Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi Yosefe, mtumiki wokhulupirika wa Yehova, anagwiritsa ntchito chikho chapadera cha siliva powombeza maula, monga mmene lemba la Genesis 44:5 limamvekera?
Palibe chifukwa chilichonse chokhulupirira kuti Yosefe anagwiritsa ntchito njira inayake yowombezera maula.
Baibulo limasonyeza mmene Yosefe ankaonera nkhani yowombeza maula pofuna kudziwa zam’tsogolo. Panthawi ina Yosefe anapemphedwa kuti amasulire maloto a Farao ndipo iye ananena kangapo konse kuti ndi Mulungu yekha amene angathe ‘kuyankha,’ kapena kuti kunena zinthu zam’tsogolo. Motero, Farao weniweniyo anafika pokhulupirira kuti Yosefe anadziwa zam’tsogolo chifukwa chouzidwa ndi Mulungu woona yekha amene Yosefeyo ankalambira, osati mizimu ayi. (Genesis 41:16, 25, 28, 32, 39) Patsogolo pake, mu Chilamulo chimene Mose anapatsidwa, Yehova analetsa kuchita matsenga kapena kuwombeza, motero anatsimikizira kuti Iyeyo ndiye anganeneretu zam’tsogolo.—Deuteronomo 18:10-12.
Motero, n’chifukwa chiyani Yosefe ananena kudzera mwa mtumiki wake kuti anagwiritsa ntchito chikho cha siliva “nawombeza ula nacho”?a (Genesis 44:5) Tiyenera kuganizira nkhani imene inachititsa kuti Yosefe anene mawuwa.
Chifukwa cha njala yaikulu kwambiri, abale ake a Yosefe anapita ku Aigupto kukapeza chakudya. Zaka zingapo m’mbuyo mwake, abale a Yosefewa anamugulitsa kuti akhale kapolo. Tsopano, mosadziwa, iwowa anayamba kupempha thandizo kwa mbale wawoyu, amene panthawiyi anali atakhala woyang’anira chakudya ku Aigupto. Yosefe sanadziulule kwa abale akewo. Koma anaganiza zowayesa kuti adziwe ngati analapa zenizeni. Ankafunanso kudziwa kuti ankakonda motani mng’ono wawo Benjamini ndi bambo awo Yakobo, omwe ankakonda kwambiri Benjamini. Chotero, Yosefe anachita machenjera.—Genesis 41:55—44:3.
Yosefe anasankha mtumiki wake mmodzi kuti adzaze chakudya m’matumba a abale ake aja, abwezere ndalama za aliyense m’thumba lake, ndi kuika chikho cha siliva cha Yosefe m’thumba la Benjamini. Zonse zimene Yosefe anali kuchitazi ankazichita ngati munthu wa udindo woyang’anira zinthu m’dziko lachikunja. Anasintha zochita zake, ndi kalankhulidwe kake kuti abale akewo, azingomuona ngati munthu waudindo umenewo basi chifukwa iwo sanali kuganizako n’komwe zoti iye ndi mbale wawo.
Yosefe atakumana ndi azibale ake, anapitiriza ndi machenjera ake, powafunsa kuti: “Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kuzindikira ndithu [kuwombeza maula, NW]?” (Genesis 44:15) Motero tingathe kuona kuti chikhocho anachigwiritsa ntchito kuyesera abale akewo. Monga tikudziwira, Benjamini sanabedi chikho chija, moterenso Yosefe sikuti anawombezadi maula ndi chikhocho ayi.
[Mawu a M’munsi]
a Pofotokoza kawombezedwe ka panthawiyi, buku lakuti The Holy Bible, With an Explanatory and Critical Commentary, lolembedwa ndi F.C. Cook , linalongosola kuti: “Ankatero mwina poponya m’madzi golide, siliva, kapena mikanda kapenanso zibangili zamtengo wapatali n’kumaziyang’anitsitsa. Njira ina yachidule inali kungoyang’ana m’madzi ngati kuti akuyang’ana pa galasi.” Katswiri wina wa Baibulo Christopher Wordsworth anati: “Nthawi zina ankadzadza madzi m’chikho ndipo ankawombeza poyang’ana chithunzithunzi chopangidwa ndi dzuwa likamanyezimira m’madzi a m’chikhocho.”