Kodi Mbiri ya M’baibulo N’njolondoladi?
M’BUKU lawo lakuti Battles of the Bible, (Nkhondo za m’Baibulo), Chaim Herzog, pulezidenti wakale wadziko la Israyeli, ndi Mordechai Gichon, amene kale anali pulofesa wa maphunziro a zinthu zofukulidwa m’mabwinja pa yunivesite ya Tel Aviv, ananena kuti:
“Mmene anafotokozera mwatsatanetsatane nkhondo za m’Baibulo . . . n’zosatheka kuti anangopeka. Mwachitsanzo, umboni wokwanira timaupeza tikatenga nkhondo ya Gideoni ndi Amidyani ndi othandizira awo, monga momwe aifotokozera pa Oweruza chaputala 6 mpaka 8, ndi kuiyerekezera ndi nkhondo yapakati pa Agiriki ndi anthu a ku Troy, imene Homer anaifotokoza m’ndakatulo yake yotchedwa Iliad. M’ndakatulo imeneyi, gombe lililonse losavuta kufikako ndi tauni iliyonse yapafupi yokhala ndi malinga zikhoza kukhala malo amene kunachitikira nkhondo imeneyi . . . Koma sizili choncho m’nkhani ya m’Baibulo ya nkhondo ya Gideoni. Mu nkhani imeneyi anafotokoza mwatsatanetsatane momwe magulu awiri onsewa ankayendera ndi zomwe anakumana nazo mogwirizana ndi malo amene kumachitikira nkhondoyo ndiponso momwe magulu awiri onsewo amamenyera nkhondoyo. Pomenyana pa nkhondoyi anayenda mtunda wa makilomita 60, ndipo n’zosatheka kufotokoza zinthu zonsezi mwatsatanetsatane moteremu, ndiyeno n’kunena kuti zinali zongopeka . . . Choncho timakakamizika kuvomereza kuti nkhondo ya m’Baibulo imeneyi, yomwe anaifotokoza mwaukatswiri ndi yolondola.”
Mungadziwe madera amene Gideoni anadutsamo mwa kugwiritsa ntchito mapu amene ali pa tsamba 18 ndi 19 mu kabuku ka mapu kakuti ‘Onani Dziko Lokoma.’ a Nkhani yake inayambira pamene “Amidyani onse ndi Aamaleki ndi ana a ku m’mawa anasonkhana pamodzi nawoloka, namanga misasa m’chigwa cha Yezreeli.” Gideoni anapempha mafuko apafupi kuti amuthandize. Nkhondoyi inayambira pa chitsime cha Harodi, kuchoka apo anafika paphiri la More, kenako anafika ku Chigwa cha Yorodano. Gideoni anapitikitsa adani akewo mpaka kuwoloka mtsinje wa Yorodano ndipo anawagonjetsa.—Oweruza 6:33–8:12.
Mapu amenewo, amene ali m’kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ akusonyeza madera akuluakulu otchulidwa mu nkhaniyi ndi zinthu zina zopezeka m’maderawo. Mapu ena (pa tsamba 15) akusonyeza madera a mafuko a Israyeli. Mapu awiri amenewa angakuthandizeni kuona kuti nkhani ya m’Baibuloyi ndi yolondoladi.
Izi zikugwirizana ndi zimene ananena malemu pulofesa Yohanan Aharoni kuti: “M’mayiko otchulidwa m’Baibulo, malo ndi mbiri yake n’zogwirizana kwambiri mwakuti munthu sangamvetse chilichonse cha zimenezi pachokha popanda chinzake.”
[Mawu a M’munsi]
a Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Background map: Based on maps copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel.