‘Khululukiranani’
KODI mumakhulupirira kuti Mulungu wakukhululukirani machimo anu? Zikuoneka kuti anthu achikulire ambiri ku United States amakhulupirira zimenezi. Dr. Loren Toussaint, yemwe anayambitsa kafukufuku amene anachitika pa yunivesite ya Michigan Institute for Social Research ananena kuti, pa anthu 1,423 a ku America amene anafunsidwa funso limeneli, pafupifupi anthu 80 pa anthu 100 alionse a zaka zoposa 45 anayankha kuti Mulungu wawakhululukira machimo awo.
Komabe, chochititsa chidwi n’chakuti pa anthu ameneŵa, anthu 57 okha pa anthu 100 alionse ananena kuti amakhululukira anthu ena. Zimenezi zikutikumbutsa mawu a Yesu pa ulaliki wa pa phiri, akuti: “Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.” (Mateyu 6:14, 15) Inde, chimodzi mwa zinthu zimene zimachititsa Mulungu kutikhululukira machimo anthu ndicho kufunitsitsa kwathu kukhululukira ena.
Mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu a ku Kolose mfundo ya makhalidwe abwino imeneyi. Anawalimbikitsa kuti: “[Pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Inde, nthaŵi zina zimenezi zimavuta kuchita. Mwachitsanzo, ngati wina wakulankhulani mawu okhumudwitsa kapena oipa, kungakhale kovuta kumukhululukira.
Komabe, kukhululukira anthu ena kumapindulitsa zedi. Dr. David R. Williams, katswiri woona za khalidwe la anthu, anafotokoza za kafukufuku wake kuti: “Tinapeza kuti anthu a ku America a zaka zoyambira 40 kupita m’tsogolo amene mitu yawo imayenda bwino ndi amene amakhululuka.” Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a mfumu yanzeru Solomo, imene inalemba zaka 3,000 zapitazo kuti: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30) Popeza kukhululukira kumalimbikitsa ubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso ndi anansi athu, tili ndi zifukwa zabwino zokhululukira ena kuchokera mu mtima.—Mateyu 18:35.