“Ndinapeza Zonse Zimene Ndinkafuna”
MALINGA ndi lipoti la bungwe loona za umoyo wa anthu la World Health Organization, akuti pakalipano kuvutika maganizo kukukhudza anthu oposa 120 miliyoni padziko lonse. Chaka chilichonse, anthu 1 miliyoni amadzipha ndipo anthu kuyambira 10 miliyoni mpaka 20 miliyoni amafuna kudzipha. Kodi ndi chiyani chingathandize anthu ovutika maganizo? Mankhwala akuchipatala angachepetse vutolo, ndipo kuwalimbikitsa n’kofunika. Komanso, ena amene ali ndi vuto limeneli apeza thandizo lina m’mabuku othandiza ofotokoza za Baibulo a Mboni za Yehova, monga momwe kalata yotsatirayi yochokera ku France ikusonyezera.
“Si kale pamene ndinkaona kuti palibe chifukwa chokhalirabe ndi moyo. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti ndife. Ndinali ngati ndafa kale m’katikati. Pofuna thandizo, ndinapemphera kwambiri kwa Yehova. Ndinaganizanso zoŵerenga buku la 2002 Yearbook of Jehovah’s Witnesses ndipo ndinalimaliza m’masiku atatu. Linandilimbikitsa kwambiri ndipo linalimbitsa chikhulupiriro changa.
“Ndinafufuza m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndipo si mmene ndinadabwira! Ndakhala ndikuŵerenga magazini ameneŵa nthaŵi zonse kwa zaka zoposa 15, koma sindinkadziŵa kuti nkhani za m’magaziniwa n’zolimbikitsa ndi zosangalatsa chonchi. Amasonyeza kwambiri chikondi, lomwe ndi khalidwe losoŵa kwambiri masiku ano. Ndinapeza zonse zimene ndinkafuna.”
Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi [“woswanyika,” NW].” (Salmo 34:18) Mosakayikira, onse “a mtima wosweka” kapena “a mzimu woswanyika” angapeze chilimbikitso ndi kuyembekezera zabwino m’tsogolo kuchokera m’Baibulo. Mboni za Yehova zimagaŵira magazini ofotokoza za m’Baibulo kuti athandize anthu ovutika kupindula ndi chilimbikitso chouziridwa ndi Mulungu chimenecho.