . . mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona.”—CHIVUMBULUTSO 21:5.
1, 2. N’chifukwa chomveka chotani chimene anthu ambiri amazengerezera kuneneratu zam’tsogolo?
KODI munanenapo kapena kuganizapo kuti, ‘Adziŵa zamaŵa ndani?’ Mukhoza kumvetsa chifukwa chake anthu amazengereza kuneneratu zam’tsogolo kapena kukhulupirira aja amene anganene monyadira kuti amatha kulosera zam’tsogolo. Kunena mwachidule, anthu sakhoza kuneneratu molondola zimene zingachitike m’miyezi kapena zaka zam’tsogolo.
2 Magazini yotchedwa Forbes ASAP inali ndi nkhani imene inafotokoza za nthaŵi. Mmenemo, Robert Cringely, wosimba zochitika m’nkhani ya pa TV analemba kuti: “Potsirizira pake, nthaŵi imatinyazitsa, koma amene amavutika koposa onse pankhani ya nthaŵi ndi aja amene amayesa kulosera zam’tsogolo. Kuyesa kulosera zam’tsogolo ndi seŵero limene nthaŵi zambiri timalephera. . . . Chikhalirechobe, otchedwa akatswiriwo akupitirizabe kulosera zam’tsogolo.”
3, 4. (a) Kodi anthu ena ali ndi chidaliro chotani ponena za meleniyamu yatsopano? (b) Koma kodi ena akuyembekezera zenizeni zotani ponena zam’tsogolo?
3 Mwina inunso mwaona kuti pamene anthu ambiri akulankhula za chaka chatsopano cha meleniyamu, zikuoneka ngati kuti anthu ambiri akuganiza zam’tsogolo. Kumayambiriro kwa chaka chatha, magazini yotchedwa Maclean’s inati: “Chaka cha 2000 chingangokhala ngati chaka china chilichonse cha pakalendala kwa anthu ambiri a ku Canada, koma chikhoza kupezananso mwamalunji ndi chiyambi chinachake chatsopano.” Pulofesa Chris Dewdney wa pa York University anapereka chifukwa chokhalira ndi chidaliro kuti: “Meleniyamu idzatanthauza kuwonjoka ku zaka zana limodzi zoipitsitsa.”
4 Kodi zimenezo zikumveka ngati nkhambakamwa chabe? Mu Canada, 22 peresenti yokha ya anthu amene anayankha pakafukufuku wina ndiwo “amakhulupirira kuti chaka cha 2000 chidzabweretsa chiyambi chatsopano cha dziko.” Ndi iko komwe, pafupifupi theka la anthuwo “akuyembekezera mkangano winanso wa padziko lonse”—nkhondo ya padziko lonse—m’kati mwa zaka 50. Mwachionekere, anthu ochuluka akuona kuti meleniyamu yatsopano singathetse mavuto athu, ndi kupanga zinthu zonse kukhala zatsopano. Bwana Michael Atiyah, pulezidenti wakale wa bungwe lotchedwa Britain’s Royal Society, analemba kuti: “Kusintha kofulumiraku . . . kumatanthauza kuti zaka za 2000 zidzafika ndi mavuto aakulu pa chitukuko chathu chonse. Mavuto a kuchuluka kwa anthu, kusoŵa zofunika pamoyo, kuwonongeka kwa malo, ndi kufalikira kwa umphaŵi atipeza kale ndipo tiyenera kulimbana nawo mwachangu.”
5. Kodi n’kuti kumene tingapezeko chidziŵitso chodalirika cha zimene zili m’tsogolo?
5 Mungalingalire kuti, ‘Popeza anthu sangathe kudziŵiratu zam’tsogolo, kodi sitingachite bwino kungoiŵala zam’tsogolo?’ Yankho n’lakuti “ayi!” N’zoona kuti anthu sangalosere molondola zam’tsogolo, koma tisaganize kuti palibe amene angathe. Eya, nanga amene angatheyo ndani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidaliro ponena za tsogolo? Mutha kupeza mayankho okhutiritsa m’maulosi osiyanasiyana anayi. Maulosiwo alembedwa m’buku lopezeka ndi anthu ochuluka ndiponso loŵerengedwa kwambiri kuposa lina lililonse, limenenso lili lomvedwa molakwa ndi anthu ambiri ndi lonyalanyazidwa kwambiri—Baibulo. Kaya maganizo a anthu ndi otani ponena za Baibulo, ndipo ngakhale mungalidziŵe bwino chotani, n’kwaphindu kwa inu kuti mupende malemba anayi ofunika ameneŵa. Iwo amaneneratu za tsogolo losangalatsa kwambiri. Ndiponso, maulosi ofunika anayiŵa amapereka chithunzi cha mmene tsogolo lanu ndi la okondedwa anu lidzakhalire.
6, 7. Ndi liti pamene Yesaya anapereka ulosi wake, ndipo zolosera zake zinakwaniritsidwa mochititsa chidwi motani?
6 Woyamba umapezeka pa Yesaya chaputala 65. Tisanauŵerenge, taikani m’maganizo chithunzi chake—ndiko kuti nthaŵi pamene ulosiwu unalembedwa ndi mkhalidwe umene ukufotokozedwamo. Yesaya mneneri wa Mulungu, amene analemba mawuŵa, anakhalapo ndi moyo kudakali zaka zoposa 100 ufumu wa Yuda usanathe. Ufumuwo unatha pamene Yehova anachotsa chitetezo chake pa Ayuda osakhulupirikawo, akumalola Ababulo kusakaza Yerusalemu ndi kutengera anthu ake ku ukaidi. Zimenezo zinadzachitika patapita zaka zoposa 100 kuchokera pamene Yesaya anazilosera.—2 Mbiri 36:15-21.
7 Ponena za mbiri ya kukwaniritsidwa kwake, kumbukirani kuti Yesaya potsogoleredwa ndi Mulungu, ananeneratu dzina la Mperisiya wodzabadwa, Koresi, amene potsirizira pake anagonjetsa Babulo. (Yesaya 45:1) Koresi analambula njira kuti Ayuda abwerere kudziko lakwawo mu 537 B.C.E. Chosangalatsa n’chakuti, Yesaya ananeneratu za kubwezeretsedwa kumeneko, monga timaŵerengera pa Yesaya chaputala 65. Iye anafotokoza mikhalidwe imene Aisrayeliwo akasangalala nayo m’dziko lakwawolo.
8. Kodi Yesaya ananeneratu za tsogolo labwino lotani, ndipo ndi mawu ati amene tikufuna kuwasamala?
8 Pa Yesaya 65:17-19 timaŵerenga kuti: “Taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa. Ndipo ndidzasangalala m’Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mawu akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mawu akufuula.” Ndithudi, Yesaya anafotokoza mikhalidwe imene inali yabwino kwambiri kuposa mmene Ayudawo anali kukhalira ku Babulo. Iye ananeneratu za kusangalala ndi kukondwa. Tsopano taonani mawuwo akuti “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Aka ndi koyamba panthaŵi zinayi zimene mawuŵa akuonekera m’Baibulo, ndipo mawu anayi ameneŵa angakhudze mwachindunji tsogolo lathu, ngakhalenso kuperekeratu chithunzi chake.
9. Kodi Ayuda akale anaphatikizidwa motani m’kukwaniritsidwa kwa Yesaya 65:17-19?
9 Kukwaniritsidwa koyambirira kwa Yesaya 65:17-19 kunakhudza Ayuda akalewo, amene malinga ndi kunenera kolondola kwa Yesaya, anabwereradi kudziko lakwawo, kumene anakhazikitsanso kulambira koyera. (Ezara 1:1-4; 3:1-4) Inunso mukudziŵa kuti malo kumene anabwererako ndi pompano padziko lapansi, osati kumalo ena alionse kumwamba. Mfundo imeneyo ingatithandize kuona zimene Yesaya anatanthauza potchula kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Tisayese n’komwe kusinkhasinkha, ngati mmene ena achitira, za maulosi osadziŵika bwino a munthu wina wotchedwa Nostradamus kapena zolosera za anthu ena. Baibulo palokha limamveketsa bwino zimene Yesaya anatanthauza.
10. Kodi “dziko lapansi” latsopano limene Yesaya ananeneratu liyenera kutanthauza chiyani kwa ife?
10 M’Baibulo, si nthaŵi zonse pamene mawu akuti “dziko lapansi” amatanthauza mbulunga yathuyi. Mwachitsanzo, Salmo 96:1 limanena kuti: “M’yimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.” Timadziŵa kuti pulaneti lathuli—mtunda ndi nyanja zake—silingathe kuimba ayi. Amaimba ndi anthu. Inde, Salmo 96:1 akunena za anthu a padziko lapansi.a Koma Yesaya 65:17 amatchulanso “kumwamba kwatsopano.” Ngati “dziko lapansi” linaimira chikhalidwe chatsopano cha anthu m’dziko la Ayuda, nanga “kumwamba kwatsopano” n’chiyani?
11. Kodi mawu akuti “kumwamba kwatsopano” anatanthauza chiyani?
11 Buku lotchedwa Cyclopædia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, lolembedwa ndi M’Clintock ndi Strong, limati: “Nthaŵi zonse pamene mawu akuti kumwamba atchulidwa m’masomphenya aulosi, amatanthauza . . . gulu lonse la olamulira . . . okhala pamwamba ndi kulamulira anthu awo, monga mmene kumwamba kwenikweniko kuliri pamwamba ndipo kulamulira dziko lapansi.” Pokamba za mawu ophatikiza akuti “kumwamba ndi dziko lapansi,” Cyclopædia imanena kuti ‘m’chilankhulo chaulosi mawuwo amatanthauza malo a anthu osiyanasiyana m’nkhani zandale. Kumwamba kumaimira olamulira; dziko lapansi limaimira olamulidwa, ndiwo anthu olamulidwa ndi akuluakulu audindo.’
12. Kodi Ayuda akale anakhala motani ndi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano”?
12 Ayudawo atabwerera kudziko lakwawo, anakhala ndi chimene tingati dongosolo latsopano la zinthu. Anakhala ndi bungwe lolamulira latsopano. Zerubalele, mbadwa ya Mfumu Davide, ndiye anali mtsogoleri, ndipo Yoswa anali mkulu wa ansembe. (Hagai 1:1, 12; 2:21; Zekariya 6:11) Ameneŵa ndiwo anali “kumwamba kwatsopano.” Kodi anali pamwamba pa chiyani? “Miyamba yatsopano” inali pamwamba pa “dziko lapansi latsopano,” anthu oyeretsedwa amene anabwezeretsedwa kudziko lakwawo kuti akamangenso Yerusalemu ndi kachisi wake wolambiriramo Yehova. Choncho, m’ganizo lenileni limeneli, panali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano m’kukwaniritsidwa kumeneko kochitika pa Ayuda panthaŵiyo.
13, 14. (a) Kodi ndi malemba ena ati amene amatchula mawu akuti “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” amene tiyenera kuwapenda? (b) N’chifukwa chiyani ulosi wa Petro uli wapadera m’nthaŵi yathu ino?
13 Koma samalani kuti musaphonye mfundo yake. Kumeneku sikungofuna kuyesa luso la kumasulira Baibulo kapena kungofuna kuona chabe zochitika za m’mbiri yakale. Mutha kuonanso zimenezi mwa kupitanso ku mbali zina kumene timapezanso mawu akuti “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano.” Pa 2 Petro chaputala 3, mudzapezapo mawu ameneŵa ndipo mudzaona kuti akukhudza tsogolo lathu.
14 Mtumwi Petro analemba kalata yake pafupifupi zaka 500 chibwerereni Ayudawo kudziko lakwawo. Monga mmodzi wa atumwi a Yesu, Petro anali kulembera otsatira a Kristu, “Mbuye” wotchulidwa pa 2 Petro 3:2. M’vesi 4, Petro akutchula za “kudza” kwa Yesu, kumene kukuchititsa ulosiwu kukhala wofunika kwambiri lerolino. Umboni wokwanira ukusonyeza kuti chichitikireni nkhondo yoyamba ya padziko lonse, Yesu wakhala alipo m’lingaliro lakuti ali ndi mphamvu monga Wolamulira wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 6:1-8; 11:15, 18) Zimenezi zilinso ndi tanthauzo lina lapadera lokhudza mbali ina imene Petro ananeneratu m’chaputala chimenechi.
15. Kodi ulosi wa Petro wonena za “miyamba yatsopano” ukukwaniritsidwa motani?
15 Pa 2 Petro 3:13 timaŵerenga kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.” Mwina mukudziŵa kale kuti Yesu kumwambako ndiye Wolamulira wamkulu mu “miyamba yatsopano.” (Luka 1:32, 33) Komabe, malemba ena m’Baibulo amasonyeza kuti iye sakulamulira yekha. Yesu analonjeza kuti atumwiwo ndi ena ofanana nawo adzakhala ndi malo kumwamba. M’buku la Ahebri, mtumwi Paulo ananena oterowo kukhala ‘olandira nawo maitanidwe akumwamba.’ Ndipo Yesu ananena kuti a m’gulu limeneli akakhala pamipando yachifumu kumwamba limodzi naye. (Ahebri 3:1; Mateyu 19:28; Luka 22:28-30; Yohane 14:2, 3) Mfundo n’njakuti alipo ena omwe akulamulira limodzi ndi Yesu monga mbali ya miyamba yatsopano. Nangano n’chiyani chimene Petro anatanthauza ndi mawu akuti “dziko lapansi latsopano”?
16. Kodi ndi “dziko latsopano” liti limene lilipo kale?
16 Mofanana ndi kukwaniritsidwa kwakale—ndiko kubwerera kwa Ayuda kudziko lakwawo—kukwaniritsidwa kwatsopano kwa 2 Petro 3:13 kukuphatikizapo anthu amene amagonjera ulamuliro wa miyamba yatsopano. Mutha kupeza mamiliyoni lero amene akugonjera mosangalala ulamuliro umenewo. Iwo akupindula ndi pulogalamu yake ya maphunziro ndipo akuyesetsa kutsatira malamulo ake a m’Baibulo. (Yesaya 54:13) Amenewo amapanga maziko a “dziko lapansi latsopano” m’ganizo lakuti akupanga chikhalidwe cha padziko lonse cha mitundu yonse, zinenero, ndi mafuko, ndipo amagwira ntchito pamodzi pogonjera Mfumu yolamulirayo, Yesu Kristu. Mfundo yofunika kwambiri n’njakuti inunso mutha kukhala mbali yake!—Mika 4:1-4.
17, 18. N’chifukwa chiyani mawu a pa 2 Petro 3:13 akutipatsa chifukwa choyang’anira m’tsogolo?
17 Koma musaganize kuti zonse zathera pomwepa, kuti sitikudziŵa zilizonse ponena za m’tsogolo. Kwenikweni, pamene mupenda nkhani ya pa 2 Petro chaputala 3, mudzaona zizindikiro za kusintha kwakukulu kumene kuli m’tsogolomu. M’vesi 5 ndi 6, Petro akulemba za tsiku la Chigumula cha Nowa, Chigumula chimene chinathetsa dziko loipa m’nthaŵi yakaleyo. M’vesi 7, Petro akutchula kuti “miyamba ndi dziko la masiku ano,” ponse paŵiri olamulira ndi anthu olamulidwa, akusungidwira ‘tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.’ Zimenezi zimatitsimikizira kuti mawu akuti “miyamba ndi dziko la masiku ano” satanthauza kumwamba kwenikweniko, koma anthu ndi olamulira awo.
18 Kenako Petro akufotokoza kuti patsiku la Yehova likudzalo padzakhala kuyeretsa kwakukulu, kutsegulira njira miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zotchulidwa pavesi 13. Taonani mawu otsirizira a vesilo—“m’menemo mukhalitsa chilungamo.” Kodi mawuŵa sakusonyeza kuti padzakhala kusintha kwakukulu kokonza zinthu? Kodi sakudzutsa chiyembekezo cha zinthu zatsopano, nthaŵi pamene anthu adzapeza chisangalalo chachikulu m’moyo kusiyana ndi mmene akukhalira lero? Ngati mukutha kuona zimenezo, ndiye kuti mwazindikira zimene Baibulo limaneneratu, kuzindikira kumene kuli ndi anthu ochepa okha.
19. Ndi mumkhalidwe wotani umene buku la Chivumbulutso likusonyezera “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” zimene zikubwera?
19 Koma tiyeni tipitirire pamenepo. Taona kupezeka kwa mawu akuti ‘kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano’ pa Yesaya chaputala 65 komanso pa 2 Petro chaputala 3. Tsopano tsegulani pa Chivumbulutso chaputala 21, pamene timapezanso mawu enanso ameneŵa m’Baibulo. Apanso, kuzindikira nthaŵi pamene nkhaniyi inalembedwa ndi mkhalidwe wofotokozedwamo kudzathandiza kwambiri. Kubwerera kumbuyo machaputala aŵiri, Chivumbulutso chaputala 19, akufotokoza nkhondo mwa zizindikiro zomvekera bwino—koma osati nkhondo yapakati pa mitundu yachidani ayi. Kumbali ina kuli “Mawu a Mulungu.” Mwachionekere, mwazindikira kuti limeneli ndi dzina laulemu la Yesu Kristu. (Yohane 1:1, 14) Iye ali kumwamba, ndipo masomphenya ameneŵa akusonyeza iye limodzi ndi magulu ankhondo akumwamba. Kodi akulimbana ndi yani? Chaputalacho chikutchula “mafumu,” “akapitawo” ankhondo, ndi anthu a maudindo osiyanasiyana, ponse paŵiri “aang’ono ndi aakulu.” Nkhondo imeneyi imaphatikizapo tsiku likudzalo la Yehova, pamene zoipa zonse zidzawonongedwa. (2 Atesalonika 1:6-10) Popitiriza, Chivumbulutso chaputala 20 chimayamba ndi kufotokoza za kuchotsedwa kwa “njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana.” Zimenezi zikutsegulira bwalo makambirano a Chivumbulutso chaputala 21.
20. Kodi Chivumbulutso 21:1 chimasonyeza kuti patsogolopa pali kusintha kwakukulu kotani?
20 Mtumwi Yohane akuyamba ndi mawu ochititsa chidwi aŵa: “Ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.” Malinga ndi zimene taona pa Yesaya chaputala 65 ndi 2 Petro chaputala 3, tiyenera kukhala otsimikiza kuti zimenezi sizikutanthauza kuchotsa miyamba yeniyeniyo ndi dziko lathuli, limodzi ndi nyanja zake. Monga momwe machaputalawo asonyezera, anthu oipa ndi olamulira awo, kuphatikizapo wolamulira wosaonekayo Satana, onse adzachotsedwa. Inde, lonjezo pano ndilo la dongosolo la zinthu latsopano lophatikizapo anthu padziko lapansi.
21, 22. Ndi madalitso otani amene Yohane akutitsimikizira, ndipo kupukuta misozi kumene akunenako kukutanthauza chiyani?
21 Timakhala otsimikizira za zimenezo pamene tipenda ulosi wochititsa chidwi umenewu. Mawu otsirizira a vesi 3 amakamba za nthaŵi pamene Mulungu adzakhala ndi anthu, powacheukira mokoma mtima anthu ochita chifuniro chake. (Ezekieli 43:7) Yohane akupitiriza m’mavesi 4, 5 kuti: “[Yehova] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona.” Ha, kulimbikitsa kwake ulosi umenewu!
22 Imani kaye ndi kusinkhasinkha pa zabwino zimene Baibulo likuneneratu. ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse kuichotsa m’maso mwawo.’ Imeneyi singakhale misozi yeniyeni imene imatuluka m’maso mwathu, ndipo singakhalenso misozi yachisangalalo. Koma misozi imene Mulungu adzapukuta ndi ija yochititsidwa ndi mavuto, chisoni, kugwiritsidwa fuŵa lamoto, kupwetekedwa, ndi kuŵaŵidwa mtima. Kodi tingatsimikize motani zimenezo? Eya, lonjezo lodabwitsa la Mulungu limeneli limagwirizanitsa kupukuta misozi kumeneku ndi kuchotsedwa kwa ‘imfa, maliro, kulira, ndi zoŵaŵitsa.’—Yohane 11:35.
23. Kodi ulosi wa Yohane ukutsimikizira za kutha kwa mikhalidwe yotani?
23 Kodi zimenezi sizikutsimikizira kuti matenda ngati kansa, sitiroko, mtima, ngakhalenso imfa zidzachotsedwa? Ndani mwa ife amene sanatayikidwepo wokondedwa wake chifukwa cha matenda, ngozi, kapena tsoka? Mulungu panopa akulonjeza kuti imfa idzachotsedwa, zimene zikutanthauza kuti ana amene angadzabadwe panthaŵiyo sadzakhala ndi chiyembekezo chakuti akakula, adzakalamba—kenako n’kuthera mu imfa. Ulosi umenewu umatanthauzanso kutha kwa matenda obwera ndi ukalamba monga nthenda yochititsa kuiŵalaiŵala, nthenda yofooketsa mafupa, matudza am’chiberekero, khungu, ngakhale ng’ala—zofala kwambiri mwa okalamba.
24. Kodi ‘kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano’ zidzakhala motani dalitso, komano tidzapendabe za chiyani?
24 Ndithudi, inunso mudzavomereza kuti maliro ndi kulira zidzachepa pochotsedwa imfa, ukalamba ndi matenda. Komabe, bwanji nanga za njala yosautsa, nkhanza kwa ana, ndi tsankho loponderezana chifukwa cha maonekedwe a khungu? Zinthu zoterozo—zofala lerolino—zitati zipitirire, maliro ndi kulira sizingathe. Choncho, moyo pansi pa “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” sudzaipitsidwa ndi zinthu zodzetsa chisoni zilipozi. Ha, kusintha kwake! Ngakhale ndi tero, tangokambirana malo atatu okha m’Baibulo opezekapo mawu akuti ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.’ Patsala malo amodzi pamene mawuwo akugwirizana ndi zimene tapendazo amenenso akugogomeza chifukwa chake tiyenera kukhala ndi chiyembekezo cha nthaŵi pamene Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake la ‘kupanga zinthu zonse kukhala zatsopano’ ndi mmene ati adzachitire zimenezo. Nkhani yotsatira ikufotokoza ulosi umenewo ndi mmene ungatipatsire chimwemwe.
[Mawu a M’munsi]
a The New English Bible limati pa Salmo 96:1: “Imbirani AMBUYE, anthu onse a padziko lapansi!” The Contemporary English Version limati: “Aliyense padziko lapansi, aimbe zitamando kwa AMBUYE.” Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yakuti Yesaya potchula “dziko lapansi latsopano” anali kutanthauza anthu a Mulungu m’dziko lakwawo.
Kodi Mukukumbukira Chiyani?
• Ndi malo atatu ati pamene Baibulo limaneneratu za ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano’?
• Kodi Ayuda akale anaphatikizidwa motani m’kukwaniritsidwa kwa ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano”?
• Kodi “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zimatanthauzanji malinga ndi Petro?
• Kodi Chivumbulutso chaputala 21 chimatisonyeza motani tsogolo labwino?
[Chithunzi patsamba 10]
Monga ananenera Yehova, Koresi analambula njira kuti Ayuda abwerere kudziko lakwawo mu 537 B.C.E.