Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
• Kodi Lusifara ndi dzina limene Baibulo limagwiritsa ntchito kunena Satana?
Dzina lakuti Lusifara limapezeka kamodzi kokha m’Malemba ndiponso m’mabaibulo ena osati onse. Mwachitsanzo, Baibulo la King James Version linamasulira Yesaya 14:12 kuti: “Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe Lusifara, mwana wa m’maŵa!”
Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “Lusifara” limatanthauza “wowala.” Baibulo la Septuagint limagwiritsa ntchito liwu la Chigiriki limene limatanthauza kuti “wobweretsa mbandakucha.” N’chifukwa chake, mabaibulo ena amamasulira liwu la Chihebrilo kuti “nthanda.” Koma Baibulo la chilatini lotchedwa Vulgate la Jerome limagwiritsa ntchito dzina loti “Lusifara” (wonyamula kuunika), ndipo zimenezi n’zomwe zachititsa kuti liwu limeneli lizipezeka m’mabaibulo ena.
Kodi Lusifara ameneyu ndi ndani? Mawu akuti “wowala,” kapena kuti “Lusifara,” akupezeka m’mawu amene Yesaya analamula Aisrayeli mwaulosi kuti alengeze monga ‘nyimbo yanchinchi yoimbira mfumu ya ku Babulo.’ Motero, mawuwo ndi mbali ya nyimbo imene kwenikweni anaimbira mzera wa mafumu a ku Babulo, kuyambira pa Nebukadinezara. Umboni winanso wakuti mawu akuti “wowala” akunena za munthu osati cholengedwa chauzimu tikuuona m’mawu akuti: “Udzatsitsidwa kunsi ku manda.” Kumanda ndi kumene anthu onse amapita, osati malo a Satana Mdyerekezi. Ndiponso, amene anaona Lusifara akutsitsidwira kumanda anafunsa kuti: ‘Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi?’ N’zoonekeratu apa kuti “Lusifara” amanena za munthu, osati cholengedwa chauzimu.—Yesaya 14:4, 15, 16.
N’chifukwa chiyani anagwiritsa ntchito mawu odziŵika amenewo pofotokoza za mafumu a ku Babulo? Tiyenera kudziŵa kuti mfumu ya ku Babulo anaitcha wowala moiseka pambuyo poti yagwa. (Yesaya 14:3) Kunyada ndiponso dyera zinkachititsa mafumu a Babulo kudzikweza pa mafumu ena amene anali nawo pafupi. Mafumu awo onse anali odzikweza kwambiri moti akuti anali kudzitama kuti: “Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu [“losonkhanira,” NW], m’malekezero a kumpoto; . . . ndidzafanana ndi Wam’mwambamwamba.”—Yesaya 14:13, 14.
“Nyenyezi za Mulungu” ndi mafumu a banja la chifumu la Davide. (Numeri 24:17) Kuyambira pa Davide, “nyenyezi” zimenezi zinali kulamulira zili ku phiri la Ziyoni. Solomo atamanga kachisi ku Yerusalemu, anthu anayamba kugwiritsa ntchito dzina loti Ziyoni kunena mzinda wonsewo. M’pangano la Chilamulo, amuna onse achiisrayeli ankayenera kupita ku Ziyoni katatu pachaka. Motero, Ziyoni anakhala “phiri losonkhanira.” Mwa kutsimikiza mtima kugonjetsa mafumu achiyuda ndi kuwachotsa pa phiri limeneli, Nebukadinezara anasonyeza cholinga chake chofuna kudzikweza pamwamba pa “nyenyezi” zimenezi. M’malo motamanda Yehova chifukwa cha kugonjetsa mafumu ameneŵa, iye mwamatama anadziona ngati Yehova. Motero, mzera wa mafumu a ku Babulo mouseka anautcha kuti “wowala” pambuyo poti wagwa.
Kudzikuza kwa olamulira a ku Babulo kunaonetsadi mtima wa “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 4:4) Iyenso amafuna ulamuliro ndipo amalakalaka atadzikweza kuposa Yehova Mulungu. Koma Lusifara si dzina limene Malemba amagwiritsa ntchito kunena Satana.
• N’chifukwa Chiyani pa 1 Mbiri 2:13-15 amanena kuti Davide anali mwana wachisanu ndi chiŵiri wa Jese pamene pa 1 Samueli 16:10, 11 akusonyeza kuti iye anali wachisanu ndi chitatu?
Mfumu Sauli ya Israyeli wakale itasiya kulambira koona, Yehova Mulungu anatumiza mneneri Samueli kuti akadzoze mwana mmodzi wa Jese kukhala mfumu. Nkhani youziridwa ya zimene zinachitikazo, imene Samueli yemweyo analemba m’zaka za m’ma 1000 B.C.E., imasonyeza kuti Davide anali mwana wachisanu ndi chitatu wa Jese. (1 Samueli 16:10-13) Komabe, nkhani imene wansembe Ezara analemba patapita zaka 600 inati: “Jese anabala mwana wake wamwamuna woyamba Eliabu, ndi Abinadabu wachiŵiri, ndi Simeya wachitatu Netaneli wachinayi, Radai wachisanu, Ozemu wachisanu ndi chimodzi, Davide wachisanu ndi chiŵiri.” (1 Mbiri 2:13-15) N’chiyani chinachitikira m’modzi wa abale ake a Davide, ndipo n’chifukwa chiyani Ezara sanatchule dzina lake?
Malemba amanena kuti Jese “anali nawo ana aamuna asanu ndi atatu.” (1 Samueli 17:12) Mwachionekere, mwana wake wina sanakhale ndi moyo mpaka kukwatira n’kukhala ndi ana. Popeza analibe ana, sakanakhala ndi choloŵa cha fuko ndipo sanafunikire kumutchula polemba za mzera wobadwira wa Jese.
Tsopano tiyeni tiganizire za nthaŵi ya Ezara. Ganizirani mmene zinthu zinalili pamene anali kulemba Mbiri. Ukapolo wa ku Babulo unali utatha zaka pafupifupi 77 m’mbuyomo, ndipo Ayuda anakhazikika m’dziko lawo. Mfumu ya Perisiya inapatsa Ezara ulamuliro woika oweruza ndi aphunzitsi a Chilamulo cha Mulungu ndiponso wokongoletsa nyumba ya Yehova. Panafunika ndandanda yolondola ya mizera yobadwira pofuna kutsimikizira choloŵa cha mafuko ndi kuonetsetsa kuti anthu oyenerera okha ndi amene anali kutumikira monga ansembe. Motero, Ezara analemba nkhani yonse ya mbiri ya mtunduwo, kuphatikizapo mbiri yolondola ndiponso yodalirika ya mzera wobadwira wa Yuda ndiponso wa Davide. Dzina la mwana wa Jese amene anamwalira asanabereke mwana linali losafunikira. Motero, Ezara sanatchule dzina lake.