Ntchito Zabwino Zimabweretsa Chitamando kwa Mulungu
AMENE amakonda Mulungu amayesetsa kusonyeza kuŵala kwa uzimu kopezeka m’Mawu ake, Baibulo. Mwanjira imeneyi, iwo amatsatira lamulo la Yesu lakuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa kumwamba.” (Mateyu 5:16) Zolankhula komanso kuchita zinthu zolungama kungabweretse ulemerero kwa Mulungu.
Mboni za Yehova zimayesetsa kukondweretsa Mulungu mwakuchita zinthu mogwirizana ndi Baibulo komanso mwakuyesetsa kuthandiza ena mwauzimu. Zimachita zimenezo ngakhale m’mayiko amene kulalikira kwawo sikunalembetsedwebe mwalamulo. Ku likulu lina la mayiko ameneŵa, Mboni zakhala zikuchititsa misonkhano yachigawo kumene kumasonkhana anthu okwana 6,000 kapena mpaka 9,000. Mbonizo zakhala zikubwereka maholo pa malo achionetsero kaamba ka misonkhano imeneyi. Monga momwe zinachitira zaka zapita, zisanachite msonkhano wawo wachigawo mu 1999, Mboni mazanamazana zinagwira ntchito molimbika kuyeretsa malo ndi kukonza zokuzira mawu komanso mipando zikwizikwi.
Kukonzekera konseku sikunathe mosazindikirika. Akuluakulu ogwira ntchito yoyang’anira malowo anaona ntchito zimenezi. Anaonanso kuti, ngakhale panali chiŵerengero chapamwamba cha 15,666, zinthu zinayenda bwino ndipo Mboni zinachita zinthu mwadongosolo. Pambuyo pake oyang’anira bwalowo anachita chidwi kwambiri ndi kuyeretsa kosasiyako kachinyalala kalikonseko.
Akuluakulu oyang’anirawo anayamikira chifukwa cha ntchitoyi mwa kuika Mbonizo pandandanda yawo kuti ndiwo adzakhale oyamba kubwereka nyumbayi chaka chotsatira. Koma oyang’anirawo sanalekere pamenepo. Pa July 15, 1999, anapereka mphoto yoyamikira kwa Komiti ya Msonkhano Wachigawo. Mawu olembedwa pa mphoto yosonyeza kuyamikirayo anali akuti: “mpingo wa Mboni za Yehova.” Ichitu n’chinthu chosayembekezeka chifukwa m’dzikoli ntchito yawo yophunzitsa Baibulo n’njoletsedwa.
Kuzungulira dziko lonse lapansi mu 2000/2001, anthu mamiliyoni akuyembekezeka kukamvetsera Misonkhano Yachigawo mazanamazana ya Mboni za Yehova ya mutu wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu.” Mwakupezekapo, mungadzionere nokha mmene anthu amene amachita mwakhama zimene Baibulo limanena amachitira ntchito zabwino zimene zimabweretsa chitamando kwa Mulungu.